Yobu 25:1-6

  • Mawu achitatu a Bilidadi (1-6)

    • ‘Kodi munthu angakhale wosalakwa pamaso pa Mulungu?’ (4)

    • Ananena kuti kukhulupirika kwa munthu nʼkopanda phindu (5, 6)

25  Bilidadi+ wa ku Shuwa anayankha kuti:   “Ulamuliro komanso mphamvu zochititsa mantha ndi zake.Iye amakhazikitsa mtendere kumwamba.*   Kodi nʼzotheka kuwerenga asilikali ake? Ndipo ndi ndani amene saona kuwala kwake?   Choncho, kodi munthu angakhale bwanji wolungama pamaso pa Mulungu,+Kapena kodi munthu wobadwa kwa mkazi angakhale bwanji wosalakwa?*+   Ngakhale mwezi si wowala kwa iyeNdipo nyenyezi si zoyera mʼmaso mwake,   Ndiye kuli bwanji munthu yemwe ndi mphutsi,Komanso mwana wa munthu yemwe ndi nyongolotsi?”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmalo ake okwezeka.”
Kapena kuti, “woyera.”