Yoswa 8:1-35

  • Yoswa anatumiza anthu oti akabisalire anthu a ku Ai (1-13)

  • Mzinda wa Ai unagonjetsedwa (14-29)

  • Chilamulo chinawerengedwa paphiri la Ebala (30-35)

8  Kenako Yehova anauza Yoswa kuti: “Usaope kapena kuchita mantha.+ Tenga amuna onse ankhondo ndipo upite kukamenyana ndi mzinda wa Ai. Dziwa kuti mfumu ya Ai ndaipereka kwa iwe limodzi ndi anthu ake, mzinda wake komanso dera lake lonse.+  Ukachitire mzinda wa Ai ndi mfumu yake zimene unachitira mzinda wa Yeriko ndi mfumu yake.+ Koma katundu ndi ziweto zamumzindawo mukatenge zikhale zanu. Usankhe amuna ena oti akabisale kumbuyo kwa mzindawo.”  Choncho Yoswa ndi amuna onse ankhondo ananyamuka kupita kukamenyana ndi mzinda wa Ai. Yoswa anasankha asilikali amphamvu ndi olimba mtima okwanira 30,000, nʼkuwatumiza usiku.  Anawalamula kuti: “Inu mukabisale kumbuyo kwa mzindawo. Musakakhale patali kwambiri ndi mzindawo, ndipo nonsenu mukakhale okonzeka.  Koma ine ndi onse amene ndikakhale nawo, tikafika pafupi kwambiri ndi mzindawo. Iwo akakatuluka kuti adzamenyane nafe ngati poyamba paja,+ tikayamba kuthawa.  Akakaona kuti tikuthawa, akatithamangitsa. Tikapitiriza kuthawa kuti tikawatulutse mpaka akafike kutali ndi mzindawo, chifukwa akaganiza kuti, ‘Akuthawa ngati poyamba paja.’+  Zikakatero, inu mukavumbuluke nʼkulanda mzindawo. Yehova Mulungu wanu adzaupereka ndithu mʼmanja mwanu.  Ndipo mukakangolanda mzindawo, mukauyatse moto.+ Mukachite zimenezi mogwirizana ndi mawu a Yehova. Ndakulamulani kuti mukachite zimenezi.”  Kenako Yoswa anatumiza amunawo ndipo anapita kukabisala. Iwo anakabisala pakati pa Beteli ndi Ai, kumadzulo kwa Ai. Koma usiku umenewo Yoswa anagona limodzi ndi asilikali amene anali nawo. 10  Yoswa anadzuka mʼmawa kwambiri nʼkusonkhanitsa asilikaliwo. Atatero ananyamuka ndipo iye limodzi ndi akulu a Isiraeli anatsogolera asilikaliwo ku Ai. 11  Asilikali onse+ amene anali ndi Yoswa anayenda nʼkukafika pafupi ndi mzindawo, kutsogolo kwake. Atafika anamanga msasa kumpoto kwa Ai, ndipo pakati pa iwo ndi mzindawo panali chigwa. 12  Pa nthawiyi anali atatumiza amuna pafupifupi 5,000 ndipo anali atabisala+ pakati pa Beteli+ ndi Ai, kumadzulo kwa mzinda wa Ai. 13  Choncho asilikali ambiri anamanga msasa wawo kumpoto kwa mzindawo,+ ndipo ochepa anamanga kumadzulo kwa mzindawo.+ Usikuwo Yoswa ananyamuka nʼkupita pakati pa chigwa chija. 14  Tsopano mfumu ya Ai itaona zimenezo, nthawi yomweyo mfumuyo ndi amuna amumzindawo anakonzeka kuti akamenyane ndi Aisiraeli. Anadzuka mʼmamawa kukakumana nawo pamalo ena pomwe ankatha kuona bwino chigwa cha mʼchipululu. Koma mfumuyo sinadziwe kuti asilikali ena anali atabisala kumbuyo kwa mzindawo. 15  Amuna a ku Ai atawaukira, Yoswa ndi Aisiraeli onse anayamba kuthawa kudzera njira yolowera kuchipululu.+ 16  Zitatero, anthu onse amumzindawo anaitanidwa kuti akathamangitse Aisiraeli. Anthuwo anathamangitsa Aisiraeliwo ndi Yoswa, mpaka anafika kutali ndi mzindawo. 17  Panalibe mwamuna ndi mmodzi yemwe amene anatsala ku Ai ndi ku Beteli. Onse anapita kukathamangitsa Aisiraeli, ndipo mageti a mzindawo anangowasiya osatseka. 18  Tsopano Yehova anauza Yoswa kuti: “Loza mzinda wa Ai ndi nthungo* imene ili mʼmanja mwako,+ chifukwa ndiupereka mʼmanja mwako.”