Yoswa 14:1-15

  • Kugawa malo kumadzulo kwa Yorodano (1-5)

  • Kalebe anapatsidwa Heburoni kuti akhale cholowa chake (6-15)

14  Aisiraeli anatenga cholowa chawo mʼdziko la Kanani. Wansembe Eliezara, Yoswa mwana wa Nuni ndi atsogoleri a mafuko a makolo a Aisiraeli ndi amene anawagawira cholowachi.+  Pogawa cholowacho kwa mafuko 9 ndi hafu,+ anachita maere+ mogwirizana ndi zimene Yehova analamula kudzera mwa Mose.  Mose anali atagawira kale cholowa mafuko awiri ndi hafu kutsidya lina la Yorodano.*+ Koma Alevi sanawagawire cholowacho.+  Ana a Yosefe anali mafuko awiri,+ la Manase ndi la Efuraimu.+ Alevi sanapatsidwe cholowa cha malo koma anangowapatsa mizinda+ yoti azikhalamo komanso malo odyetserako ziweto ndi osungirako katundu wawo.+  Choncho Aisiraeli anagawana dzikolo mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.  Tsopano amuna a ku Yuda anapita kwa Yoswa ku Giligala.+ Ndipo Kalebe+ mwana wa Yefune Mkenizi, anauza Yoswa kuti: “Inu mukudziwa bwino zimene Yehova anauza+ Mose, munthu wa Mulungu woona,+ ku Kadesi-barinea zokhudza ine ndi inu.+  Ndinali ndi zaka 40 pamene Mose mtumiki wa Yehova anandituma kudzafufuza zokhudza dzikoli,+ kuchokera ku Kadesi-barinea. Nditabwerako ndinamuuza moona mtima zonse zimene ndinaona.+  Ngakhale kuti abale anga amene ndinali nawo, anapangitsa anthu kuchita mantha kwambiri,* ine ndinatsatira Yehova Mulungu wanga ndi mtima wonse.+  Mose anandilumbirira tsiku limenelo kuti: ‘Dziko limene wakaliponda ndi mapazi ako lidzakhala cholowa chako ndi cha ana ako mpaka kalekale, chifukwa watsatira Yehova Mulungu wanga ndi mtima wako wonse.’+ 10  Yehova wandisunga ndi moyo+ mogwirizana ndi zimene analonjeza.+ Tsopano padutsa zaka 45 kuchokera pamene Yehova analonjeza Mose pa nthawi imene Aisiraeli anali mʼchipululu.+ Lero ndili ndi zaka 85. 11  Ndipo ndine wamphamvu ngati mmene ndinalili tsiku limene Mose anandituma. Mphamvu zanga zidakali mmene zinalili pa nthawiyo, moti ndikhoza kupita kunkhondo komanso kuchita zinthu zina. 12  Choncho ndipatseni dera lamapiri ili limene Yehova anandilonjeza tsiku limene lija. Ngakhale kuti pa tsikulo, munamva kuti kumeneko kuli Aanaki+ komanso mizinda ikuluikulu yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri,+ sindikukayikira kuti Yehova adzakhala nane,+ ndipo ndikawathamangitsa ndithu ngati mmene Yehova analonjezera.”+ 13  Choncho Yoswa anadalitsa Kalebe mwana wa Yefune ndipo anamʼpatsa mzinda wa Heburoni kuti ukhale cholowa chake.+ 14  Nʼchifukwa chake mzinda wa Heburoni unakhala cholowa cha Kalebe mwana wa Yefune Mkenizi, mpaka lero, chifukwa iye anatsatira Yehova Mulungu wa Isiraeli ndi mtima wake wonse.+ 15  Poyamba mzinda wa Heburoni unkatchedwa Kiriyati-ariba.+ (Ariba anali munthu wamphamvu pakati pa Aanaki.) Kenako mʼdzikolo munakhala mopanda nkhondo.+

Mawu a M'munsi

Imeneyi ndi mbali yakumʼmawa.
Mʼchilankhulo choyambirira, “anachititsa mitima ya anthu kusungunuka.”