Yona 4:1-11

  • Yona anakwiya ndipo ankafuna kufa (1-3)

  • Yehova anaphunzitsa Yona kukhala wachifundo (4-11)

    • “Kodi pali chifukwa choti ukwiyire choncho?” (4)

    • Anamuphunzitsa pogwiritsa ntchito chomera chamtundu wa mphonda (6-10)

4  Koma zimenezi sizinamusangalatse Yona ngakhale pangʼono moti anakwiya koopsa.  Choncho iye anapemphera kwa Yehova kuti: “Inu Yehova, kodi zimene ndimaopa ndili kwathu zija si zimenezi? Nʼchifukwa chaketu ndinkafuna kuthawira ku Tarisi.+ Ndinadziwa kuti inu ndinu Mulungu wachifundo, wokoma mtima, wosakwiya msanga, wachikondi chokhulupirika chochuluka+ komanso mumamva chisoni mukafuna kubweretsa tsoka.  Inu Yehova, chotsani moyo wanga, chifukwa kuli bwino ndingofa kusiyana nʼkuti ndikhale ndi moyo.”+  Yehova anamufunsa kuti: “Kodi pali chifukwa choti ukwiyire choncho?”  Kenako Yona anatuluka mumzindawo nʼkukakhala pansi kumʼmawa kwa mzindawo. Kumeneko anamanga kachisakasa kuti akhale pamthunzi podikira kuti aone zimene zichitikire mzindawo.+  Ndiyeno Yehova Mulungu anameretsa chomera cha mtundu wa mphonda* kuti chiyange pamene Yona anakhala. Anachita zimenezi kuti pakhale mthunzi nʼcholinga choti apeze mpumulo. Yona anasangalala kwambiri chifukwa cha chomeracho.  Koma Mulungu woona anatumiza mbozi mʼbandakucha wa tsiku lotsatira kuti ikadye chomera cha mtundu wa mphondacho, moti chinafota.  Dzuwa litatuluka, Mulungu anatumizanso mphepo yotentha yochokera kumʼmawa. Dzuwa linawotcha kwambiri Yona moti anangotsala pangʼono kukomoka. Choncho Yona anapempha mobwerezabwereza kuti angofa. Iye ankanena kuti: “Kuli bwino ndingofa kusiyana nʼkuti ndikhale ndi moyo.”+  Ndiyeno Mulungu anafunsa Yona kuti: “Kodi pali chifukwa choti ukwiyire ndi chomera cha mtundu wa mphondachi?”+ Yona anayankha kuti: “Ndikuyeneradi kukwiya, ndakwiya kwambiri moti ndikufuna kufa.” 10  Koma Yehova anati: “Iwe ukumvera chisoni chomera cha mtundu wa mphondachi, chimene sunachivutikire kapena kuchikulitsa, chimene changomera usiku umodzi wokha kenako nʼkufa. 11  Kodi ine sindikuyenera kumvera chisoni mzinda waukulu wa Nineve,+ mmene muli anthu oposa 120,000, omwe sadziwa kusiyanitsa zoyenera ndi zolakwika?* Kodi sindiyenera kumveranso chisoni ziweto zawo zambiri?”+

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “nsatsi.”
Kapena kuti, “dzanja lawo lamanja ndi lamanzere.”