Wolembedwa ndi Yohane 9:1-41
9 Akuyenda anaona munthu amene anabadwa ndi vuto losaona.
2 Ophunzira ake anamufunsa kuti: “Rabi,+ anachimwa ndi ndani kuti munthuyu abadwe ndi vuto losaonali? Ndi iyeyu kapena makolo ake?”
3 Yesu anayankha kuti: “Munthuyu kapena makolo ake, onse sanachimwe. Koma izi zinachitika kuti ntchito za Mulungu zionekere kudzera mwa iye.+
4 Tiyenera kugwira ntchito za Mulungu amene anandituma kudakali masana.+ Usiku ukubwera pamene munthu sangagwire ntchito.
5 Pamene ine ndili mʼdziko, ndine kuwala kwa dzikoli.”+
6 Atanena zimenezi, analavulira malovu pansi nʼkukanda matope ndi malovuwo, kenako anapaka matopewo mʼmaso mwa munthuyo.+
7 Ndiyeno anamuuza kuti: “Pita ukasambe mʼdziwe la Siloamu” (dzina limene kumasulira kwake ndi “Otumizidwa”). Choncho anapita kukasamba ndipo anabwerako akuona.+
8 Ndiyeno anthu oyandikana nawo komanso anthu ena amene mʼmbuyomo ankamuona akupemphapempha anayamba kunena kuti: “Kodi uyu si amene ankakhala pansi nʼkumapemphapempha uja?”
9 Ena ankanena kuti: “Ndi yemweyu.” Enanso ankanena kuti: “Ayi, wangofanana naye.” Koma mwiniwakeyo ankawauza kuti: “Inde, ndi ineyo.”
10 Choncho anamufunsa kuti: “Ndiye maso akowa atseguka bwanji?”
11 Iye anayankha kuti: “Munthu wina dzina lake Yesu anakanda matope nʼkuwapaka mʼmaso mwangamu. Kenako anandiuza kuti, ‘Pita ku Siloamu ukasambe.’+ Ndiye ndinapitadi kukasamba ndipo ndayamba kuona.”
12 Atatero anthuwo anamufunsa kuti: “Ali kuti munthu ameneyo?” Iye ananena kuti: “Sindikudziwa.”
13 Iwo anatenga munthu amene poyamba anali wosaona uja nʼkupita naye kwa Afarisi.
14 Tsiku limene Yesu anakanda matope nʼkutsegula maso a munthuyo+ linali la Sabata.+
15 Pa nthawi imeneyo Afarisi nawonso anayamba kufunsa munthu uja mmene anayambira kuona. Iye anawafotokozera kuti: “Anapaka matope mʼmaso mwanga, ndiye ndinapita kukasamba, basi kenako ndayamba kuona.”
16 Ndiyeno ena mwa Afarisiwo anayamba kunena kuti: “Munthu ameneyu si wochokera kwa Mulungu, chifukwa sasunga Sabata.”+ Ena ankanena kuti: “Kodi munthu wochimwa angachite bwanji zizindikiro ngati zimenezi?”+ Choncho anthuwo anagawanika.+
17 Afarisiwo anafunsanso munthu amene anali wosaona uja kuti: “Nanga iwe ukuti bwanji za munthu ameneyu, popeza kuti wakutsegula maso?” Munthuyo anati: “Ndi mneneri.”
18 Komabe Ayudawo sanakhulupirire kuti munthuyu analidi wosaona ndipo wayamba kuona, mpaka anaitanitsa makolo ake a munthuyo.
19 Iwo anafunsa makolowo kuti: “Kodi uyu ndi mwana wanu amene mukuti anabadwa wosaona? Nanga zatheka bwanji kuti ayambe kuona?”
20 Makolo akewo anayankha kuti: “Tikudziwa kuti uyu ndi mwana wathu komanso kuti anabadwa wosaona.
21 Koma sitikudziwa kuti zatheka bwanji kuti ayambe kuona panopa, komanso sitikudziwa amene wamutsegula maso. Mufunseni mwiniwakeyu. Ndi wamkulu ameneyu, afotokoze yekha.”
22 Makolo akewo ananena zimenezi chifukwa ankaopa atsogoleri achipembedzo a Chiyuda.+ Chifukwa iwo anali atagwirizana kale kuti ngati wina angavomereze kuti Yesu ndi Khristu, azimuchotsa musunagoge.+
23 Nʼchifukwa chake makolo akewo ananena kuti: “Ndi wamkulu ameneyu. Mufunseni mwiniwakeyu.”
24 Choncho iwo anaitananso munthu amene anali wosaona uja kachiwiri nʼkumuuza kuti: “Lemekeza Mulungu, ife tikudziwa kuti munthu ameneyu ndi wochimwa.”
25 Iye anayankha kuti: “Zoti ndi wochimwa, ine sindikudziwa. Chimodzi chokha chimene ine ndikudziwa nʼchakuti, poyamba ndinali wosaona koma tsopano ndikuona.”
26 Ndiyeno iwo anamufunsa kuti: “Anakuchita chiyani? Watsegula bwanji maso ako?”
27 Iye anawayankha kuti: “Ndakuuzani kale koma inu simumamvetsera. Nanga nʼchifukwa chiyani mukufuna kumvanso? Kapena inunso mukufuna kukhala ophunzira ake?”
28 Atanena zimenezi, iwo anamunyoza kuti: “Iweyo ndi amene uli wophunzira wa munthu amene uja, koma ife ndi ophunzira a Mose.
29 Tikudziwa kuti Mulungu analankhula ndi Mose, koma za munthu uyu, sitikudziwa kuti akuchokera kuti.”
30 Munthuyo anawayankha kuti: “Zimenezi nʼzodabwitsa ndithu, simukudziwa kumene wachokera, chikhalirecho wanditsegula maso.
31 Tikudziwa kuti Mulungu samvetsera ochimwa,+ koma ngati munthu amaopa Mulungu ndipo amachita chifuniro chake, munthu ameneyo amamumvetsera.+
32 Kuyambira kalekale sitinamvepo kuti munthu wina watsegula maso a munthu amene anabadwa wosaona.
33 Munthu ameneyu akanakhala kuti si wochokera kwa Mulungu, sakanatha kuchita chilichonse.”+
34 Poyankha iwo anamuuza kuti: “Wobadwira mu uchimo wokhawokha iwe. Ndiye kodi ukufuna utiphunzitse?” Zitatero anamuchotsa musunagoge!+
35 Yesu anamva kuti munthu uja amuchotsa musunagoge. Ndipo atakumana naye anamufunsa kuti: “Kodi ukukhulupirira Mwana wa munthu?”
36 Munthuyo anayankha kuti: “Kodi mwana wa munthuyo ndi ndani? Ndiuzeni bambo kuti ndimukhulupirire.”
37 Yesu anamuuza kuti: “Wamuona kale, ndipo ndi amene akulankhula nawe panopa.”
38 Iye ananena kuti: “Ndakukhulupirirani Ambuye.” Ndipo anamugwadira.
39 Ndiyeno Yesu ananena kuti: “Ndinabwera mʼdziko lino kudzapereka chiweruzo chakuti, osaona ayambe kuona+ ndipo amene akuona akhale osaona.”+
40 Afarisi amene anali naye anamva zimenezi, ndipo anafunsa Yesu kuti: “Kodi ifenso ndife osaona?”
41 Yesu anawauza kuti: “Mukanakhala osaona, simukanakhala ndi tchimo. Koma popeza mukunena kuti ‘Tikuona,’ tchimo lanu silidzakhululukidwa.”+