Yobu 41:1-34

  • Mulungu anafotokoza kudabwitsa kwa ngʼona (1-34)

41  “Kodi ungawedze ngʼona*+ ndi mbedzaKapena kumanga lilime lake ndi chingwe?   Kodi ungadutsitse chingwe* mʼmphuno mwakeKapena kubowola nsagwada zake ndi ngowe?*   Kodi iyo ingakuchonderere kambirimbiri,Kapena kodi ingalankhule nawe mofatsa?   Kodi ingachite nawe pangano,Kuti ikhale kapolo wako moyo wake wonse?   Kodi ungasewere nayo ngati mbalame,Kapena kodi ungaimange pachingwe kuti izisangalatsa ana ako aakazi?   Kodi ochita malonda angaigulitse posinthanitsa ndi chinthu china? Kodi angaiduledule nʼkuigawa kwa amalonda?   Kodi ungabowole chikopa chake ndi ntcheto,*+Kapena mutu wake ndi mikondo yophera nsomba?   Igwire ndi dzanja lako,Sudzaiwala ikadzakuukira ndipo sudzabwerezanso.   Kuyembekezera kuti ungaigonjetse nʼkungotaya nthawi. Kungoiona kokha umachita mantha.* 10  Palibe angalimbe mtima kuti aipute. Ndiye ndi ndani amene angaimitsane ndi ine?+ 11  Ndi ndani anandipatsapo chinthu chilichonse kuti ndimubwezere?+ Chilichonse chimene chili pansi pa thambo ndi changa.+ 12  Sindikhala chete osanena za miyendo yake,Zokhudza mphamvu zake ndi thupi lake loumbidwa bwino. 13  Ndi ndani anachotsa chikopa chake cholimba? Ndi ndani angalowe pakati pa nsagwada zake itayasamula? 14  Ndi ndani angatsegule zitseko zapakamwa pake?* Mano ake onse ndi ochititsa mantha. 15  Pamsana pake pali mizere ya mambaAmene ndi othithikana kwambiri. 16  Ndi othithikana kwambiri,Moti ngakhale mpweya sungadutse pakati pawo. 17  Ndi omatirirana,Anaphatikana ndipo sizingatheke kuwalekanitsa. 18  Ikayetsemula pamaoneka kuwala,Ndipo maso ake ali ngati kuwala kwa mʼbandakucha. 19  Mʼkamwa mwake mumatuluka kungʼanima kwa mphezi,Komanso mumathetheka moto. 20  Mʼmphuno mwake mumatuluka utsi,Ngati ngʼanjo imene yayatsidwa ndi udzu. 21  Mpweya wake umayatsa makala,Ndipo mʼkamwa mwake mumatuluka lawi la moto. 22  Mʼkhosi mwake muli mphamvu zochuluka,Ndipo onse amene akumana nayo amachita mantha kwambiri. 23  Minofu yake ndi yokwinyikakwinyika komanso yothithikana.Ndi yolimba ngati kuti anaiumbira pomwepo ndipo sisuntha. 24  Mtima wake ndi wolimba ngati mwala.Inde ndi wolimba ngati mwala wa mphero. 25  Ikadzuka, ngakhale anthu amphamvu amachita mantha.Ikamagwedeza mchira wake imachititsa mantha. 26  Palibe amene angaigonjetse ndi lupanga,Ngakhalenso mkondo, mpaliro, kapena muvi.+ 27  Chitsulo imangochiona ngati udzu,Ndipo kopa imangomuona* ngati mtengo wowola. 28  Muvi suipangitsa kuti ithawe.Miyala yoponya ndi gulaye* imasanduka mapesi kwa iyo. 29  Chibonga imangochiona ngati phesi,Ndipo imaseka ikamva phokoso la nthungo. 30  Kumimba kwake kuli ngati timapale tosongoka.Ikagona mʼmatope imakhala ngati chopunthira mbewu.+ 31  Imachititsa madzi akuya kuwira ngati ali mumphika.Imatakasa nyanja ngati mphika wa mafuta onunkhira. 32  Ikamasambira imasiya madzi a thovu mʼmbuyo mwake. Moti munthu angaganize kuti madzi achita imvi. 33  Padziko lapansi palibe chofanana nayo.Mulungu anaipanga kuti isamachite mantha. 34  Imayangʼana mopanda mantha nyama iliyonse yodzikweza. Iyo ndi mfumu ya zilombo zonse zakutchire, zomwe ndi zamphamvu.”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Leviyatani.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mlulu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “minga.”
Umenewu ndi mpaliro umene mwina unali ndi mano oyangʼana kumbuyo ngati dzino la mbedza.
Kapena kuti, “umangodzigwera.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “zakumaso kwake.”
Kapena kuti, “mkuwa imangowuona.”
Gulaye ndi chipangizo choponyera miyala chimene amachita kupukusa ndi dzanja.