Yoswa 12:1-24

  • Mafumu amene anagonjetsedwa kumʼmawa kwa Yorodano (1-6)

  • Mafumu amene anagonjetsedwa kumadzulo kwa Yorodano (7-24)

12  Awa ndi mafumu amene Aisiraeli anagonjetsa nʼkulanda madera awo kumʼmawa kwa mtsinje wa Yorodano, kuchokera kuchigwa cha Arinoni+ kukafika kuphiri la Herimoni+ ndi ku Araba konse, chakumʼmawa:+  Sihoni+ mfumu ya Aamori, yemwe ankakhala ku Hesiboni ndipo ankalamulira kuyambira kumzinda wa Aroweli,+ womwe unali mʼmbali mwa chigwa cha Arinoni+ komanso kuyambira pakatikati pa chigwachi, ndi hafu ya Giliyadi mpaka kukafika kuchigwa cha Yaboki, kumalire ndi Aamoni.  Ankalamuliranso ku Araba mpaka kunyanja ya Kinereti*+ chakumʼmawa kwa nyanjayi, mpaka kukafika kunyanja ya Araba, yomwe ndi Nyanja Yamchere.* Komanso ankalamulira kumʼmawa, cha ku Beti-yesimoti ndiponso chakumʼmwera, kumunsi kwa Pisiga.+  Mfumu ina ndi Ogi+ wa ku Basana yemwe anali mmodzi wa Arefai+ otsala, ndipo ankakhala ku Asitaroti ndi ku Edirei.  Ankalamulira kuphiri la Herimoni, ku Saleka ndi ku Basana+ konse, mpaka kukafika kumalire a Agesuri ndi Amaakati.+ Ankalamuliranso hafu ya Giliyadi mpaka kumalire ndi dera limene Sihoni, mfumu ya Hesiboni, ankalamulira.+  Mose mtumiki wa Yehova ndi Aisiraeli anagonjetsa mafumuwa.+ Kenako Mose mtumiki wa Yehova anapereka maderawa kwa fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi hafu ya fuko la Manase kuti akhale awo.+  Yoswa ndi Aisiraeli anagonjetsa mafumu akudera lakumadzulo kwa mtsinje wa Yorodano, kuchokera ku Baala-gadi+ kuchigwa cha Lebanoni+ mpaka kuphiri la Halaki,+ limene lili moyangʼanizana ndi Seiri.+ Atawagonjetsa, Yoswa anapereka dzikolo kwa mafuko a Isiraeli poligawa mʼmagawomagawo.+  Dzikoli linkaphatikizapo dera lamapiri, dera la Sefela, chigwa cha Araba, malo otsetsereka, chipululu ndi Negebu.+ Limeneli linali dziko la Ahiti, Aamori,+ Akanani, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi.+ Mafumu awo anali awa:   Mfumu ya Yeriko,+ imodzi. Mfumu ya Ai+ pafupi ndi Beteli, imodzi. 10  Mfumu ya Yerusalemu, imodzi. Mfumu ya Heburoni,+ imodzi. 11  Mfumu ya Yarimuti, imodzi. Mfumu ya Lakisi, imodzi. 12  Mfumu ya Egiloni, imodzi. Mfumu ya Gezeri,+ imodzi. 13  Mfumu ya Debiri,+ imodzi. Mfumu ya Gederi, imodzi. 14  Mfumu ya Horima, imodzi. Mfumu ya Aradi, imodzi. 15  Mfumu ya Libina,+ imodzi. Mfumu ya Adulamu, imodzi. 16  Mfumu ya Makeda,+ imodzi. Mfumu ya Beteli,+ imodzi. 17  Mfumu ya Tapuwa, imodzi. Mfumu ya Heferi, imodzi. 18  Mfumu ya Afeki, imodzi. Mfumu ya Lasaroni, imodzi. 19  Mfumu ya Madoni, imodzi. Mfumu ya Hazori,+ imodzi. 20  Mfumu ya Simironi-meroni, imodzi. Mfumu ya Akasafu, imodzi. 21  Mfumu ya Taanaki, imodzi. Mfumu ya Megido, imodzi. 22  Mfumu ya Kadesi, imodzi. Mfumu ya Yokineamu+ ku Karimeli, imodzi. 23  Mfumu ya Dori kumapiri a Dori,+ imodzi. Mfumu ya Goimu ku Giligala, imodzi. 24  Mfumu ya Tiriza, imodzi. Mafumu onse analipo 31.

Mawu a M'munsi

Imeneyi ndi Nyanja Yakufa.
Imeneyi ndi nyanja ya Genesareti yomwe inkadziwikanso kuti nyanja ya Galileya.