Yoswa 16:1-10

  • Cholowa cha mbadwa za Yosefe (1-4)

  • Cholowa cha fuko la Efuraimu (5-10)

16  Gawo limene ana a Yosefe+ anapatsidwa+ linayambira kumtsinje wa Yorodano kufupi ndi Yeriko kukafika kumadzi akumʼmawa kwa Yeriko, kudutsa kuchipululu chochokera ku Yeriko kukafika kudera lamapiri la Beteli.+  Kuchokera ku Beteli wa ku Luzi, malire ake anakadutsa kumalire a Aareki ku Ataroti.  Kenako anatsetserekera kumadzulo kumalire a Ayafeleti, mpaka kukafika kumalire a Beti-horoni Wakumunsi+ kupita ku Gezeri,+ nʼkukathera kunyanja.  Choncho mbadwa za Yosefe,+ omwe ndi Manase ndi Efuraimu, analandira gawo lawo.+  Malire akumʼmawa a gawo la ana a Efuraimu motsatira mabanja awo anali awa: Kuchokera ku Ataroti-adara+ mpaka kukafika ku Beti-horoni Wakumtunda+  nʼkukathera kunyanja. Kumpoto kwake kunali Mikametatu,+ ndipo malirewo anazungulira chakumʼmawa kukafika ku Taanatu-silo, nʼkupitirirabe chakumʼmawa mpaka ku Yanoa.  Ndiyeno anatsetsereka kuchokera ku Yanoa kukafika ku Ataroti ndi ku Naara mpaka ku Yeriko,+ nʼkupitirirabe mpaka ku Yorodano.  Kuchokera ku Tapuwa,+ malirewo analowera chakumadzulo kuchigwa cha Kana nʼkukathera kunyanja.+ Chimenechi ndi cholowa cha fuko la Efuraimu motsatira mabanja awo.  Cholowa cha ana a Efuraimu chinaphatikizapo mizinda imene inali mkati mwa cholowa cha Manase,+ mizinda yonse ndi midzi yake. 10  Koma Aefuraimu sanathamangitse Akanani amene ankakhala ku Gezeri.+ Choncho Akananiwo akukhalabe pakati pa Aefuraimu mpaka lero,+ ndipo anayamba kuwagwiritsa ntchito yaukapolo.+

Mawu a M'munsi