Yobu 2:1-13
2 Pambuyo pa zimenezi, linafika tsiku limene ana a Mulungu woona*+ anapita kukaonekera pamaso pa Yehova,+ ndipo Satana nayenso anapita kukaonekera pamaso pa Yehova.+
2 Kenako Yehova anafunsa Satana kuti: “Kodi ukuchokera kuti iwe?” Satanayo anayankha Yehova kuti: “Ndimazungulira mʼdziko lapansi komanso kuyendayendamo.”+
3 Ndiyeno Yehova anafunsanso Satana kuti: “Kodi mtima wako uli pa mtumiki wanga Yobu? Padziko lapansi palibe wina wofanana naye. Iye ndi munthu wokhulupirika amene amachita zoyenera,*+ amaopa Mulungu ndiponso amapewa zoipa. Iye akupitirizabe kukhala wokhulupirika+ ngakhale kuti iweyo ukufuna kuti ndimuwononge*+ popanda chifukwa.”
4 Koma Satana anayankha Yehova kuti: “Khungu kusinthanitsa ndi khungu. Munthu angapereke chilichonse chimene ali nacho kuti apulumutse moyo wake.
5 Koma panopa mutambasule dzanja lanu nʼkuwononga thupi lake,* ndipo akutukwanani mʼmaso muli gwa!”+
6 Ndiyeno Yehova anauza Satana kuti: “Chabwino, iye ali mʼmanja mwako. Koma usachotse moyo wake.”
7 Choncho Satana anachoka pamaso pa Yehova nʼkukachititsa kuti Yobu azunzike ndi zilonda zopweteka,+ kuyambira kuphazi mpaka kumutu.
8 Ndiyeno Yobu anatenga phale loti azidzikandira ndipo ankakhala paphulusa.+
9 Patapita nthawi, mkazi wake anamufunsa kuti: “Kodi mukupitirizabe kukhala wokhulupirika? Tukwanani Mulungu mufe!”
10 Koma Yobu anamuyankha kuti: “Ukulankhula ngati mmene amalankhulira akazi opusa. Kodi tizingolandira zabwino zokhazokha kuchokera kwa Mulungu woona osalandiranso zoipa?”+ Ngakhale kuti anakumana ndi zonsezi, Yobu sananene chilichonse cholakwika.*+
11 Anzake atatu a Yobu anamva za masoka onse amene anamugwera ndipo aliyense wa iwo anabwera kuchokera kwawo. Mayina awo anali Elifazi+ wa ku Temani, Bilidadi+ wa ku Shuwa+ ndi Zofari+ wa ku Naama. Iwo anapangana kuti akumane kuti apite akatonthoze Yobu ndi kumulimbikitsa.
12 Atamuona ali chapatali, sanamuzindikire. Kenako anayamba kulira mokweza mawu ndipo anangʼamba zovala zawo nʼkumawaza fumbi mʼmwamba komanso pamutu pawo.+
13 Kenako anakhala pansi limodzi ndi Yobuyo kwa masiku 7 masana ndi usiku. Palibe amene analankhula naye chilichonse chifukwa anaona kuti ululu wake unali waukulu kwambiri.+
Mawu a M'munsi
^ Mawu okuluwika a Chiheberi onena za angelo omwe ndi ana a Mulungu.
^ Kapena kuti, “munthu wopanda cholakwa komanso wamtima wowongoka.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ndimumeze.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “nʼkuwononga fupa ndi mnofu wake.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Yobu sanachimwe ndi milomo yake.”