Yobu 3:1-26

  • Yobu anadandaula kuti anabadwiranji (1-26)

    • Anafunsa chifukwa chake ankazunzika (20, 21)

3  Pambuyo pa zimenezi mʼpamene Yobu anayamba kulankhula ndi kutemberera tsiku limene anabadwa.*+  Yobu anati:   “Zikanakhala bwino tsiku limene ndinabadwa likanapanda kufika,+Ndiponso usiku umene wina ananena kuti: ‘Mwamuna wapangika mʼmimba.’   Tsiku limenelo likhale mdima. Mulungu wakumwamba asaliganizirenso,Ndipo kuwala kusalifikire.   Mdima wandiweyani ulitenge.* Mtambo wa mvula uliphimbe. Zinthu zimene zimadetsa tsiku ziliopseze.   Usiku umenewo utengedwe ndi mdima wandiweyani.+Usasangalale pakati pa masiku apachaka,Pachiwerengero cha miyezi, usalowe nawo.   Ndithu usiku umenewo ukhale wosabereka.Phokoso lachisangalalo lisamveke usiku umenewo.   Otemberera masiku alitemberere tsikulo,Iwo amene angathe kudzutsa ngʼona.+   Nyenyezi zake zamʼmawa kuli kachisisira zizime.Lidikire kuwala koma lisakuone,Ndipo lisaone kuwala kwa mʼbandakucha. 10  Chifukwa silinatseke zitseko za mimba ya mayi anga,+Komanso silinabise mavuto kuti ndisawaone. 11  Nʼchifukwa chiyani sindinafe pobadwa? Nʼchifukwa chiyani sindinamwalire nditatuluka mʼmimba?+ 12  Nʼchifukwa chiyani mawondo a mayi anga anandilandila,Ndipo nʼchifukwa chiyani anandiyamwitsa? 13  Chifukwa pano bwenzi ndikugona popanda wondisokoneza.+Bwenzi ndili mʼtulo komanso ndikupuma+ 14  Limodzi ndi mafumu apadziko lapansi ndi alangizi awo,Amene anadzimangira malo omwe panopa ndi mabwinja. 15  Kapena ndi akalonga amene anali ndi golide,Amene nyumba zawo zinadzaza ndi siliva. 16  Kapena nʼchifukwa chiyani sindinakhale ngati pakati pomwe papita padera popanda mayi kuzindikira,Ngati ana amene sanaonepo kuwala? 17  Ngakhale oipa asiya kuvutika kumandako,Ndipo kumeneko anthu ofooka, akupuma.+ 18  Kumeneko akaidi onse ali pa mtendere.Iwo samvanso mawu a munthu wowakakamiza kugwira ntchito. 19  Anthu onyozeka ndi olemekezeka amakhala chimodzimodzi kumeneko,+Ndipo kapolo amamasuka kwa mbuye wake. 20  Nʼchifukwa chiyani Mulungu amapereka kuwala kwa munthu amene akuvutika,Ndiponso moyo kwa anthu omwe ali pamavuto aakulu?+ 21  Nʼchifukwa chiyani anthu amene amafuna kufa, samafa?+ Iwo amakumba pansi pofunafuna imfa, kuposa mmene amakumbira chuma chobisika. 22  Anthu amenewa amasangalala kwambiri,Amakondwera akapeza manda. 23  Nʼchifukwa chiyani Mulungu amapereka kuwala kwa munthu amene wasochera,Amene Mulungu wamutchingira njira?+ 24  Chifukwa mʼmalo moti ndidye chakudya ndimausa moyo,+Ndipo kubuula kwanga+ kumakhuthuka ngati madzi. 25  Chifukwa chinthu chimene ndimachita nacho mantha chandibwerera,Ndipo chimene ndinali kuchiopa chandichitikira. 26  Ndikusowa mtendere, mavuto achuluka, sindikupeza mpumulo,Koma mavuto akungobwerabe.”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “kutemberera tsiku lake.”
Kapena kuti, “Mdima ndi mthunzi wa imfa zilitenge.”