Yoswa 21:1-45

  • Mizinda ya Alevi (1-42)

    • Mizinda ya ana a Aroni (9-19)

    • Mizinda ya Akohati otsala (20-26)

    • Mizinda ya Agerisoni (27-33)

    • Mizinda ya Amerari (34-40)

  • Malonjezo a Yehova anakwaniritsidwa (43-45)

21  Tsopano atsogoleri a mabanja a Alevi, anapita kwa wansembe Eliezara,+ Yoswa mwana wa Nuni ndi kwa atsogoleri a mafuko a Isiraeli.  Analankhula nawo ku Silo+ mʼdziko la Kanani, kuti: “Kudzera mwa Mose, Yehova analamula kuti tipatsidwe mizinda yoti tizikhalamo komanso malo oti tizidyetserako ziweto zathu.”+  Choncho Aisiraeli anamvera lamulo la Yehova nʼkupatsa Alevi mizindayo+ ndi malo ake odyetserako ziweto, kuchokera pa cholowa chawo.+  Atachita maere, maerewo anagwera mabanja a Akohati.+ Ndipo Alevi, omwe anali ana a wansembe Aroni, anapatsidwa mizinda 13 kuchokera mʼmafuko a Yuda,+ Simiyoni+ ndi Benjamini.+  Anachita maere ena, ndipo Akohati amene anatsala anawapatsa mizinda 10 yochokera mʼmabanja a fuko la Efuraimu,+ la Dani ndi hafu ya fuko la Manase.+  Anachitanso maere, ndipo ana a Gerisoni+ anapatsidwa mizinda 13 yochokera mʼmabanja a fuko la Isakara, la Aseri, la Nafitali ndi hafu ya fuko la Manase ku Basana.+  Anthu a mʼbanja la Merari+ anapatsidwa mizinda 12 yochokera mʼfuko la Rubeni, la Gadi ndi la Zebuloni,+ motsatira mabanja awo.  Choncho Aisiraeli anachita maere nʼkupatsa Alevi mizinda imeneyi ndi malo ake odyetserako ziweto, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula kudzera mwa Mose.+  Aisiraeli anapereka mizinda yotsatirayi kuchokera ku fuko la Yuda ndi la Simiyoni+ 10  kuti ikhale ya ana a Aroni ochokera mʼmabanja a Akohati, omwe anali Alevi, chifukwa maere oyamba anagwera iwowa. 11  Anawapatsa Kiriyati-ariba,+ kutanthauza Heburoni.+ (Ariba anali bambo wa Anaki.) Mzindawu pamodzi ndi malo ouzungulira odyetserako ziweto unali mʼdera lamapiri la Yuda. 12  Koma malo ena onse amumzindawo komanso midzi yake, anawapereka kwa Kalebe mwana wa Yefune kuti akhale ake.+ 13  Ana a wansembe Aroni anawapatsa mzinda wothawirako munthu amene wapha mnzake,+ wa Heburoni+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Anawapatsanso Libina+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 14  Yatiri+ ndi malo ake odyetserako ziweto, Esitemowa+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 15  Holoni+ ndi malo ake odyetserako ziweto, Debiri+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 16  Aini+ ndi malo ake odyetserako ziweto, Yuta+ ndi malo ake odyetserako ziweto ndiponso Beti-semesi ndi malo ake odyetserako ziweto. Panali mizinda 9 kuchokera mʼmafuko awiri amenewa. 17  Kuchokera mʼfuko la Benjamini, anawapatsa Gibiyoni+ ndi malo ake odyetserako ziweto, Geba ndi malo ake odyetserako ziweto,+ 18  Anatoti+ ndi malo ake odyetserako ziweto ndiponso Alimoni ndi malo ake odyetserako ziweto. Yonse inalipo mizinda 4. 19  Mizinda yonse imene anapereka kwa ansembe, ana a Aroni, inalipo 13 ndi malo ake odyetserako ziweto.+ 20  Mabanja a ana a Kohati, kapena kuti Alevi otsala, anapatsidwa mizinda yochokera mʼfuko la Efuraimu pambuyo pochita maere. 21  Anawapatsa mzinda wothawirako munthu amene wapha mnzake,+ wa Sekemu,+ ndi malo ake odyetserako ziweto mʼdera lamapiri la Efuraimu. Anawapatsanso Gezeri+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 22  Kibizaimu ndi malo ake odyetserako ziweto ndiponso Beti-horoni+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Yonse inalipo mizinda 4. 