Yona 2:1-10

  • Pemphero la Yona ali mʼmimba mwa chinsomba (1-9)

  • Chinsomba chinalavulira Yona kumtunda (10)

2  Kenako Yona anapemphera kwa Yehova Mulungu wake, ali mʼmimba mwa chinsombacho.+  Iye anati: “Nditavutika kwambiri ndinaitana inu Yehova ndipo munandiyankha.+ Ndinafuula kupempha thandizo ndili mʼManda* akuya,+ Ndipo inu munamva mawu anga.   Mutandiponya pamalo ozama, pansi penipeni pa nyanja yakuya,Madzi amphamvu anandimiza.+ Mafunde anu amphamvu anadutsa pamwamba panga.+   Ndipo ine ndinati, ‘Mwandithamangitsa pamaso panu! Kodi kachisi wanu woyera ndidzamuonanso?’   Madzi anandimiza moti ndinangotsala pangʼono kufa.+Ndinamira mʼmadzi akuya kwambiri. Zomera zamʼnyanja zinakulunga mutu wanga.   Ndinamira mpaka mʼmunsi mwenimweni mwa mapiri. Zotsekera za dziko lapansi zinayamba kunditsekereza kuti ndikhale komweko mpaka kalekale. Koma inu Yehova Mulungu wanga, munanditulutsa mʼdzenje ndili wamoyo.+   Nditatsala pangʼono kufa, ndinakumbukira Yehova.+ Ndipo pemphero langa linafika kwa inu mʼkachisi wanu woyera.+   Anthu okhulupirira mafano opanda pake, amasiya Mulungu amene angawasonyeze chikondi chokhulupirika.*   Koma ine, ndidzakutamandani ndi kupereka nsembe kwa inu. Zimene ndalonjeza ndidzazikwaniritsa.+ Chipulumutso chimachokera kwa Yehova.”+ 10  Kenako Yehova analamula chinsomba chija ndipo chinalavula Yona kumtunda.

Mawu a M'munsi

Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mabaibulo ena amati, “amasiya kukhulupirika kwawo.”