Yoswa 7:1-26

  • Aisiraeli anagonjetsedwa ku Ai (1-5)

  • Pemphero la Yoswa (6-9)

  • Aisiraeli anagonjetsedwa chifukwa cha tchimo (10-15)

  • Tchimo la Akani linadziwika, anaponyedwa miyala (16-26)

7  Kenako Aisiraeli anachita zinthu zosakhulupirika potenga zinthu zoyenera kuwonongedwa. Akani+ mwana wa Karami, mwana wa Zabidi, mwana wa Zera, wa fuko la Yuda, anatenga zina mwa zinthu zoyenera kuwonongedwa.+ Chifukwa cha zimenezi, Yehova anakwiyira kwambiri Aisiraeli.+  Tsopano Yoswa anatumiza amuna ena kuchokera ku Yeriko kupita ku Ai,+ pafupi ndi Beti-aveni, kumʼmawa kwa Beteli.+ Iye anawauza kuti: “Pitani mukafufuze zokhudza mzindawu.” Amunawo anapita nʼkukafufuza zokhudza mzinda wa Ai.  Amunawo atabwerako anauza Yoswa kuti: “Musachite kutumiza anthu onse kumeneko. Amuna pafupifupi 2,000 kapena 3,000, akhoza kugonjetsa Ai. Musatopetse anthu onse kuti apite kumeneko, chifukwa kuli anthu ochepa.”  Choncho amuna pafupifupi 3,000 okha anapita ku Ai, koma anathamangitsidwa ndi amuna a kumeneko.+  Ndipo amuna a Chiisiraeli 36 anaphedwa. Anthu a ku Ai anawathamangitsa kuchokera pageti kutsetsereka mpaka kukafika ku Sebarimu. Ndipo ankawapha mʼnjira yonse. Zitatero, Aisiraeli anachita mantha kwambiri.  Zimenezi zitachitika, Yoswa anangʼamba zovala zake ndipo anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake pansi patsogolo pa Likasa la Yehova, mpaka madzulo. Anachita zimenezi pamodzi ndi akulu a Isiraeli, nʼkumadzithira fumbi kumutu.  Ndipo Yoswa anati: “Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, nʼchifukwa chiyani mwalola kuti anthu ayende mtunda wonsewu mpaka kuwoloka mtsinje wa Yorodano, nʼkudzatipereka mʼmanja mwa Aamori kuti atiphe? Zikanakhala bwino tikanangokhala kutsidya lina lija la Yorodano!  Pepanitu Yehova, ndingatinso chiyani nanga, poti Isiraeli wathawa pamaso pa adani ake?  Akanani ndi anthu onse a mʼdzikoli adzamva zimenezi, ndipo adzabwera nʼkufafaniza dzina lathu padziko lapansi. Ndiye mudzateteza bwanji dzina lanu lalikulu?”+ 10  Yehova anauza Yoswa kuti: “Tadzuka iwe! Nʼchifukwa chiyani wadzigwetsa mpaka nkhope yako pansi? 11  Aisiraeli achimwa ndiponso aphwanya pangano+ limene ndinawalamula kuti alisunge. Iwo atenga zina mwa zinthu zoyenera kuwonongedwa.+ Aba+ zinthuzo ndi kuzibisa pakati pa katundu wawo.+ 12  Choncho Aisiraeli sadzathanso kulimbana ndi adani awo. Iwo azingogonja nʼkumathawa adani awo, chifukwa nawonso akhala zinthu zoyenera kuwonongedwa. Sindikhalanso nanu kufikira mutachotsa pakati panu zinthu zoyenera kuwonongedwazo.+ 13  Dzuka ndipo uyeretse anthuwa.+ Uwauze kuti, ‘Mudziyeretse pokonzekera mawa, chifukwa Yehova, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti: “Anthu inu pakati panu pali zinthu zoyenera kuwonongedwa. Simudzathanso kulimbana ndi adani anu, pokhapokha mutachotsa zinthu zoyenera kuwonongedwazo. 