Yobu 36:1-33
-
Elihu anatamanda Mulungu chifukwa cha mphamvu zake zopanda malire (1-33)
36 Elihu anapitiriza kunena kuti:
2 “Ndilezereni mtima kwa kanthawi kochepa kuti ndifotokoze,Chifukwa ndidakali ndi mawu oti ndinene mʼmalo mwa Mulungu.
3 Ndifotokoza mwatsatanetsatane zimene ndikudziwa,Ndipo ndinena kuti amene anandipanga, ndi wachilungamo.+
4 Ndikunena zoona, mawu anga si onama.Amene amadziwa chilichonse+ akukuonani.
5 Inde, Mulungu ndi wamphamvu+ ndipo sakana munthu aliyense.Iye ali ndi mphamvu zazikulu zomvetsa zinthu.*
6 Iye sadzateteza moyo wa anthu oipa,+Koma amachitira chilungamo anthu amene ali pamavuto.+
7 Iye sasiya kuyangʼanitsitsa wolungama.+Amawaika kukhala mafumu,+ ndipo amalemekezeka mpaka kalekale.
8 Koma akamangidwa mʼmatangadza,Nʼkugwidwa ndi zingwe zamavuto,
9 Iye amawaululira zimene achita,Zimene alakwitsa chifukwa cha kunyada kwawo.
10 Iye amatsegula makutu awo kuti awapatse malangizoNdi kuwauza kuti asiye kuchita zoipa.+
11 Akamamumvera komanso kumutumikira,Zinthu zidzawayendera bwino pa nthawi yonse ya moyo wawo,Ndipo moyo wawo udzakhala wosangalatsa.+
12 Koma akapanda kumvera, adzaphedwa ndi lupanga*+Ndipo adzafa ali osadziwa zinthu.
13 Anthu oipa mtima* adzasunga chakukhosi.
Iwo sapempha thandizo ngakhale Mulungu atawamanga.
14 Iwo amafa adakali ana,+Amakhala pakati pa mahule aamuna apakachisi moyo wawo wonse.+
15 Koma Mulungu amapulumutsa anthu ovutika pa mavuto awo,Amatsegula makutu awo akamaponderezedwa.
16 Iye amakukokani mukatsala pangʼono kukumana ndi mavuto+Nʼkukupititsani pamalo otakasuka, opanda mavuto.+Patebulo panu pali chakudya chambiri chabwino chimene chimakusangalatsani.+
17 Kenako mudzakhutira ndi chiweruzo chimene chidzaperekedwe kwa oipa.+Pa nthawi imene chiweruzo chidzaperekedwe komanso chilungamo chidzatsatiridwe.
18 Samalani kuti mkwiyo usakuchititseni zinthu mwanjiru,*+Ndipo musalole kuti akupatseni ziphuphu zambiri nʼkukusocheretsani.
19 Kodi kulira kwanu kopempha thandizoKapena kuyesetsa kwanu mwamphamvu kungakuthandizeni kuti musakumane ndi mavuto?+
20 Musamalakelake kuti usiku ufike,Pamene anthu amasowa pamalo awo.
21 Samalani kuti musayambe kuchita zinthu zoipa,Musasankhe zimenezi mʼmalo mwa mavuto.+
22 Pajatu Mulungu ali ndi mphamvu zapamwamba.Kodi pali mphunzitsi winanso wofanana naye?
23 Ndi ndani anauzapo Mulungu kuti chitani izi,+Kapena ndi ndani amene anamuuza kuti, ‘Zimene mwachitazi ndi zolakwikaʼ?+
24 Kumbukirani kulemekeza ntchito zake,+Zimene anthu amazitchula munyimbo zawo.+
25 Anthu onse aziona,Munthu amaziyangʼana ali patali.
26 Inde Mulungu ndi wamkulu kuposa mmene tikudziwira.+Palibe amene angawerenge* zaka zimene wakhala ndi moyo.+
27 Iye amakoka madontho a madzi.+Madonthowo amasintha nʼkukhala nkhungu imene imapanga mvula,
28 Kenako mitambo imagwetsa mvula,+Imagwetsera aliyense madzi.
29 Kodi alipo amene angamvetse mmene mitambo anaitambasulira,Komanso kugunda kochokera mutenti yake?*+
30 Onani mmene amaiwalitsira ndi mphenzi zake*+Ndipo amaphimba pansi pa nyanja* ndi madzi.
31 Pogwiritsa ntchito zimenezi, iye amapereka chakudya kwa anthu onse.Amawapatsa chakudya chochuluka.+
32 Iye amafumbata mphezi mʼmanja mwake,Ndipo amailamula kuti ikagwere pamene akufuna.+
33 Mabingu ake amanena za iye,Ngakhale ziweto zimadziwa amene akubwera.”
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Mphamvu za mtima wake nʼzazikulu.”
^ Kapena kuti, “ndi chida.”
^ Kapena kuti, “ampatuko.”
^ Kapena kuti, “kuwomba mʼmanja mwanjiru.”
^ Kapena kuti, “Nʼzosatheka kufufuza.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mumsasa wake.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “kuwala kwake.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mizu ya nyanja.”