Yoswa 18:1-28

  • Dera lotsala linagawidwa ku Silo (1-10)

  • Cholowa cha fuko la Benjamini (11-28)

18  Kenako gulu lonse la Aisiraeli linasonkhana ku Silo,+ ndipo kumeneko anamanga chihema chokumanako,+ popeza pa nthawiyo nʼkuti atagonjetsa dzikolo.+ 2  Koma panali mafuko 7 a Aisiraeli amene anali asanagawiridwebe cholowa. 3  Choncho Yoswa anafunsa Aisiraeli kuti: “Kodi muzengereza mpaka liti osapita kukalanda dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu wakupatsani?+ 4  Sankhani amuna atatu pa fuko lililonse oti ndiwatume. Akayendere dzikolo nʼkulemba mmene lilili kuti lidzagawidwe mogwirizana ndi cholowa cha mafuko awo. Akatero adzabwerere kwa ine. 5  Ndiyeno adzagawe dzikolo mʼzigawo 7.+ Fuko la Yuda lidzakhalabe kugawo lawo kumʼmwera,+ ndipo a mʼbanja la Yosefe adzakhalabe kugawo lawo kumpoto.+ 6  Koma inuyo mukagawe dzikolo mʼzigawo 7 ndipo mukazilembe. Kenako mukabwere nazo kuno kuti ndidzakuchitireni maere+ pamaso pa Yehova Mulungu wathu. 7  Koma Alevi sadzapatsidwa gawo pakati panu,+ chifukwa cholowa chawo ndi unsembe wa Yehova.+ Fuko la Gadi, Rubeni ndi hafu ya fuko la Manase+ analandira kale cholowa chawo, chimene Mose mtumiki wa Yehova anawapatsa kutsidya lakumʼmawa la Yorodano.” 8  Choncho amuna aja anakonzeka kuti azipita, ndipo Yoswa anawalamula kuti: “Pitani mukayendere dzikolo nʼkulemba mmene lilili. Mukatero mukabwere kuno, ndipo ndidzakuchitirani maere pamaso pa Yehova ku Silo kuno.”+ 9  Amunawo anapitadi kukayendera dzikolo ndipo analigawa mʼzigawo 7 potsatira mizinda yake nʼkulemba mʼbuku. Atamaliza anabwerera kwa Yoswa kumsasa ku Silo. 10  Kenako Yoswa anawachitira maere pamaso pa Yehova ku Silo+ ndipo anagawira Aisiraeli dzikolo moti fuko lililonse analipatsa gawo limodzi.+ 11  Maere oyamba anagwera fuko la Benjamini motsatira mabanja awo, ndipo anapatsidwa dera limene linali pakati pa ana a Yuda+ ndi ana a Yosefe.+ 12  Kumpoto, malire a gawo lawo anayambira ku Yorodano nʼkupitirira kukafika kumalo otsetsereka akumpoto kwa Yeriko,+ nʼkukwera phiri chakumadzulo, nʼkukathera kuchipululu cha Beti-aveni.+ 13  Malirewo anapitirira kukafika kumʼmwera kwa malo otsetsereka otchedwa Luzi, kutanthauza Beteli.+ Kuchokera ku Luzi anatsetserekera ku Ataroti-adara,+ nʼkukadutsa paphiri lakumʼmwera kwa Beti-horoni Wakumunsi.+ 14  Kumadzulo kwa gawolo, malirewo anakhotera kumʼmwera, paphiri loyangʼanizana ndi kumʼmwera kwa Beti-horoni. Kuchokera pamenepo anakathera ku Kiriyati-baala, kutanthauza Kiriyati-yearimu,+ womwe ndi mzinda wa Yuda. Amenewa ndi malire akumadzulo a gawo la Benjamini. 15  Malire akumʼmwera a gawolo anayambira kumapeto kwa Kiriyati-yearimu, nʼkulowera chakumadzulo, nʼkupitirira kukafika kukasupe wa madzi a Nafitoa.+ 16  Malirewo anakafika kumapeto kwa phiri loyangʼanizana ndi chigwa cha Mwana wa Hinomu,+ limene linathera kumpoto kwa chigwa cha Arefai.+ Kenako anatsetserekera kuchigwa cha Hinomu kumʼmwera kwa malo otsetsereka otchedwa Yebusi+ mpaka kukafika ku Eni-rogeli.+ 17  Analowera chakumpoto nʼkukafika ku Eni-semesi mpaka kumzinda wa Gelilotu, womwe uli kutsogolo kwa chitunda cha Adumi.+ Kuchokera pamenepo, anatsetserekera kumwala+ wa Bohani,+ mwana wa Rubeni. 18  Anapitirira nʼkukafika kumalo otsetsereka akumpoto amene ali kutsogolo kwa Araba, nʼkutsetsereka kukafika ku Araba. 19  Malirewo anapitirira mpaka kumalo otsetsereka akumpoto kwa Beti-hogila,+ nʼkukathera kugombe lakumpoto kwa Nyanja Yamchere,*+ kumapeto kwa mtsinje wa Yorodano mbali yakumʼmwera. Awa anali malire akumʼmwera a gawo la Benjamini. 20  Kumʼmawa, malire ake anali mtsinje wa Yorodano. Ichi chinali cholowa cha ana a Benjamini motsatira mabanja awo, ndi malire ake kuzungulira gawo lonse. 21  Mizinda ya fuko la Benjamini motsatira mabanja awo inali Yeriko, Beti-hogila, Emeki-kezizi, 22  Beti-araba,+ Zemaraimu, Beteli,+ 23  Aavi, Para, Ofira, 24  Kefara-amoni, Ofini ndi Geba.+ Mizinda 12 ndi midzi yake. 25  Kunalinso Gibiyoni,+ Rama, Beeroti, 26  Mizipe, Kefira, Moza, 27  Rekemu, Iripeeli, Tarala, 28  Zela,+ Ha-elefi, Yebusi, kutanthauza Yerusalemu,+ Gibea+ ndi Kiriyati. Mizinda 14 ndi midzi yake. Chimenechi chinali cholowa cha ana a Benjamini motsatira mabanja awo.

Mawu a M'munsi

Imeneyi ndi Nyanja Yakufa.