Yobu 19:1-29
19 Yobu anayankha kuti:
2 “Kodi mupitiriza kundisowetsa mtendere mpaka liti,+Nʼkumandibaya ndi mawu?+
3 Maulendo 10 onsewa mwakhala mukundidzudzula.*Simukuchita manyazi kuti mukundichitira nkhanza.+
4 Ngati ndalakwitsadi chinachake,Zotsatira zake ndithana nazo ndekha.
5 Ngati mukupitiriza kudzikweza pamaso panga,Nʼkumanena kuti ndikuyenera kukumana ndi mavuto amene ndikukumana nawowa,
6 Dziwani kuti ndi Mulungu amene wandisocheretsa,Ndipo wandikola ndi ukonde wake wosakira nyama.
7 Ine ndakhala ndikulira chifukwa cha mavuto anga, koma palibe amene akundichitira zabwino.+Ndakhala ndikufuula popempha thandizo, koma chilungamo sichikupezeka.+
8 Iye watseka njira yanga ndi khoma lamiyala moti sindingathe kudutsa,Watchinga njira zanga ndi mdima.+
9 Iye wandichotsera ulemerero wanga,Ndipo wandivula chisoti chaulemu kumutu kwanga.
10 Wandigumula mbali zonse mpaka ndatheratu.Chiyembekezo changa wachizula ngati mtengo.
11 Mkwiyo wake wandiyakira,Ndipo akungondiona ngati mdani wake.+
12 Asilikali ake asonkhana pamodzi nʼkundizungulira,Ndipo amanga misasa yawo kuzungulira tenti yanga.
13 Abale anga enieni wawathamangitsira kutali ndi ine,Ndipo anthu amene akundidziwa akundisala.+
14 Anzanga apamtima* anandithawa,Ndipo anthu amene ndinkawadziwa bwino andiiwala.+
15 Alendo amʼnyumba mwanga+ komanso akapolo anga aakazi akundiona ngati munthu wachilendo.Ndine mlendo kwa iwo.
16 Ndaitana wantchito wanga koma sakundiyankha.Ndamuchonderera ndi pakamwa panga kuti andichitire chifundo.
17 Mpweya wanga wakhala wonyansa kwa mkazi wanga,+Ndipo ndakhala wonunkha kwa abale anga enieni.*
18 Ngakhale ana angʼonoangʼono akundinyoza.Ndikaimirira, akumayamba kundinyogodola.
19 Anzanga onse apamtima akudana nane,+Ndipo amene ndinkawakonda anditembenukira.+
20 Ndangotsala mafupa okhaokha,+Ndipo pangʼonongʼono nʼkanafa.*
21 Ndichitireni chifundo anzanganu, ndichitireni chifundo,Chifukwa dzanja la Mulungu landikhudza.+
22 Nʼchifukwa chiyani mukupitiriza kundizunza ngati mmene Mulungu akuchitira?+Nʼchifukwa chiyani mukupitirizabe kundiukira?*+
23 Zikanakhala bwino mawu anga akanalembedwa,Zikanakhala bwino akanalembedwa mʼbuku!
24 Akanalembedwa pathanthwe mochita kugoba kuti akhale mpaka kalekaleAkanalembedwa ndi chitsulo chogobera nʼkuthirapo mtovu.
25 Ine ndikudziwa bwino kuti wondiwombola+ ali moyo,Iye adzabwera nthawi ina ndipo adzaimirira padziko lapansi.*
26 Pambuyo poti khungu langa lawonongedwa chonchi,Ndidakali moyo, ndidzaona Mulungu,
27 Ine ndidzamuona ndekha,Maso angawa adzamuona, osati a munthu wina.+
Koma mkati mwanga ndikumva kupanikizika kwambiri.*
28 Chifukwa inu mukunena kuti, ‘Tikukuzunza mwa njira yanji?’+
Popeza amene ndayambitsa mavutowa ndine.
29 Mukuyenera kuopa lupanga,+Chifukwa mukalakwitsa zinthu, mudzalangidwa ndi lupanga,Mukuyenera kudziwa kuti kuli woweruza.”+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “mwakhala mukundinyoza.”
^ Kapena kuti, “Abale anga.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “kwa ana aamuna a mimba yanga,” kutanthauza kuti mimba imene inandibereka (mimba ya mayi anga).
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ndapulumuka ndi khungu la mano anga.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndipo simukukhutira ndi mnofu wanga.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “adzaimirira pafumbi.”
^ Kapena kuti, “Impso zanga zasiya kugwira ntchito mʼmimba mwanga.”