Yoswa 19:1-51

  • Cholowa cha fuko la Simiyoni (1-9)

  • Cholowa cha fuko la Zebuloni (10-16)

  • Cholowa cha fuko la Isakala (17-23)

  • Cholowa cha fuko la Aseri (24-31)

  • Cholowa cha fuko la Nafitali (32-39)

  • Cholowa cha fuko la Dani (40-48)

  • Cholowa cha Yoswa (49-51)

19  Maere achiwiri+ anagwera Simiyoni, kutanthauza fuko la Simiyoni,+ motsatira mabanja awo. Cholowa chawo chinali pakati pa cholowa cha Yuda.+  Cholowa chawocho chinali Beere-seba+ kuphatikizapo Sheba, Molada,+  Hazara-suali,+ Bala, Ezemu,+  Elitoladi,+ Betuli, Horima,  Zikilaga,+ Beti-marikaboti, Hazara-susa,  Beti-lebaoti+ ndi Saruheni. Mizinda 13 ndi midzi yake.  Chinalinso Aini, Rimoni, Eteri ndi Asani.+ Mizinda 4 ndi midzi yake  ndiponso midzi yonse yozungulira mizinda imeneyi mpaka kukafika ku Baalati-beere, komwe ndi ku Rama wakumʼmwera. Ichi chinali cholowa cha fuko la Simiyoni motsatira mabanja awo.  Cholowa cha ana a Simiyoni chinatengedwa mʼgawo la Yuda chifukwa ana a Yuda gawo lawo linkawakulira. Choncho ana a Simiyoni anapatsidwa malo pakati pa cholowa chawo.+ 10  Maere achitatu+ anagwera ana a Zebuloni+ motsatira mabanja awo. Malire a cholowa chawo anakafika ku Saridi. 11  Malirewa analowera chakumadzulo, kukafika ku Marala ndipo anapitirira mpaka ku Dabeseti komanso kuchigwa chimene chili kutsogolo kwa Yokineamu. 12  Kuchokera ku Saridi analowera kumʼmawa mpaka kumalire a Kisilotu-tabori. Ndiyeno anapitirira kukafika ku Daberati+ mpaka ku Yafiya. 13  Kuchokera kumeneko, malirewo analowera chakumʼmawa nʼkukafika ku Gati-heferi,+ ku Eti-kazini ndi ku Rimoni mpaka ku Nea. 14  Malirewo anazungulira kumpoto kwa Nea kukafika ku Hanatoni, nʼkukathera kuchigwa cha Ifita-eli 15  komanso ku Katati, Nahalala, Simironi,+ Idala ndi ku Betelehemu.+ Mizinda 12 ndi midzi yake. 16  Chimenechi chinali cholowa cha ana a Zebuloni motsatira mabanja awo,+ ndipo imeneyi inali mizinda yawo ndi midzi yake. 17  Maere a 4+ anagwera Isakara,+ kapena kuti ana a Isakara motsatira mabanja awo. 18  Malire a gawo lawo anakafika ku Yezereeli,+ Kesulotu, Sunemu,+ 19  Hafaraimu, Sioni, Anaharati, 20  Rabiti, Kisioni, Ebezi, 21  Remeti, Eni-ganimu,+ Eni-hada ndi Beti-pazezi. 22  Malirewo anakafikanso ku Tabori,+ ku Sahazuma ndi ku Beti-semesi nʼkukathera ku Yorodano. Mizinda 16 ndi midzi yake. 23  Ichi chinali cholowa cha fuko la Isakara motsatira mabanja awo,+ ndipo imeneyi inali mizinda yawo ndi midzi yake. 24  Maere a 5+ anagwera fuko la Aseri+ motsatira mabanja awo. 25  Malire a gawo lawo anadutsa ku Helikati,+ Hali, Beteni, Akasafu, 26  Alameleki, Amadi ndi Misali. Analowera kumadzulo nʼkukafika ku Karimeli+ ndi ku Sihori-libanati. 