Yona 1:1-17

  • Yona ankafuna kuthawa Yehova (1-3)

  • Yehova anayambitsa chimphepo (4-6)

  • Mavuto anayamba chifukwa cha Yona (7-13)

  • Yona anaponyedwa mʼnyanja (14-16)

  • Chinsomba chinameza Yona (17)

1  Yehova analankhula ndi Yona*+ mwana wa Amitai, kuti:  “Nyamuka upite kumzinda waukulu wa Nineve.+ Kumeneko ukalengeze uthenga wachiweruzo kwa anthu amumzindawo chifukwa ndaona zoipa zimene akuchita.”  Koma Yona ananyamuka nʼkulowera ku Tarisi, kuthawa Yehova. Atafika ku Yopa anapeza chombo chopita ku Tarisi. Iye analipira ndalama za ulendowo pothawa Yehova nʼkukwera chombocho kuti apite ku Tarisi limodzi ndi anthu amene anali mmenemo.  Ndiyeno Yehova anabweretsa mphepo yamphamvu panyanja, ndipo kenako panachitika chimkuntho choopsa, moti chombocho chinatsala pangʼono kusweka.  Oyendetsa chombo anachita mantha kwambiri ndipo aliyense anayamba kuitana mulungu wake kuti amuthandize. Iwo anayamba kuponya mʼnyanja katundu amene anali mʼchombocho kuti chipepukidwe.+ Apa nʼkuti Yona atatsikira mkatikati mwa chombocho nʼkugona tulo tofa nato.  Kenako woyendetsa chombo anapita pamene Yona anagona nʼkumufunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani ukungogona? Tadzuka uitane mulungu wako! Mwina Mulungu woona atikomera mtima ndipo sitifa.”+  Ndiyeno anayamba kuuzana kuti: “Tiyeni tichite maere+ kuti tidziwe amene wachititsa kuti tsokali litigwere.” Choncho anachitadi maere ndipo maerewo anagwera Yona.+  Ndiyeno anamufunsa kuti: “Tiuze, ndani wachititsa kuti tsoka limeneli litigwere? Umagwira ntchito yanji ndipo ukuchokera kuti? Kwanu nʼkuti ndipo ndiwe wa mtundu uti?”  Iye anayankha kuti: “Ndine Mheberi ndipo ndimaopa* Yehova Mulungu wakumwamba, amene anapanga nyanja ndi mtunda.” 10  Anthuwo atamva zimenezi anachita mantha kwambiri, ndipo anamufunsa kuti: “Wachitiranji zimenezi?” (Anthuwo anadziwa kuti Yona akuthawa Yehova, chifukwa iye anali atawauza zimenezo.) 11  Kenako anamufunsa kuti: “Ndiye tichite nawe chiyani kuti nyanjayi ikhale bata?” Apa nʼkuti chimkuntho choopsa chija chikukulirakulira. 12  Iye anawayankha kuti: “Mundinyamule nʼkundiponya mʼnyanjamu ndipo nyanjayi ikhala bata. Ndikudziwa kuti mkunthowu ukuchitika chifukwa cha ine.” 13  Koma anthuwo anayesetsa kuti adutse mafunde amphamvuwo nʼkukafika kumtunda. Komabe sanakwanitse chifukwa mkunthowo unkawonjezeka kwambiri. 14  Kenako anthuwo anafuulira Yehova kuti: “Chonde Yehova, musalole kuti tife chifukwa cha munthu uyu! Musatiimbe mlandu wa magazi a munthu wosalakwa, chifukwa inu Yehova mwachita zimene mumafuna.” 15  Kenako ananyamula Yona nʼkumuponya mʼnyanja ndipo nyanjayo inakhala bata. 16  Zitatero anthuwo anaopa kwambiri Yehova.+ Choncho anapereka nsembe kwa Yehova ndipo analonjeza kuti azimutumikira. 17  Tsopano Yehova anatumiza chinsomba chachikulu kuti chikameze Yona moti Yona anakhala mʼmimba mwa nsomba masiku atatu, masana ndi usiku.+

Mawu a M'munsi

Kutanthauza “Nkhunda.”
Kapena kuti, “ndimalambira.”