Yobu 8:1-22

  • Mawu oyamba a Bilidadi (1-22)

    • Ananena kuti ana a Yobu anachimwa (4)

    • ‘Ngati ukanakhaladi woyera, Mulungu akanakuteteza’ (6)

    • Ananena kuti Yobu ndi woipa (13)

8  Bilidadi+ wa ku Shuwa+ anayankha kuti:   “Kodi ukhala ukulankhula chonchi mpaka liti?+ Mawu a mʼkamwa mwako ali ngati mphepo yamphamvu.   Kodi Mulungu angapotoze chilungamo?Kapena kodi Wamphamvuyonse angapotoze zinthu zimene ndi zolungama?   Ngati ana ako anamuchimwira,Iye anawalanga chifukwa cha kupanduka kwawo,*   Koma ngati iweyo utayangʼana kwa Mulungu,+Nʼkuchonderera Wamphamvuyonse kuti akuchitire chifundo,   Ndipo ngati ukanakhaladi woyera komanso ngati umachitadi zoyenera,+Iye akanakumvera*Ndipo akanakubwezeretsa mmene unalili poyamba.   Ndipo ngakhale kuti chiyambi chako chinali chachingʼono,Tsogolo lako likanakhala lalikulu.+   Tafunsa mʼbadwo wakale,Ndipo ganizira zinthu zimene makolo awo anapeza.+   Chifukwa ife tabadwa dzulodzuloli, ndipo sitikudziwa kalikonse,Chifukwa masiku athu padziko lapansi ali ngati mthunzi. 10  Kodi iwo sadzakulangizaNdipo sadzakuuza zimene akudziwa?* 11  Kodi gumbwa* angamere pamalo pamene si padambo? Ndipo kodi bango lingakule popanda madzi? 12  Lidakali ndi maluwa, lisanadulidwe nʼkomwe,Lidzauma zomera zonse zisanaume. 13  Zimenezi ndi zimene zidzachitikire* anthu onse amene aiwala Mulungu,Chifukwa chiyembekezo cha anthu oipa* chidzatha. 14  Amene amadalira zinthu zosathandiza,Amene amadalira zinthu zosalimba ngati ulusi wa kangaude.* 15  Iye adzatsamira nyumba yake, koma idzagwa.Adzayesetsa kuigwira, koma sidzalimba. 16  Iye ali ngati chomera chothiriridwa chimene chili padzuwa.Ndipo nthambi zake zimakula mʼmunda.+ 17  Mizu yake imapiringizana pamulu wa miyala.Iye amaona kuti miyalayo ndi nyumba yake. 18  Koma akazulidwa* pamalo akewo,Malowo adzamukana nʼkunena kuti, ‘Ine sindinayambe ndakuonapo.’+ 19  Umu ndi mmene adzathere,*+Kenako zomera zina zidzamera kuchokera mufumbi. 20  Ndithudi, Mulungu sadzakana anthu okhulupirika,*Kapena kuthandiza* anthu ochita zoipa. 21  Chifukwa adzakupangitsa kuti useke,Ndipo udzafuulanso chifukwa chosangalala. 22  Anthu odana nawe adzachita manyazi,Ndipo tenti ya anthu oipa kudzakhala kulibe.”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Iye anawapereka mʼmanja mwa kupanduka kwawo.”
Kapena kuti, “Iye akanadzuka kuti akumvere.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “sadzatulutsa mawu kuchokera mʼmitima yawo?”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mmenemu ndi mmene zilili njira za.”
Kapena kuti, “ampatuko.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “nyumba ya kangaude.”
Kapena kuti, “akamezedwa.”
Kapena kuti, “Umu ndi mmene njira yake idzathere.”
Kapena kuti, “anthu opanda cholakwa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kugwira dzanja la.”