Yobu 39:1-30

  • Nyama zimene Mulungu analenga zimasonyeza kuti pali zambiri zimene anthu sakudziwa (1-30)

    • Mbuzi zamʼmapiri komanso mphoyo (1-4)

    • Bulu wamʼtchire (5-8)

    • Ngʼombe yamphongo yamʼtchire (9-12)

    • Nthiwatiwa (13-18)

    • Hatchi (19-25)

    • Kabawi komanso chiwombankhanga (26-30)

39  “Kodi ukudziwa nthawi imene mbuzi zamʼmapiri zimabereka?+ Kodi unayamba waona mphoyo zikubereka?+   Kodi umawerenga miyezi imene imadutsa zili ndi bere? Kodi ukudziwa nthawi imene zimabereka?   Zimagwada zikamaswa ana awo,Ndipo ululu wawo wapobereka umatha.   Ana awo amakhala amphamvu ndipo amakulira mʼtchire.Amachoka osabwereranso kwa makolo awo.   Ndi ndani anapatsa bulu wamʼtchire ufulu womangodziyendera,+Ndipo ndi ndani amene anamasula zingwe za bulu wamʼtchire?   Ndinamupatsa chipululu kuti ikhale nyumba yake,Ndiponso dera la nthaka yamchere kuti akhale malo ake okhala.   Amapewa phokoso lamumzinda,Ndipo samva mawu a munthu amene amalamula nyama kuti zigwire ntchito.   Amayendayenda mʼmapiri pofunafuna msipu,Ndipo amafunafuna chomera chilichonse chobiriwira.   Kodi ngʼombe yamphongo yamʼtchire imafunitsitsa kukutumikira?+ Kodi ingagone usiku wonse mʼkhola lako?* 10  Kodi ungamange ngʼombe yamʼtchire ndi zingwe kuti ikulimire mizere,Kapena kodi ingalole kuti upite nayo kuchigwa kukalima? 11  Kodi ungaikhulupirire chifukwa ili ndi mphamvu zochuluka,Nʼkuisiya kuti ikugwirire ntchito yako yotopetsa? 12  Kodi ungaidalire kuti ikubweretsere zokolola zako?Ndipo kodi ingatenge zokololazo nʼkupita nazo pamalo opunthira? 13  Nthiwatiwa imakupiza mapiko ake mosangalala,Koma kodi mapiko ndi nthenga zake nʼzofanana ndi za dokowe?+ 14  Imasiya mazira ake munthaka,Ndipo imawatenthetsa mumchenga. 15  Imaiwala kuti phazi linalake likhoza kuwaphwanya,Kapenanso kuti nyama yakutchire ikhoza kuwaponda. 16  Imachitira nkhanza ana ake ngati kuti si ake,+Ndipo siopa kuti ntchito imene yagwira powasamalira ingakhale yopanda phindu. 17  Chifukwa Mulungu sanaipatse* nzeruNdipo sanaipange kuti izichita zinthu mozindikira. 18  Koma ikaimirira nʼkutambasula mapiko ake kuti ithawe,Imaseka hatchi ndi wokwerapo wake. 19  Kodi ndi iwe amene umapereka mphamvu kwa hatchi?+ Kodi ndi iwe amene umaveka khosi lake manyenje awirawira? 20  Kodi ungaichititse kuti idumphe ngati dzombe? Phokoso lamphamvu limene imatulutsa mʼmphuno mwake ndi lochititsa mantha.+ 21  Imachita mgugu mʼchigwa, ndipo imasangalala ndi mphamvu zake.+Imapita kumene kukuchitika nkhondo.*+ 22  Imanyoza mantha ndipo siopa chilichonse.+ Sibwerera mʼmbuyo chifukwa choopa lupanga. 23  Kachikwama koika mivi kamachita phokoso kakamagunda mʼnthiti mwake,Mkondo ndi nthungo yake zimanyezimira. 24  Imathamangira kutsogolo* ikunjenjemera chifukwa chosangalala.Ndipo singaime chifukwa choti yamva phokoso la lipenga. 25  Lipenga likangolira imati, ‘Eyaa!’ Imanunkhiza nkhondo ili kutali,Ndipo imamva kufuula kwa atsogoleri a asilikali komanso phokoso la nkhondo.+ 26  Kodi nzeru zako ndi zimene zimachititsa kuti kabawi auluke,Komanso atambasulire mapiko ake kumʼmwera? 27  Kapena kodi chiwombankhanga chimauluka mʼmwamba chifukwa choti iweyo wachilamula,+Nʼkukamanga chisa chake pamwamba kwambiri?+ 28  Chimagona kuphedi usiku wonse,Ndipo chimakhala mʼmalo ake otetezeka kuphanga lapathanthwe.* 29  Chili pamalo omwewo, chimafunafuna chakudya,+Maso ake amaona kutali kwambiri. 30  Ana ake amamwa magazi.Ndipo kumene kuli zakufa, ichonso chimakhala komweko.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “modyeramo ziweto.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amaichititsa kuti iiwale.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Imapita kukakumana ndi zida zankhondo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Imameza nthaka.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “padzino la thanthwe.”