+ Choncho Yoswa analoza mzindawo ndi nthungo imene inali mʼmanja mwake. 19  Atangouloza, asilikali amene anabisala aja anavumbuluka nʼkuthamangira kumzindawo ndipo anaulanda. Nthawi yomweyo anauyatsa moto.+ 20  Amuna a ku Ai atatembenuka anangoona utsi uli tolo mumzindawo, ndipo analibiretu mphamvu zoti nʼkuthawira kulikonse. Kenako asilikali a Chiisiraeli amene ankathawira kuchipululu aja, anatembenukira amuna a ku Aiwo. 21  Yoswa ndi Aisiraeli onse amene anali naye ataona kuti asilikali omwe anabisala aja alanda mzindawo, ndiponso ataona utsi mumzindawo, anatembenukira amuna a ku Ai nʼkuyamba kuwapha. 22  Ndiyeno asilikali amene analanda mzinda aja anatuluka mumzindamo kudzamenyana ndi amuna a ku Aiwo. Choncho amuna a ku Ai anali pakati pa Aisiraeli, ena mbali ino, ena mbali inayo. Aisiraeliwo anapha amuna a ku Ai, moti palibe amene anatsala kapena kuthawa.+ 23  Koma mfumu ya ku Ai+ anaigwira nʼkupita nayo kwa Yoswa. 24  Aisiraeli anapha ndi lupanga amuna onse ankhondo a ku Ai kuchipululu kumene anthu a ku Aiwo anawathamangitsirako. Atatero, Aisiraeliwo anabwerera ku Ai nʼkukapha ndi lupanga ena onse otsala. 25  Anthu onse amene anaphedwa tsikulo, amuna ndi akazi, anakwana 12,000, anthu onse a ku Ai. 26  Ndipo Yoswa sanatsitse mkono wake umene anagwiritsa ntchito poloza mzindawo ndi nthungo+ mpaka anthu onse a ku Ai ataphedwa.+ 27  Koma Aisiraeliwo anatenga ziweto ndi katundu wamumzindawo nʼkukhala zawo, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Yoswa.+ 28  Ndiyeno Yoswa anatentha mzinda wa Ai nʼkuusiya uli bwinja loti lidzakhala choncho mpaka kalekale,+ ndipo lilipobe mpaka lero. 29  Mfumu ya Ai anaipachika pamtengo mpaka madzulo. Koma dzuwa litatsala pangʼono kulowa, Yoswa analamula kuti achotse mtembo wa mfumuyo pamtengopo.+ Atauchotsa anakauponya pageti la mzindawo nʼkuunjikapo mulu waukulu wa miyala, ndipo muluwo ulipo mpaka lero. 30  Nthawi imeneyi ndi imene Yoswa anamangira Yehova Mulungu wa Isiraeli guwa lansembe pa Phiri la Ebala.+ 31  Anamanga guwalo mogwirizana ndi zimene Mose mtumiki wa Yehova analamula Aisiraeli, mogwirizananso ndi zimene zinalembedwa mʼbuku la Chilamulo+ cha Mose kuti: “Guwa lansembe la miyala yathunthu ndiponso yosasema ndi chipangizo chachitsulo.”+ Ndipo iwo anaperekapo kwa Yehova nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano.+ 32  Kenako Yoswa analemba pamiyala Chilamulo+ chimene Mose analembera Aisiraeli.+ 33  Aisiraeli onse, atsogoleri awo, akapitawo awo, ndi oweruza awo anasonkhanitsidwa pamodzi. Panalinso alendo ndi nzika.+ Ena anaima mbali iyi ya Likasa, ena anaima mbali inayo, pamaso pa Alevi omwe anali ansembe amene ananyamula likasa la pangano la Yehova. Hafu ya anthuwo inaima mʼphiri la Gerizimu, ndipo hafu ina inaima mʼphiri la Ebala,+ (ngati mmene Mose mtumiki wa Yehova analamulira),+ kuti Aisiraeliwo adalitsidwe. 34  Zimenezi zitatha, Yoswa anawerenga mokweza mawu onse a Chilamulo,+ madalitso+ ndi matemberero,+ mogwirizana ndi zonse zolembedwa mʼbuku la Chilamulo. 35  Panalibe ngakhale mawu amodzi pa mawu onse amene Mose analamula, amene Yoswa sanawawerenge mokweza pamaso pa mpingo wonse wa Aisiraeli.+ Panalinso akazi ndi ana, komanso alendo+ okhala pakati pawo.+

Mawu a M'munsi

Tikati “nthungo” tikutanthauza mkondo waungʼono, wopepukirako.