Wolembedwa ndi Yohane 1:1-51

  • Mawu anakhala munthu (1-18)

  • Umboni umene Yohane Mʼbatizi anapereka (19-28)

  • Yesu ndi Mwanawankhosa wa Mulungu (29-34)

  • Ophunzira oyambirira a Yesu (35-42)

  • Filipo komanso Natanayeli (43-51)

1  Pachiyambi, panali wina amene ankadziwika kuti Mawu,+ ndipo Mawuyo anali ndi Mulungu+ komanso Mawuyo anali mulungu.*+  Ameneyu anali ndi Mulungu kuyambira pachiyambi.  Zinthu zonse zinakhalako kudzera mwa iye+ ndipo palibe chinthu ngakhale chimodzi chimene chinakhalapo popanda iyeyo.  Moyo unakhalapo kudzera mwa iye ndipo moyowo unali kuwala kounikira anthu.+  Kuwalako kukuunika mumdima+ koma mdimawo sunagonjetse kuwalako.  Kunabwera munthu wina amene anatumidwa monga nthumwi ya Mulungu. Dzina lake anali Yohane.+  Munthu ameneyu anabwera ngati mboni, kuti adzachitire umboni za kuwala+ nʼcholinga chakuti anthu osiyanasiyana akhulupirire kudzera mwa iye.  Sikuti iyeyu anali kuwalako,+ koma anangobwera kudzachitira umboni za kuwalako.  Kuwala kwenikweni kumene kumaunikira anthu osiyanasiyana kunali kutatsala pangʼono kubwera mʼdziko.+ 10  Iye anali mʼdziko+ ndipo dziko linakhalapo kudzera mwa iye,+ koma dzikolo silinamudziwe. 11  Anabwera kudziko lakwawo, koma anthu akwawo enieniwo sanamulandire. 12  Komabe onse amene anamulandira, anawapatsa mphamvu kuti akhale ana a Mulungu,+ chifukwa choti ankakhulupirira dzina lake.+ 13  Iwowa sanabadwe kuchokera mwa anthu kapena chifukwa cha kufuna kwa anthu kapenanso chifukwa cha kufuna kwa munthu, koma anabadwa kuchokera kwa Mulungu.+ 14  Choncho Mawu ameneyo anakhala ndi thupi la nyama+ ndipo ankakhala pakati pathu. Ife tinaona ulemerero wake, ulemerero wofanana ndi umene mwana wobadwa yekha+ amalandira kuchokera kwa bambo ake. Mulungu ankamukomera mtima kwambiri* komanso ankaphunzitsa choonadi. 15  (Yohane ankachitira umboni za iye, moti ankachita kufuula kuti: “Uyu ndi amene ndinkanena uja kuti, ‘Amene akubwera mʼmbuyo mwangamu ndi wamkulu kuposa ine, chifukwa anakhalapo ine ndisanabadwe.’”)+ 16  Chifukwa chakuti anali ndi kukoma mtima kwakukulu, nthawi zonse tinkalandira kukoma mtima kwakukulu kosefukira. 17  Popeza Chilamulo chinaperekedwa kudzera mwa Mose,+ kukoma mtima kwakukulu+ komanso choonadi zinakhalako kudzera mwa Yesu Khristu.+ 18  Palibe munthu amene anaonapo Mulungu ndi kale lonse,+ mulungu wobadwa yekha+ amene ali pambali pa Atate*+ ndi amene anafotokoza za Mulungu.+ 19  Yohane anapereka umboni pamene Ayuda anatumiza ansembe ndi Alevi kuchokera ku Yerusalemu kukamufunsa kuti: “Kodi ndiwe ndani?”+ 20  Iye anavomera ndipo sanakane. Ananena kuti: “Ine si Khristu.” 21  Iwo anamufunsa kuti: “Nanga ndiwe ndani? Ndiwe Eliya kapena?”+ Iye anayankha kuti: “Ayi.” “Kapena ndiwe Mneneri?”+ Iye anayankha kuti: “Ayi!” 22  Choncho iwo anamufunsa kuti: “Nanga ndiwe ndani? Tiuze kuti tikathe kupereka yankho kwa amene atituma. Mwiniwakewe umati ndiwe ndani?” 23  Iye anati: “Ndine mawu a winawake amene akufuula mʼchipululu kuti, ‘Wongolani njira ya Yehova,’*+ monga mmene mneneri Yesaya ananenera.”+ 24  Anthuwo anatumidwa ndi Afarisi. 25  Choncho anamufunsa kuti: “Nanga nʼchifukwa chiyani umabatiza anthu ngati iweyo si iwe Khristu, Eliya kapena Mneneri?” 26  Yohane anawayankha kuti: “Ine ndimabatiza mʼmadzi. Pakati panu paimirira wina amene inu simukumudziwa. 27  Iye ndi amene akubwera mʼmbuyo mwangamu ndipo ine si woyenera kumasula zingwe za nsapato zake.”+ 28  Zinthu zimenezi zinachitikira ku Betaniya, kutsidya la Yorodano, kumene Yohane ankabatiza anthu.