14  Mawa mʼmawa, mubwere mafuko onse. Fuko limene Yehova adzasankhe+ lidzabwera patsogolo. Kenako mbumba ndi mbumba, ndipo mbumba imene Yehova adzasankhe idzabwera patsogolo. Kenako banja ndi banja, ndipo banja limene Yehova adzasankhe lidzabwera patsogolo, kenako mwamuna aliyense payekhapayekha. 15  Amene apezeke ndi zinthu zoyenera kuwonongedwazo, adzatenthedwa ndi moto,+ limodzi ndi banja lake komanso zinthu zake zonse. Adzatenthedwa chifukwa waphwanya pangano+ la Yehova ndiponso wachita choipa chochititsa manyazi mu Isiraeli.”’” 16  Ndiyeno Yoswa anadzuka mʼmawa kwambiri, nʼkuuza Aisiraeli kuti afike pamaso pa Mulungu, fuko ndi fuko, ndipo fuko la Yuda linasankhidwa. 17  Kenako anauza mabanja a mʼfuko la Yuda kufika pamaso pa Mulungu, ndipo banja la Zera+ linasankhidwa. Kenako anauza banja la Zera kufika pamaso pa Mulungu, mwamuna aliyense payekhapayekha, ndipo Zabidi anasankhidwa. 18  Potsirizira pake anauza a mʼbanja la Zabidi kufika pamaso pa Mulungu, mwamuna aliyense payekhapayekha. Ndipo Akani mwana wa Karami, mwana wa Zabidi, mwana wa Zera, wa fuko la Yuda, anasankhidwa.+ 19  Tsopano Yoswa anauza Akani kuti: “Mwana wanga, chonde, lemekeza Yehova Mulungu wa Isiraeli, ulula kwa iye. Tandiuza chonde, wachita chiyani? Usandibisire.” 20  Akani anayankha Yoswa kuti: “Ndithudi, ineyo ndi amene ndachimwira Yehova Mulungu wa Isiraeli. Zimene ndinachita ndi izi: 21  Pakati pa zinthu zoyenera kuwonongedwa ndinaonapo chovala chokongola komanso chamtengo wapatali cha ku Sinara,+ masekeli* a siliva 200 komanso mtanda umodzi wa golide wolemera masekeli 50. Nditaziona ndinazisirira ndipo ndinazitenga. Panopa chovalacho ndi ndalamazo ndazikumbira pansi, pakati pa tenti yanga, ndipo ndalamazo zili pansi pa chovalacho.” 22  Nthawi yomweyo Yoswa anatuma anthu, amene anathamangira kutentiko. Iwo anachipezadi chovalacho mʼhema wake, ndipo ndalama zinali pansi pake. 23  Anthuwo anatenga zinthuzo muhemayo ndipo anabwera nazo kwa Yoswa ndi Aisiraeli onse nʼkuziika pansi, pamaso pa Yehova. 24  Kenako Yoswa ndi Aisiraeli onse anatenga Akani+ mwana wa Zera, limodzi ndi siliva uja, chovala chamtengo wapatali chija, mtanda wa golide uja,+ komanso ana ake aamuna ndi aakazi, ngʼombe zake, abulu, nkhosa, ndiponso hema wake, ndi chilichonse chomwe chinali chake, nʼkupita nawo kuchigwa cha Akori.+ 25  Ndiyeno Yoswa anati: “Nʼchifukwa chiyani watibweretsera tsoka?*+ Lero Yehova akubweretsera iweyo tsoka.” Atatero, Aisiraeli onse anayamba kuwaponya miyala+ anthuwo ndipo kenako anawatentha ndi moto.+ Umu ndi mmene anawaphera, anawaponya miyala. 26  Pambuyo pake, anaunjika mulu waukulu wa miyala pa iye. Muluwo ulipo mpaka lero. Zitatero, mkwiyo waukulu wa Yehova unatha.+ Nʼchifukwa chake malowo amatchedwa chigwa cha Akori* mpaka lero.

Mawu a M'munsi

Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4. Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “watibweretsera mavuto; wachititsa kuti tinyanyalidwe.”
Kutanthauza, “Tsoka; Kunyanyalidwa.”