Yobu 4:1-21

  • Mawu oyamba a Elifazi (1-21)

    • Ananyoza kukhulupirika kwa Yobu (7, 8)

    • Anafotokoza uthenga wochokera kwa mzimu (12-17)

    • ‘Mulungu sakhulupirira atumiki ake’ (18)

4  Kenako Elifazi+ wa ku Temani anayankha kuti:  2  “Munthu atayesa kukulankhula, kodi sukhumudwa? Chifukwa ndi ndani angathe kudziletsa kuti asalankhule?  3  Nʼzoona kuti walangiza anthu ambiri,Ndipo unkalimbitsa anthu ofooka.  4  Mawu ako ankadzutsa munthu aliyense amene wagwa,Ndipo unkalimbitsa anthu amene mawondo awo anali olobodoka.  5  Koma panopa zakuchitikira iweyo, ndipo watopa nazo,Zakhudza iweyo, ndipo wafooka nazo.  6  Popeza umaopa Mulungu, kodi sukuyenera kulimba mtima? Popeza ndiwe wokhulupirika,+ kodi ulibe chiyembekezo?  7  Takumbukira: Kodi pali munthu wosalakwa amene anawonongedwapo? Ndi liti pamene anthu ochita zoyenera anawonongedwapo?  8  Zimene ine ndaona nʼzakuti, anthu amene amalima* munda wa zoipa,Ndiponso amene amafesa mavuto, amakolola zomwezo.  9  Iwo amawonongeka ndi mpweya wa Mulungu,Ndipo mkwiyo wake ukayaka amatha. 10  Mkango umabangula, ndipo mkango wamphamvu umamveka kulira,Komabe ngakhale mano a mikango yamphamvu,* amathyoka. 11  Mkango umafa chifukwa chosowa nyama yoti udye,Ndipo ana a mkango amamwazikana. 12  Tsopano winawake anandibweretsera mawu mwachinsinsi,Ndipo khutu langa linamva kunongʼona kwa mawuwo. 13  Maganizo osautsa atandifikira mʼmasomphenya usiku,Pa nthawi imene anthu amakhala ali mʼtulo tofa nato, 14  Ndinanjenjemera kwambiri,Ndipo mafupa anga onse anagwidwa ndi mantha. 15  Mzimu unadutsa kumaso kwanga,Ndipo ubweya wa pathupi langa unaimirira. 16  Kenako mzimuwo unaima,Koma sindinazindikire maonekedwe ake. Chinthu chinaima pamaso panga.Kunali bata, kenako ndinamva mawu akuti: 17  ‘Kodi munthu angakhale wolungama kuposa Mulungu? Kodi munthu angakhale woyera kuposa amene anamupanga?’ 18  Iyetu sakhulupirira atumiki ake,Ndipo angelo* ake amawapezera zifukwa. 19  Nanga kuli bwanji anthu amene amakhala mʼnyumba zadothi,Amene maziko awo ali mʼfumbi?+Amene amathudzulidwa mosavuta ngati kadziwotche. 20  Amakhala ndi moyo mʼmawa koma pofika madzulo amakhala ataphwanyika.Amawonongeka kwamuyaya, ndipo palibe amene amazindikira. 21  Iwo ali ngati tenti imene chingwe chake chasololedwa. Iwo amafa alibe nzeru.”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “amene amakonza.”
Kapena kuti, “mikango yamphamvu yamanyenje.”
Kapena kuti, “amithenga.”