Yoswa 20:1-9

  • Mizinda yothawirako (1-9)

20  Kenako Yehova anauza Yoswa kuti:  “Uza Aisiraeli kuti, ‘Sankhani mizinda yothawirako+ imene ndinakuuzani kudzera mwa Mose,  kuti wopha munthu mwangozi* azithawirako pothawa wobwezera magazi.+  Azithawira kumzinda umodzi mwa mizindayi.+ Akatero azikaima pageti+ nʼkufotokoza nkhani yake kwa akulu a mzindawo. Akuluwo azimulandira nʼkumupatsa malo mumzindamo ndipo azikhala nawo limodzi.  Ngati wobwezera magazi amene akumuthamangitsa wafika, akuluwo asamapereke wopha munthuyo kwa wobwezera magaziyo, chifukwa iye sanaphe munthuyo mwadala ndipo sankadana naye.+  Munthuyo azikhala mumzindawo mpaka atakaonekera pamaso pa oweruza,*+ ndipo azikhalabe komweko mpaka mkulu wa ansembe amene alipo pa nthawiyo atafa.+ Zikatero, wopha munthuyo akhoza kubwerera nʼkukalowa mumzinda wa kwawo komwe anathawa kuja, nʼkumakhala mʼnyumba mwake.’”+  Choncho anasankha mizinda ina kuti ikhale yopatulika. Mizinda yake inali Kedesi+ ku Galileya mʼdera lamapiri la Nafitali, Sekemu+ mʼdera lamapiri la Efuraimu komanso Kiriyati-ariba,+ kutanthauza Heburoni, mʼdera lamapiri la Yuda.  Kuchigawo cha Yorodano, kumʼmawa kwa Yeriko, anasankha Bezeri,+ mʼchipululu cha mʼdera lokwererapo la fuko la Rubeni. Anasankhanso Ramoti+ ku Giliyadi mʼdera la fuko la Gadi komanso Golani+ ku Basana mʼdera la fuko la Manase.+  Imeneyi inali mizinda imene inasankhidwa kuti Aisiraeli onse ndi alendo okhala pakati pawo, azithawirako akapha munthu mwangozi,+ kuti asaphedwe ndi wobwezera magazi asanakaonekere pamaso pa oweruza.*+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “mosadziwa.”
Kapena kuti, “pamaso pa mpingo.”
Kapena kuti, “mpingo.”