Yona 3:1-10

  • Yona anamvera Mulungu nʼkupita ku Nineve (1-4)

  • Anthu a ku Nineve analapa atamva uthenga wa Yona (5-9)

  • Mulungu anaganiza zoti asawononge Nineve (10)

3  Yehova analankhula ndi Yona kachiwiri kuti:+  “Nyamuka, upite kumzinda waukulu wa Nineve,+ ndipo ukalalikire uthenga umene ndikuuze.”  Choncho Yona ananyamuka nʼkupita ku Nineve+ pomvera mawu a Yehova.+ Mzinda wa Nineve unali waukulu kwambiri* ndipo mtunda wake unali woyenda masiku atatu.  Kenako Yona analowa mumzindawo nʼkuyenda ulendo wa tsiku limodzi. Iye ankalalikira kuti: “Kwangotsala masiku 40 okha ndipo Nineve awonongedwa.”  Anthu a ku Nineve anakhulupirira Mulungu+ ndipo anayamba kulengeza kuti aliyense, popanda wotsala, asale kudya ndipo avale ziguduli.  Uthengawo utafika kwa mfumu ya Nineve, mfumuyo inanyamuka pampando wake wachifumu nʼkuvula chovala chake chachifumu. Kenako inavala chiguduli nʼkukhala paphulusa.  Kuwonjezera pamenepo, mfumu inalamula anthu kuti alengeze mu Nineve kuti:“Mfumu ndi akuluakulu ake alamula kuti: Munthu aliyense, ngʼombe, nkhosa komanso chiweto chilichonse zisadye chilichonse. Munthu aliyense kapena chiweto zisadye chakudya kapena kumwa madzi.  Munthu aliyense komanso ziweto zivale chiguduli. Afuulire Mulungu kuchokera pansi pa mtima ndipo aliyense asiye zinthu zoipa komanso zachiwawa zimene amachita.  Ndani angadziwe, mwina Mulungu woona asintha maganizo pa zimene amafuna kuchita ndipo abweza mkwiyo wake woyaka moto, moti satiwononga?” 10  Mulungu woona ataona zimene anachita, kuti anasiya kuchita zoipa,+ anasintha maganizo ake ndipo sanawabweretsere tsoka limene ananena kuti awabweretsera.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Mulungu ankauona kuti ndi mzinda waukulu.”