Yoswa 5:1-15
5 Mafumu onse a Aamori+ amene anali kutsidya la kumadzulo kwa mtsinje wa Yorodano, ndi mafumu onse a Akanani+ amene anali mʼmbali mwa nyanja, anamva kuti Yehova anaphwetsa madzi a mtsinje wa Yorodano mpaka Aisiraeli onse atawoloka. Atangomva zimenezo, anachita mantha kwambiri,*+ moti analibenso mphamvu chifukwa choopa Aisiraeli.+
2 Pa nthawi imeneyo, Yehova anauza Yoswa kuti: “Panga timipeni tamiyala ndipo udule khungu+ amuna a Chiisiraeli kachiwiri.”
3 Choncho Yoswa anapanga timipeni tamiyala nʼkudula amuna a Chiisiraeli. Zimenezi zinachitikira ku Gibeyati-haaraloti.*+
4 Yoswa anawadula chifukwa chakuti amuna onse amene anatuluka mu Iguputo, onse otha kupita kunkhondo,* anali atafera mʼchipululu pa ulendo wochokera ku Iguputo.+
5 Anthu onse amene anachoka ku Iguputo anali odulidwa. Koma onse amene anabadwira mʼchipululu pa ulendo wochokera ku Iguputo, anali asanadulidwe.
6 Aisiraeliwo anayenda mʼchipululu zaka 40,+ mpaka anthu onse amene anatuluka mu Iguputo, amene sanamvere mawu a Yehova+ atatha kuphatikizapo amuna onse otha kupita kunkhondo. Amenewo Yehova anawalumbirira kuti sadzawalola kuona dziko+ limene Yehova analumbirira makolo awo kuti adzalipereka kwa anthu ake,*+ dziko loyenda mkaka ndi uchi.+
7 Iye analowetsa mʼdzikomo ana awo mʼmalo mwa iwowo.+ Ana amenewa Yoswa anawadula, chifukwa sanadulidwe pa nthawi imene anali pa ulendo.
8 Atamaliza kudula amuna onse, aliyense anakhalabe muhema wake pamsasapo mpaka atachira.
9 Kenako Yehova anauza Yoswa kuti: “Lero ndachititsa kuti Aiguputo asamakunyozeninso.”* Choncho malowo amawatchula kuti Giligala,*+ mpaka lero.
10 Aisiraeliwo anakhalabe ku Giligala ndipo anachita Pasika madzulo pa tsiku la 14 la mweziwo,+ mʼchipululu cha Yeriko.
11 Tsiku lotsatira, iwo anayamba kudya zokolola za mʼdzikomo. Pa tsikuli anayamba kudya mikate yopanda zofufumitsa+ ndiponso tirigu wokazinga.
12 Mana analeka kugwa pa tsikuli, pamene Aisiraeli anadya zokolola za mʼdzikomo. Kuyambira pamenepo, sipankakhalanso mana oti Aisiraeli azidya.+ Choncho chaka chimenechi nʼchimene iwo anayamba kudya zokolola za mʼdziko la Kanani.+
13 Yoswa ali pafupi ndi Yeriko, anakweza maso ake ndipo anaona mwamuna wina+ ataima patsogolo pake, atanyamula lupanga mʼmanja.+ Yoswa anamuyandikira nʼkumufunsa kuti: “Kodi uli kumbali yathu kapena kumbali ya adani athu?”
14 Munthuyo anayankha kuti: “Ayi, ndabwera chifukwa ndine kalonga* wa gulu lankhondo la Yehova.”+ Atatero, Yoswa anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake pansi, ndipo anamuuza kuti: “Lankhulani mbuyanga kwa kapolo wanu.”
15 Ndiyeno kalonga wa gulu lankhondo la Yehovayo anauza Yoswa kuti: “Vula nsapato zako, chifukwa malo amene waimawo ndi oyera.” Nthawi yomweyo, Yoswa anavula nsapato zake.+
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mitima yawo inasungunuka.”
^ Kutanthauza “Phiri la Makungu Akunsonga.”
^ Kapena kuti, “onse azaka zoyenera kukhala asilikali.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “kwa ife.”
^ Kapena kuti, “Ndachotsa chitonzo cha Iguputo pa inu.”
^ Kutanthauza “Kuchotsa.”
^ Kapena kuti, “ndine mtsogoleri.”