Yoswa 17:1-18

  • Cholowa cha Manase ­chakumadzulo (1-13)

  • Dera lina la mbadwa za Yosefe (14-18)

17  Kenako fuko la Manase,+ mwana woyamba wa Yosefe,+ linapatsidwa gawo lake.+ Makiri+ mwana woyamba wa Manase, bambo wake wa Giliyadi, anali msilikali wamphamvu, choncho anapatsidwa dera la Giliyadi ndi Basana.+  Ana a Manase otsalawo anapatsidwa gawo lawo motsatira mabanja awo. Gawolo linaperekedwa kwa ana a Abi-ezeri,+ ana a Heleki, ana a Asiriyeli, ana a Sekemu, ana a Heferi ndi ana a Semida. Amenewa anali ana aamuna a Manase mwana wa Yosefe, motsatira mabanja awo.+  Tselofekadi+ mwana wa Heferi, mwana wa Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase, analibe ana aamuna, koma aakazi okhaokha. Mayina a anawo anali Mala, Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.  Iwo anapita kwa wansembe Eliezara,+ Yoswa mwana wa Nuni ndi atsogoleri, nʼkuwauza kuti: “Yehova ndi amene analamula Mose kuti atipatse cholowa pakati pa abale athu.”+ Choncho anawapatsa cholowa pakati pa azichimwene a bambo awo, pomvera lamulo la Yehova.+  Fuko la Manase linapatsidwa magawo 10, kuwonjezera pa dera la Giliyadi ndi Basana lomwe linali kutsidya lina* la Yorodano.+  Ana aakazi a fuko la Manase anapatsidwa cholowa pakati pa ana aamuna a fukolo, ndipo dera la Giliyadi linakhala cholowa cha ana otsala a fukolo.  Malire a gawo la fuko la Manase anayambira ku Aseri kukafika ku Mikametatu,+ patsogolo pa Sekemu.+ Malirewo analowera kumʼmwera* kukafika kwa anthu okhala ku Eni-Tapuwa.  Dera la Tapuwa+ linakhala la Manase, koma mzinda wa Tapuwa umene unali mʼmalire a Manase, unali wa ana a Efuraimu.  Malire a gawolo anatsetserekera kuchigwa cha Kana kenako analowera kumʼmwera kwa chigwachi. Pakati pa mizinda ya Manase panali mizinda ya Efuraimu+ ndipo malire a fuko la Manasewo anali kumpoto kwa chigwachi, ndipo anakathera kunyanja.+ 10  Kumʼmwera kwa malirewo linali gawo la Efuraimu, ndipo kumpoto linali gawo la Manase lomwe linakathera kunyanja.+ Kumpoto, gawo la Manase linakakumana ndi la Aseri, ndipo kumʼmawa linakakumana ndi la Isakara. 11  Mizinda yotsatirayi ya mʼgawo la Isakara ndi Aseri, pamodzi ndi anthu ake ndi midzi yake yozungulira, inali ya Manase: Beti-seani, Ibuleamu,+ Dori,+ Eni-dori,+ Taanaki,+ Megido komanso madera atatu amapiri. 12  Koma ana a Manase analephera kulanda mizindayi, moti Akanani anakakamira kukhalabe mʼderali.+ 13  Aisiraeli atakula mphamvu, anayamba kuwagwiritsa ntchito yaukapolo Akananiwo,+ koma sanathe kuwathamangitsiratu.+ 14  Ana a Yosefe anafunsa Yoswa kuti: “Nʼchifukwa chiyani mwatipatsa gawo limodzi lokha+ kuti likhale cholowa chathu, pomwe tilipo anthu ambiri popeza Yehova akutidalitsabe mpaka pano?”+ 15  Yoswa anawayankha kuti: “Ngati mulipo ambiri pitani kumtunda kunkhalango ya Aperezi+ ndi ya Arefai,+ mukagwetse mitengo nʼkutenga deralo, poti dera lamapiri la Efuraimu+ lakucheperani.” 16  Kenako ana a Yosefe anati: “Dera lamapiri silitikwanira, ndiponso Akanani akuchigwa, a ku Beti-seani+ ndi midzi yake yozungulira ndiponso akuchigwa cha Yezereeli+ ali ndi magaleta ankhondo+ okhala ndi zitsulo zazitali zakuthwa.” 17  Poyankha, Yoswa anauza anthu a fuko la Yosefe, omwe ndi ana a Efuraimu ndi Manase, kuti: “Ndinu ambiri ndipo ndinu amphamvu kwambiri. Simuyenera kukhala ndi gawo limodzi lokha,+ 18  koma mutengenso dera lamapiri.+ Ngakhale kuti ndi lankhalango, mudzagwetsamo mitengo ndipo gawo lanu likathera kumeneko. Mudzathamangitsa Akanani ngakhale kuti ndi amphamvu ndipo ali ndi magaleta ankhondo okhala ndi zitsulo zazitali zakuthwa.”+

Mawu a M'munsi

Imeneyi ndi mbali yakumʼmawa.
Mʼchilankhulo choyambirira, “kumanja.”