Yobu 29:1-25

  • Yobu anakumbukira masiku amene ankasangalala asanayambe kukumana ndi mayesero (1-25)

    • Ankalemekezedwa pageti la mzinda (7-10)

    • Ankachita zinthu zachilungamo (11-17)

    • Aliyense ankamvera malangizo ake (21-23)

29  Yobu anapitiriza kulankhula* kuti:   “Ndikulakalaka ndikanakhala ngati mmene ndinalili mʼmiyezi yapitayi,Masiku amene Mulungu ankandiyangʼanira,   Pamene anachititsa nyale yake kuwala pamutu panga,Pamene ndinkayenda mumdima iye nʼkumandiunikira ndi kuwala kwake.+   Ngati mmene ndinalili ndili mnyamata* komanso ndili ndi mphamvu,Pa nthawi imene Mulungu anali bwenzi langa lapamtima,+   Pamene Wamphamvuyonse anali adakali ndi ine,Nthawi imene ana* anga onse anali moyo,   Pamene ndinkasambitsa mapazi anga mʼmafuta amumkaka,Ndiponso pamene matanthwe ankanditulutsira mitsinje ya mafuta.+   Pa nthawi imene ndinkakonda kupita pageti la mzinda+Nʼkukakhala pabwalo la mzinda,+   Anyamata ankandiona nʼkupatuka,*Ndipo ngakhale achikulire ankaimirira pondipatsa ulemu.+   Akalonga ankakhala chete,Ndipo ankagwira pakamwa pawo. 10  Anthu olemekezeka sankalankhula,Lilime lawo linkamatirira mʼkamwa mwawo. 11  Aliyense amene wamva ndikulankhula, ankanena zabwino za ine,Ndipo amene andiona, ankandichitira umboni. 12  Chifukwa ndinkapulumutsa wosauka amene akupempha thandizo,+Komanso mwana wamasiye ndi aliyense amene analibe womuthandiza.+ 13  Munthu amene watsala pangʼono kufa ankandidalitsa,+Ndipo ndinkasangalatsa mtima wa mkazi wamasiye.+ 14  Ndinkavala chilungamo ngati chovala.Chilungamo changa chinali ngati mkanjo* komanso nduwira. 15  Ndinali ngati maso kwa munthu amene ali ndi vuto losaona,Ndipo ndinali ngati mapazi kwa wolumala. 16  Ndinali bambo kwa osauka,+Ndipo ndinkafufuza mlandu wa anthu amene sindinkawadziwa.+ 17  Ndinkaphwanya nsagwada za wochita zoipa,+Ndipo aliyense amene wagwidwa ndi woipayo, ndinkamulanditsa. 18  Ndinkanena kuti, ‘Ndidzafera mʼnyumba yanga,*+Ndipo masiku anga adzakhala ochuluka ngati mchenga. 19  Mizu yanga idzamwazikana mpaka kukafika mʼmadzi,Ndipo mame adzakhala usiku wonse panthambi zanga. 20  Anthu adzapitiriza kundilemekeza,Ndipo uta umene uli mʼmanja mwanga udzapitiriza kuponya mivi.’ 21  Anthu ankandimvera ndipo ankandidikirira,Ankakhala phee kuyembekezera kuti amve malangizo anga.+ 22  Ndikamaliza kulankhula, iwo sankalankhulanso.Ndipo mawu anga ankawasangalatsa.* 23  Iwo ankandidikirira ngati akudikira mvula,Anali ngati anthu amene akudikirira mwachidwi mvula yomalizira.+ 24  Ndikawamwetulira, iwo sankakhulupirira,Akaona nkhope yanga yosangalala, ankalimbikitsidwa. 25  Ndinkawapatsa malangizo ngati mtsogoleri wawo,Ndinkakhala ngati mfumu imene ili pakati pa asilikali ake,+Ndinali ngati wotonthoza anthu amene akulira.”+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “kulankhula mwandakatulo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmasiku a unyamata wanga.”
Kapena kuti, “antchito.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “nʼkubisala.”
Kapena kuti, “malaya akunja odula manja.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼchisa changa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ankadonthera mʼmakutu mwawo pangʼonopangʼono.”