Yobu 30:1-31

  • Yobu anafotokoza mmene zinthu zinasinthira pa moyo wake (1-31)

    • Anthu opanda pake ankamunyoza (1-15)

    • Ankaona kuti Mulungu sakumuthandiza (20, 21)

    • “Khungu langa lada” (30)

30  “Tsopano anthu amene ndi aangʼono kwa ine,Akundiseka.+Anthu amene abambo awo sindikanalolaKuwaika pamodzi ndi agalu olondera nkhosa zanga.   Kodi mphamvu za manja awo zinali za ntchito yanji kwa ine? Nyonga zawo zatha.   Iwo atoperatu chifukwa cha njala ndiponso kusowa zinthu.Amatafuna dera loumaLimene linali lowonongeka kale komanso labwinja.   Iwo amathyola chitsamba chamchere mʼtchire,Ndipo mizu ya mitengo ndi imene inali chakudya chawo.   Iwo amathamangitsidwa mʼmudzi.+Anthu amawakuwiza ngati akuba.   Iwo amakhala mʼmalo otsetsereka amʼzigwa,*Mʼmaenje amʼnthaka ndi mʼmatanthwe.   Amalira mokuwa ali pazitsambaAmaunjikana pansi pa zitsamba zaminga.   Monga ana a anthu opusa komanso opanda dzina,Iwo athamangitsidwa* mʼdziko.   Koma pano amandinyoza ngakhale akamaimba nyimbo zawo,+Ndakhala chinthu choseketsa* kwa iwo.+ 10  Amanyansidwa nane ndipo safuna kundiyandikira.+Sazengereza kundilavulira kumaso.+ 11  Chifukwa Mulungu wandilanda zida* nʼkundipangitsa kuti ndikhale wopanda mphamvu,Iwo amachita zinthu modzikuza pamaso panga. 12  Iwo aimirira kudzanja langa lamanja ngati gulu la anthu achiwawa kuti andiukire.Amandichititsa kuti ndithawe,Koma amanditchingira njira kuti andiwononge. 13  Iwo awononga njira zangaNʼkupangitsa kuti mavuto anga akule,+Popanda aliyense wowaletsa.* 14  Amabwera ngati akudutsa pampanda umene wagumuka,Iwo amabwera mwamkokomo mʼmalo owonongeka kale. 15  Zoopsa zandipanikiza.Ulemu wanga wachoka ngati kuti wauluzika ndi mphepo,Ndipo chipulumutso changa chachoka ngati mtambo. 16  Tsopano moyo wanga ukuchoka.+Tsiku lililonse ndikuvutika.+ 17  Usiku mafupa anga amapweteka kwambiri,*+Ndipo ululu waukulu sukutha.+ 18  Chovala changa chakokeka mwamphamvu kwambiri.Ndipo chikundilepheretsa kupuma mofanana ndi kolala yothina ya chovala changa. 19  Mulungu wandiponya mʼmatope,Moti ndikungokhala ngati fumbi ndi phulusa. 20  Ndimafuulira kwa inu kuti mundithandize, koma simundiyankha.+Ndimaimirira, koma inu mumangondiyangʼana. 21  Mwandiukira mwankhanza kwambiri.+Ndi mphamvu zonse za dzanja lanu, mwandimenya. 22  Mwandinyamula nʼkundiuluza ndi mphepo.Kenako mwandiponyera uku ndi uku mumphepo yamkuntho. 23  Chifukwa ndikudziwa kuti mudzandipereka ku imfa,Kunyumba imene aliyense wamoyo adzapitako. 24  Koma palibe amene angamenye munthu amene ali pamavuto*+Pamene akupempha thandizo pa nthawi ya tsoka. 25  Kodi sindinalirire anthu amene akukumana ndi mavuto?* Kodi sindinalirire anthu osauka?+ 26  Ngakhale kuti ndinkayembekezera zinthu zabwino, zoipa nʼzimene zinabwera.Ndinkadikirira kuwala, koma kunabwera mdima. 27  Mʼmimba mwanga simunasiye kubwadamuka,Masiku amasautso anandipeza. 28  Ndikuyendayenda ndili wachisoni+ ndipo dzuwa silikuwala. Ndaimirira pakati pa mpingo ndipo ndikulira popempha thandizo. 29  Ndakhala mʼbale wake wa mimbulu,Ndiponso mnzawo wa ana aakazi a nthiwatiwa.+ 30  Khungu langa lada ndipo likusuwa.+Mafupa anga akuwotcha chifukwa cha kutentha.* 31  Zeze wanga akungogwiritsidwa ntchito polira,Ndipo chitoliro changa changokhala choimbira anthu amene akulira.”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “amʼmakhwawa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “akwapulidwa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mwambi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “wakhwefula chingwe cha uta wanga.”
Mabaibulo ena amati, “Popanda aliyense wowathandiza.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mafupa anga amabowoledwa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “angamenye mulu wa zinthu zowonongeka.”
Kapena kuti, “amene zinthu sizikuwayendera bwino.”
Mabaibulo ena amati, “chifukwa cha kuphwanya kwa thupi.”