Yobu 27:1-23

  • Yobu anatsimikiza ndi mtima wonse kukhalabe wokhulupirika (1-23)

    • “Sindidzasiya kukhala wokhulupirika” (5)

    • Anthu oipa alibe chiyembekezo (8)

    • “Nʼchifukwa chiyani mukulankhula zopanda nzeru?” (12)

    • Anthu oipa sapindula chilichonse (13-23)

27  Yobu anapitiriza kulankhula* kuti:  2  “Pali Mulungu wamoyo amene wandimana chilungamo,+Ndiponso pali Wamphamvuyonse amene wachititsa moyo wanga kuti ukhale wowawa,+  3  Ngati ndikupitirizabe kupuma,Ndiponso mzimu wochokera kwa Mulungu uli mʼmphuno mwanga,+  4  Milomo yanga sidzalankhula zopanda chilungamo,Ndipo lilime langa silidzalankhula zachinyengo.  5  Inetu sindingayerekeze nʼkomwe kunena kuti amuna inu ndinu olungama. Mpaka ndidzamwalire, sindidzasiya* kukhala wokhulupirika.+  6  Ndipitirizabe kukhala wolungama ndipo sindisiya.+Mtima wanga sudzanditsutsa* nthawi yonse imene ndidzakhale ndi moyo.*  7  Mdani wanga alangidwe mofanana ndi munthu woipa,Ndipo wondiukira alangidwe ngati munthu wosalungama.  8  Kodi munthu woipa* akawonongedwa amakhala ndi chiyembekezo chilichonse,+Mulungu akachotsa moyo wake?  9  Kodi Mulungu adzamva kulira kwakeMavuto akadzamugwera?+ 10  Kapena kodi iye adzasangalala ndi Wamphamvuyonse? Kodi adzapemphera kwa Mulungu nthawi zonse? 11  Ndikuphunzitsani zokhudza mphamvu za Mulungu.*Sindibisa chilichonse chokhudza Wamphamvuyonse. 12  Ngati nonsenu mwaona masomphenya,Nʼchifukwa chiyani mukulankhula zopanda nzeru? 13  Ili ndi gawo la munthu woipa lochokera kwa Mulungu,+Cholowa chimene anthu ozunza anzawo amalandira kuchokera kwa Wamphamvuyonse. 14  Ana ake akachuluka, adzaphedwa ndi lupanga,+Ndipo mbadwa zake sizidzakhala ndi chakudya chokwanira. 15  Mbadwa zake zimene zidzapulumuke zidzaikidwa mʼmanda zitafa ndi mliri,Ndipo akazi awo amasiye sadzawalira. 16  Ngakhale ataunjika siliva ngati fumbi,Nʼkusunga zovala zabwino kwambiri ngati dothi, 17  Ngakhale ataziunjika pamodzi,Munthu wolungama ndi amene adzazivale,+Ndipo anthu osalakwa adzagawana siliva wake. 18  Nyumba imene wamanga ndi yosalimba ngati ya kadziwotche,Ndiponso ngati chisakasa+ chimene mlonda wamanga. 19  Iye adzapita kukagona ali wolemera, koma chuma chake sichidzakhalitsa.Akadzatsegula maso ake, padzakhala palibe chilichonse. 20  Zoopsa zidzamufikira ngati madzi osefukira.Chimphepo chamkuntho chidzamuba usiku.+ 21  Mphepo yakumʼmawa idzamunyamula nʼkumusowetsa,Ndipo idzamuchotsa pamalo pake.+ 22  Idzamuwomba mopanda chisoni+Pamene akuyesera kuthawa mphamvu ya mphepoyo.+ 23  Idzamuwombera mʼmanja monyozaNdipo idzamuimbira mluzu+ ili pamalo ake.”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “kulankhula mwandakatulo.”
Kapena kuti, “ndidzapitirizabe.”
Kapena kuti, “sudzandinyoza.”
Kapena kuti, “masiku onse a moyo wanga.”
Kapena kuti, “wampatuko.”
Mabaibulo ena amati, “Ndikuphunzitsani ndi dzanja la Mulungu.”