23  Kuchokera mʼfuko la Dani, anawapatsa Eliteke ndi malo ake odyetserako ziweto, Gibitoni ndi malo ake odyetserako ziweto, 24  Aijaloni+ ndi malo ake odyetserako ziweto ndiponso Gati-rimoni ndi malo ake odyetserako ziweto. Yonse inalipo mizinda 4. 25  Kuchokera ku hafu ya fuko la Manase, anawapatsa Taanaki+ ndi malo ake odyetserako ziweto ndiponso Gati-rimoni ndi malo ake odyetserako ziweto. Inalipo mizinda iwiri. 26  Mizinda yonse ndi malo ake odyetserako ziweto, imene mabanja a ana otsala a Kohati anapatsidwa, inalipo 10. 27  Ana a Gerisoni+ a mʼmabanja a Alevi, anapatsidwa mizinda kuchokera ku hafu ya fuko la Manase. Anawapatsa mzinda wothawirako munthu amene wapha mnzake, wa Golani+ ku Basana ndi malo ake odyetserako ziweto ndiponso Beesitera ndi malo ake odyetserako ziweto. Inalipo mizinda iwiri. 28  Kuchokera mʼfuko la Isakara,+ anawapatsa Kisioni ndi malo ake odyetserako ziweto, Daberati+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 29  Yarimuti ndi malo ake odyetserako ziweto ndiponso Eni-ganimu ndi malo ake odyetserako ziweto. Yonse inalipo mizinda 4 30  Kuchokera mʼfuko la Aseri,+ anawapatsa Misali ndi malo ake odyetserako ziweto, Abidoni ndi malo ake odyetserako ziweto, 31  Helikati+ ndi malo ake odyetserako ziweto ndiponso Rehobu+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Yonse inalipo mizinda 4. 32  Kuchokera mʼfuko la Nafitali, anawapatsa mzinda wothawirako+ munthu amene wapha mnzake, wa Kedesi+ ku Galileya ndi malo ake odyetserako ziweto. Anawapatsanso Hamoti-dori ndi malo ake odyetserako ziweto ndiponso Karitani ndi malo ake odyetserako ziweto. Yonse inalipo mizinda itatu. 33  Mizinda yonse ya Agerisoni motsatira mabanja awo inalipo 13 ndi malo ake odyetserako ziweto. 34  Kuchokera mʼfuko la Zebuloni,+ mabanja a Amerari,+ amene ndi Alevi otsala, anapatsidwa Yokineamu+ ndi malo ake odyetserako ziweto, Karita ndi malo ake odyetserako ziweto, 35  Dimena ndi malo ake odyetserako ziweto ndiponso Nahalala+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Yonse inalipo mizinda 4. 36  Kuchokera mʼfuko la Rubeni, anawapatsa Bezeri+ ndi malo ake odyetserako ziweto, Yahazi ndi malo ake odyetserako ziweto,+ 37  Kademoti ndi malo ake odyetserako ziweto ndiponso Mefaata ndi malo ake odyetserako ziweto. Yonse inalipo mizinda 4. 38  Kuchokera mʼfuko la Gadi,+ anawapatsa mzinda wothawirako munthu amene wapha mnzake, wa Ramoti ku Giliyadi+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Anawapatsanso Mahanaimu+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 39  Hesiboni+ ndi malo ake odyetserako ziweto ndiponso Yazeri+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Yonse inalipo mizinda 4. 40  Amerari omwe anatsala pa mabanja a Alevi, anapatsidwa mizinda yokwana 12 motsatira mabanja awo, pochita maere. 41  Mizinda yonse ya Alevi mʼdziko limene Aisiraeli anapatsidwa inalipo 48, pamodzi ndi malo ake odyetserako ziweto.+ 42  Mzinda uliwonse unali ndi malo odyetserako ziweto. Ndi mmene mizinda yonseyi inalili. 43  Choncho Yehova anapatsa Aisiraeli dziko lonse limene analumbira kuti adzapatsa makolo awo,+ ndipo iwo analanda dzikolo nʼkumakhalamo.+ 44  Yehova anachititsa kuti azikhala mwamtendere mʼdzikolo, mogwirizana ndi zonse zimene analumbirira makolo awo.+ Panalibe mdani aliyense amene anatha kulimbana nawo.+ Yehova anapereka adani awo onse mʼmanja mwawo.+ 45  Palibe lonjezo* limene silinakwaniritsidwe, pa malonjezo onse abwino amene Yehova analonjeza nyumba ya Isiraeli. Onse anakwaniritsidwa.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “liwu.”