Yoswa 15:1-63

  • Cholowa cha fuko la Yuda (1-12)

  • Mwana wamkazi wa Kalebe analandira malo (13-19)

  • Mizinda ya anthu a fuko la Yuda (20-63)

15  Gawo limene linaperekedwa+ ku fuko la Yuda kuti ligawidwe kwa mabanja awo linkafika kumalire a Edomu+ ndi kuchipululu cha Zini, mpaka kumapeto kwa Negebu, kumʼmwera.  Malire awo akumʼmwera ankayambira kumapeto kwa Nyanja Yamchere,*+ kugombe lake lakumʼmwera.  Malirewo analowera kumʼmwera kuchitunda cha Akirabimu+ nʼkukafika ku Zini. Kenako anakwera kuchokera kumʼmwera kupita ku Kadesi-barinea,+ nʼkukafika ku Hezironi mpaka ku Adara, nʼkuzungulira kukafika cha ku Karika.  Ndiyeno anapitirira kukafika ku Azimoni+ mpaka kuchigwa cha Iguputo+ nʼkukathera ku Nyanja.* Amenewa anali malire awo akumʼmwera.  Malire akumʼmawa anali Nyanja Yamchere* mpaka pamene mtsinje wa Yorodano umathira mʼnyanjayi. Malire akumpoto anakhota pagombe pamene mtsinje wa Yorodano umathirira mʼnyanjayi.+  Malirewo anapitirira mpaka ku Beti-hogila+ nʼkukadutsa kumpoto kwa Beti-araba,+ kukafika kumwala wa Bohani,+ mwana wa Rubeni.  Anakafika ku Debiri kuchigwa cha Akori+ nʼkukhotera kumpoto cha ku Giligala,+ patsogolo pa chitunda cha Adumi, kumʼmwera kwa chigwa cha mtsinje. Malirewo anapitirira nʼkukafika kumadzi a Eni-semesi,+ nʼkukathera ku Eni-rogeli.+  Kuchokera pamenepo, anapitirira mpaka kuchigwa cha mwana wa Hinomu,+ kumalo otsetsereka otchedwa Yebusi+ kumʼmwera, kutanthauza Yerusalemu.+ Anapitirirabe mpaka pamwamba pa phiri loyangʼanizana ndi chigwa cha Hinomu, limene lili kumadzulo kwa chigwacho. Phirilo lili kumpoto kwa chigwa cha Arefai, kumapeto kwa chigwacho.  Kuchokera pamwamba pa phirilo, malirewo anakafika kukasupe wa madzi a Nafitoa,+ nʼkupitirira mpaka kumizinda ya mʼmbali mwa phiri la Efuroni. Anapitirirabe mpaka ku Baala, kutanthauza Kiriyati-yearimu.+ 10  Kuchokera ku Baala, malirewo anazungulira chakumadzulo kulowera kuphiri la Seiri, nʼkukadutsa pamalo otsetsereka a phiri la Yearimu kumpoto, kutanthauza Kesaloni. Ndiyeno anatsetserekera ku Beti-semesi,+ nʼkukafika ku Timuna.+ 11  Malirewo anakafika kumalo otsetsereka otchedwa Ekironi+ kumpoto, nʼkukadutsa ku Sikeroni. Anapitirira mpaka kuphiri la Baala kukafika ku Yabineeli, nʼkukathera kunyanja. 12  Malire akumadzulo anali Nyanja Yaikulu*+ ndi gombe lake. Amenewa anali malire a ana a Yuda a mbali zonse motsatira mabanja awo. 13  Kalebe+ mwana wa Yefune anamʼpatsa gawo lake pakati pa ana a Yuda pomvera lamulo la Yehova kwa Yoswa. Anamʼpatsa Kiriyati-ariba, kutanthauza Heburoni. (Ariba anali bambo wa Anaki.)+ 14  Choncho Kalebe anathamangitsa mbadwa za ana atatu a Anaki+ kuderalo. Anawo anali Sesai, Ahimani ndi Talimai.+ 15  Kenako anapita kukamenyana ndi anthu a mumzinda wa Debiri.+ (Poyamba dzina la mzinda wa Debiri linali Kiriyati-seferi.) 16  Kenako Kalebe anati: “Aliyense amene agonjetse mzinda wa Kiriyati-seferi nʼkuulanda, ndidzamʼpatsa mwana wanga Akisa, kuti akhale mkazi wake.” 17  Otiniyeli+ mwana wa Kenazi,+ mʼbale wake wa Kalebe, analanda mzindawo. Choncho Kalebe anamʼpatsa Akisa,+ mwana wake, kuti akhale mkazi wake. 18  Pamene Akisa ankapita kunyumba, anauza Otiniyeli kuti apemphe munda kwa Kalebe bambo ake. Kenako Akisa anatsika pabulu.