Yobu 33:1-33

  • Elihu anadzudzula Yobu chifukwa chodzilungamitsa (1-33)

    • Dipo linapezeka (24)

    • Adzakhala ndi mphamvu ngati mmene analili ali mnyamata (25)

33  “Koma tsopano inu a Yobu, imvani mawu anga,Ndipo mvetserani zonse zimene ndikufuna kunena.   Inetu nditsegula pakamwa panga,Lilime langa likuyenera* kulankhula.   Zonena zanga zikusonyeza kuwongoka kwa mtima wanga,+Ndipo milomo yanga imanena moona mtima zimene ndikudziwa.   Mzimu wa Mulungu unandiumba,+Ndipo mpweya wa Wamphamvuyonse unandipatsa moyo.+   Ngati mungathe ndiyankheni.Konzekerani kuti mundifotokozere mfundo zanu.   Inetu nʼchimodzimodzi ndi inu pamaso pa Mulungu woona.Inenso ndinaumbidwa ndi dongo.+   Choncho musachite nane mantha,Ndipo musapanikizike ndi zimene ndikuuzeni.   Koma ndakumvani mukunena kuti,Inde, ndakhala ndikumva mawu anu akuti,   ‘Ndine woyera, wopanda tchimo,+Ndine wosadetsedwa, ndilibe cholakwa.+ 10  Koma Mulungu amapeza zifukwa zonditsutsira,Amandiona ngati mdani wake.+ 11  Amaika mapazi anga mʼmatangadza,Amayangʼanitsitsa njira zanga zonse.’+ 12  Koma munalakwitsa ponena zimenezi, choncho ndikuyankhani kuti: Mulungu ndi wamkulu kwambiri kuposa munthu.+ 13  Nʼchifukwa chiyani mukumudandaula?+ Kodi nʼchifukwa chakuti sanakuyankheni mawu anu onse?+ 14  Paja Mulungu amalankhula koyamba ndi kachiwiri,Koma palibe amene amamvetsera. 15  Iye amalankhula mʼmaloto ndi mʼmasomphenya a usiku,+Anthu akakhala mʼtulo tofa nato,Akamagona pamabedi awo. 16  Pa nthawi imeneyi mʼpamene amatsegula anthu makutu,+Ndipo amadinda* malangizo ake mʼmaganizo mwawo, 17  Pofuna kubweza munthu kuti asachite zoipa+Komanso kumuteteza kuti asakhale wonyada.+ 18  Mulungu amateteza moyo wake kuti usapite kudzenje,*+Amateteza munthu kuti asawonongedwe ndi lupanga.* 19  Munthu amadzudzulidwanso ndi ululu ali pabedi pake,Ndiponso pamene mafupa ake akumupweteka nthawi zonse, 20  Moti amaipidwa* ndi chakudya,Ndipo iye amakana* ngakhale chakudya chabwino.+ 21  Mnofu wake umatha, osaonekanso,Ndipo mafupa ake amene samaoneka, amakhala pamtunda.* 22  Moyo wake umayandikira kudzenje.*Umayandikira amene amabweretsa imfa. 23  Ngati iye ali ndi mthenga,*Womulankhulira mmodzi pa omulankhulira 1,000,Kuti auze munthu zimene zili zoyenera, 24  Zikatero Mulungu amamukomera mtima nʼkunena kuti,‘Mupulumutseni kuti asapite mʼdzenje,*+ Chifukwa ndapeza dipo.*+ 25  Mnofu wake usalale* kuposa mmene unalili ali mnyamata.+Abwerere ku masiku ake aunyamata pamene anali ndi mphamvu.’+ 26  Adzapemphera kwa Mulungu+ ndipo iye adzamukomera mtima,Adzaona nkhope yake akufuula mosangalala,Ndipo Mulungu adzayambanso kuona munthuyo kuti ndi wolungama. 27  Munthu ameneyo adzauza* anthu kuti,‘Ndachimwa+ komanso kukhotetsa zimene zinali zolungama,Koma sindinalandire zimene ndimayenera kulandira.* 28  Iye wandiwombola* kuti ndisapite kudzenje,*+Ndipo moyo wanga udzaona kuwala.’ 29  Zoonadi, Mulungu amachitira munthu zinthu zonseziAmamuchitira kawiri kapena katatu, 30  Kuti amupulumutse* kudzenje,*Nʼcholinga choti asangalale ndi moyo.+ 31  Tcherani khutu inu a Yobu. Ndimvetsereni! Khalani chete, ndipo ine ndipitiriza kulankhula. 32  Ngati muli ndi mawu, ndiyankheni. Lankhulani chifukwa ndikufuna nditsimikizire kuti ndinu wosalakwa. 33  Ngati mulibe mawu alionse, mvetserani mawu anga.Khalani chete, ndipo ine ndikuphunzitsani kuti mukhale wanzeru.”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Lilime langa ndi mʼkamwa mwanga zikuyenera.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amaika chidindo pa.”
Kapena kuti, “kumanda.”
Kapena kuti, “ndi chida.”
Kapena kuti, “moyo wake umakana.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “moyo wake umaipidwa.”
Kapena kuti, “amaonekera.”
Kapena kuti, “kumanda.”
Kapena kuti, “mngelo.”
Kapena kuti, “kumanda.”
Kapena kuti, “ukhale wathanzi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “adzaimbira.”
Mabaibulo ena amati, “Koma sindinapindule chilichonse.”
Kapena kuti, “Iye wawombola moyo wanga.”
Kapena kuti, “kumanda.”
Kapena kuti, “Kuti achotse moyo wake.”
Kapena kuti, “kumanda.”