27  Kenako anabwerera kulowera kumʼmawa ku Beti-dagoni, nʼkukafika ku Zebuloni ndi kumpoto kwa chigwa cha Ifita-eli. Anakafikanso ku Beti-emeki ndi ku Nehieli nʼkupitirira mpaka ku Kabulu chakumanzere. 28  Anapitirira mpaka ku Eburoni, Rehobu, Hamoni ndi Kana mpaka kumzinda waukulu wa Sidoni.+ 29  Malirewo anabwerera ku Rama, mpaka kukafika kumzinda wa Turo+ wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri. Kenako anabwereranso ku Hosa nʼkukathera kunyanja mʼchigawo cha Akizibu. 30  Anakafikanso ku Uma, Afeki+ ndi Rehobu.+ Mizinda 22 ndi midzi yake. 31  Ichi chinali cholowa cha fuko la Aseri motsatira mabanja awo+ ndipo imeneyi inali mizinda yawo ndi midzi yake. 32  Maere a 6+ anagwera ana a Nafitali motsatira mabanja awo. 33  Malire a gawo lawo anayambira ku Helefi, kumtengo waukulu wa ku Zaananimu,+ ku Adami-nekebi ndi ku Yabineeli mpaka kukafika ku Lakumu nʼkukathera ku Yorodano. 34  Malirewo anabwerera kumadzulo ku Azinotu-tabori, nʼkupitirira mpaka ku Hukoku nʼkukafika ku Zebuloni kumʼmwera. Anakafikanso ku Aseri kumadzulo ndi ku Yuda chakumʼmawa, kumtsinje wa Yorodano. 35  Mizinda yake yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri inali Zidimu, Zere, Hamati,+ Rakati, Kinereti, 36  Adama, Rama, Hazori,+ 37  Kedesi,+ Edirei, Eni-hazori, 38  Yironi, Migidala-eli, Horemu, Beti-anati ndi Beti-semesi.+ Mizinda 19 ndi midzi yake. 39  Chimenechi chinali cholowa cha fuko la Nafitali motsatira mabanja awo,+ ndipo imeneyi inali mizinda yawo ndi midzi yake. 40  Maere a 7+ anagwera fuko la Dani+ motsatira mabanja awo. 41  Malire a gawo la cholowa chawo anadutsa ku Zora,+ Esitaoli, Iri-semesi, 42  Saalabini,+ Aijaloni,+ Itila, 43  Eloni, Timuna,+ Ekironi,+ 44  Eliteke, Gebetoni,+ Baalati, 45  Yehuda, Bene-beraki, Gati-rimoni,+ 46  Me-jarikoni ndi Rakoni, nʼkukafika kumalire amene ali kutsogolo kwa Yopa.+ 47  Koma fuko la Dani gawo lawo linkawachepera,+ choncho anapita kukachita nkhondo ku Lesemu.+ Analanda mzindawo nʼkupha anthu ake ndi lupanga. Kenako anautenga nʼkuyamba kukhalamo ndipo anausintha dzina loti Lesemu nʼkuupatsa dzina loti Dani, potengera dzina la kholo lawo Dani.+ 48  Ichi chinali cholowa cha fuko la Dani motsatira mabanja awo, ndipo imeneyi inali mizinda yawo ndi midzi yake. 49  Choncho anamaliza kugawa dzikolo ndipo fuko lililonse linali ndi cholowa chake. Kenako Aisiraeli anamʼpatsa Yoswa mwana wa Nuni cholowa chake pakati pawo. 50  Molamulidwa ndi Yehova, anamʼpatsa mzinda umene anapempha wa Timinati-sera,+ mʼdera lamapiri la Efuraimu ndipo iye anamanga mzindawo nʼkumakhalamo. 51  Zimenezi zinali zigawo za cholowa chimene wansembe Eliezara, Yoswa mwana wa Nuni ndi atsogoleri a mafuko a Isiraeli anagawira anthu.+ Anagawa dzikolo pochita maere ku Silo+ pamaso pa Yehova, pakhomo la chihema chokumanako.+ Choncho anamaliza kugawa dzikolo.

Mawu a M'munsi