* Atatero Kalebe anamʼfunsa kuti: “Ukufuna chiyani?”+ 19  Iye anapempha kuti: “Ndidalitseni, poti mwandipatsa malo akumʼmwera* mundipatsenso Guloti-maimu.”* Atatero, Kalebe anamʼpatsa Guloti Wakumtunda ndi Guloti Wakumunsi. 20  Ichi chinali cholowa cha fuko la Yuda, motsatira mabanja awo. 21  Mizinda ya kumapeto kwa gawo la fuko la Yuda, chakumalire ndi Edomu+ kumʼmwera, inali Kabizeeli, Ederi, Yaguri, 22  Kina, Dimona, Adada, 23  Kedesi, Hazori, Itinani, 24  Zifi, Telemu, Bealoti, 25  Hazori-hadata, Kerioti-hezironi, kutanthauza Hazori, 26  Amamu, Sema, Molada,+ 27  Hazara-gada, Hesimoni, Beti-peleti,+ 28  Hazara-suali, Beere-seba,+ Bizioti, 29  Baala, Iimu, Ezemu, 30  Elitoladi, Kesili, Horima,+ 31  Zikilaga,+ Madimana, Sanasana, 32  Lebaoti, Silihimu, Aini ndi Rimoni.+ Mizinda 29 pamodzi ndi midzi yake. 33  Ku Sefela+ kunali Esitaoli, Zora,+ Asina, 34  Zanowa, Eni-ganimu, Tapuwa, Enamu, 35  Yarimuti, Adulamu,+ Soko, Azeka,+ 36  Saaraimu,+ Aditaimu, Gedera ndi Gederotaimu.* Mizinda 14 ndi midzi yake. 37  Zenani, Hadasha, Migidala-gadi, 38  Dilani, Mizipe, Yokiteeli, 39  Lakisi,+ Bozikati, Egiloni, 40  Kaboni, Lamamu, Kitilisi, 41  Gederoti, Beti-dagoni, Naama ndi Makeda.+ Mizinda 16 ndi midzi yake. 42  Libina,+ Eteri, Asani,+ 43  Ifita, Asina, Nezibi, 44  Keila, Akizibu ndi Maresha. Mizinda 9 ndi midzi yake. 45  Ekironi pamodzi ndi midzi yake yozungulira, ikuluikulu ndi ingʼonoingʼono yomwe. 46  Kuchokera ku Ekironi kulowera chakumadzulo, malo onse amene ali mʼmbali mwa Asidodi ndi midzi yake. 47  Asidodi+ pamodzi ndi midzi yake yozungulira, ikuluikulu ndi ingʼonoingʼono yomwe, Gaza+ pamodzi ndi midzi yake yozungulira, ikuluikulu ndi ingʼonoingʼono yomwe, mpaka kukafika kuchigwa cha Iguputo ndi ku Nyanja Yaikulu* pamodzi ndi dera la mʼmbali mwa nyanjayi.+ 48  Kudera lamapiri kunali Samiri, Yatiri,+ Soko, 49  Dana, Kiriyati-sana, kutanthauza Debiri, 50  Anabi, Esitemo,+ Animu, 51  Goseni,+ Holoni ndi Gilo.+ Mizinda 11 ndi midzi yake. 52  Arabu, Duma, Esana, 53  Yanimu, Beti-tapuwa, Apeka, 54  Humita, Kiriyati-ariba kutanthauza Heburoni,+ ndi Ziori. Mizinda 9 ndi midzi yake. 55  Maoni,+ Karimeli, Zifi,+ Yuta, 56  Yezereeli, Yokideamu, Zanowa, 57  Kayini, Gibea ndi Timuna.+ Mizinda 10 ndi midzi yake. 58  Haluli, Beti-zuri, Gedori, 59  Maaratu, Beti-anotu ndi Elitekoni. Mizinda 6 ndi midzi yake. 60  Kiriyati-baala, kutanthauza Kiriyati-yearimu+ ndi Raba. Mizinda iwiri ndi midzi yake. 61  Kuchipululu kunali Beti-araba,+ Midini, Sekaka, 62  Nibisani, Mzinda wa Mchere ndi Eni-gedi.+ Mizinda 6 ndi midzi yake. 63  Amuna a fuko la Yuda analephera kuthamangitsa Ayebusi+ a ku Yerusalemu,+ moti Ayebusi+ akukhalabe limodzi ndi Ayuda ku Yerusalemu mpaka lero.

Mawu a M'munsi

Imeneyi ndi Nyanja Yakufa.
Imeneyi ndi Nyanja Yaikulu ya Mediterranean.
Imeneyi ndi Nyanja Yakufa.
Imeneyi ndi nyanja ya Mediterranean.
Mabaibulo ena amati, “anawomba mʼmanja ali pabulu.”
Kapena kuti, “mwandipatsa Negebu.”
Kutanthauza “Mabeseni a Madzi.”
Mabaibulo ena amati, “Gedala komanso makola ake a nkhosa.”
Imeneyi ndi nyanja ya Mediterranean.