+ 29  Tsiku lotsatira anaona Yesu akubwera kwa iye, ndipo anati: “Taonani, Mwanawankhosa+ wa Mulungu amene akuchotsa uchimo+ wa dziko!+ 30  Uyu ndi amene ndinkanena uja kuti: ‘Amene akubwera mʼmbuyo mwangamu ndi wamkulu kuposa ine,* chifukwa anakhalapo ine ndisanabadwe.’+ 31  Inenso sindinkamudziwa, koma chifukwa chimene ndikubatizira anthu mʼmadzi nʼchakuti iyeyu aonekere kwa Isiraeli.”+ 32  Yohane anachitiranso umboni kuti: “Ndinaona mzimu ukutsika ngati nkhunda kuchokera kumwamba ndipo unakhalabe pa iye.+ 33  Inenso sindinkamudziwa, koma Mulungu amene anandituma kudzabatiza mʼmadzi anandiuza kuti: ‘Ukadzaona mzimu ukutsika nʼkukhazikika pamunthu wina,+ ameneyo ndi amene amabatiza ndi mzimu woyera.’+ 34  Ine ndinaonadi zimenezo ndipo ndachitira umboni kuti iyeyu ndi Mwana wa Mulungu.”+ 35  Tsiku lotsatira Yohane analinso ataima ndi ophunzira ake awiri, 36  ndipo ataona Yesu akuyenda, ananena kuti: “Onani, Mwanawankhosa+ wa Mulungu!” 37  Ophunzira awiriwo atamumva akunena zimenezi, anatsatira Yesu. 38  Kenako Yesu anacheuka, ndipo atawaona akumutsatira, anawafunsa kuti: “Kodi mukufunafuna chiyani?” Iwo anati: “Rabi, (dzina limeneli akalimasulira limatanthauza, “Mphunzitsi”) kodi mumakhala kuti?” 39  Iye anawauza kuti: “Tiyeni mukaoneko.” Choncho anapita kukaona kumene ankakhala ndipo anakhala naye tsiku limenelo. Apa nʼkuti nthawi ili cha mʼma 4 koloko madzulo.* 40  Andireya,+ mchimwene wake wa Simoni Petulo anali mmodzi wa awiriwo, amene anamva zimene Yohane ananena nʼkutsatira Yesu. 41  Choyamba iyeyu anakumana ndi mchimwene wake Simoni ndipo anamuuza kuti: “Ifetu tapeza Mesiya”+ (dzina limeneli akalimasulira limatanthauza, “Khristu”), 42  ndipo anapita naye kwa Yesu. Yesu atamuyangʼana anati: “Iwe ndiwe Simoni+ mwana wa Yohane, dzina lako likhala Kefa” (limene kumasulira kwake ndi “Petulo”).+ 43  Tsiku lotsatira, Yesu anaganiza zoti apite ku Galileya. Ndiyeno anakumana ndi Filipo+ nʼkumuuza kuti: “Ukhale wotsatira wanga.” 44  Filipo anali wochokera ku Betsaida, mzinda umene kunkachokera Andireya ndi Petulo. 45  Kenako Filipo anakumana ndi Natanayeli+ nʼkumuuza kuti: “Ife tapeza Yesu, mwana wa Yosefe,+ wa ku Nazareti. Chilamulo cha Mose komanso zimene aneneri analemba zimanena za iyeyu.” 46  Koma Natanayeli anamufunsa kuti: “Kodi mu Nazareti mungatuluke munthu aliyense wabwino?” Filipo anamuuza kuti: “Tiye ukaone.” 47  Yesu ataona Natanayeli akubwera kumene iye anali, ananena kuti: “Onani Mwisiraeli ndithu, amene mwa iye mulibe chinyengo.”+ 48  Natanayeli anamufunsa kuti: “Mwandidziwa bwanji?” Yesu anamuyankha kuti: “Filipo asanakuitane, ine ndinakuona uli pansi pa mtengo wamkuyu paja.” 49  Natanayeli anamuyankha kuti: “Rabi, ndinu Mwana wa Mulungu, ndinu Mfumu ya Isiraeli.”+ 50  Yesu anamuyankha kuti: “Kodi wakhulupirira chifukwa choti ndakuuza kuti ndinakuona uli pansi pa mtengo wamkuyu? Udzaona zinthu zazikulu kuposa zimenezi.” 51  Kenako anamuuza kuti: “Ndithu ndikukuuzani anthu inu, mudzaona kumwamba kutatseguka, angelo a Mulungu akukwera ndi kutsika kupita kumene kuli Mwana wa munthu.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “anali ngati mulungu.”
Kapena kuti, “ankamusonyeza kukoma mtima kwakukulu.”
Kapena kuti, “pachifuwa cha Atate.” Izi zikusonyeza kuti ankakondedwa mwapadera.
Kapena kuti, “mwangamu wandipitirira.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ola la 10,” kuwerenga kuchokera mʼma 6 koloko mʼmawa.