Yoswa 9:1-27

  • Agibiyoni ochenjera anapempha mgwirizano (1-15)

  • Bodza la Agibiyoni linadziwika (16-21)

  • Agibiyoni anakhala otola nkhuni ndi kutunga madzi (22-27)

9  Mafumu onse amene anali kumadzulo kwa Yorodano+ anamva zimene zinachitika. Amenewa anali mafumu a Ahiti, Aamori, Akanani, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi.+ Iwo ankakhala kudera lamapiri, ku Sefela ndiponso mʼmbali monse mwa Nyanja Yaikulu*+ komanso pafupi ndi Lebanoni. Mafumuwa atangomva zimene zinachitikazo,  anapanga mgwirizano kuti amenyane ndi Yoswa ndi Isiraeli.+  Nawonso anthu a ku Gibiyoni+ anamva zimene Yoswa anachita ku Yeriko+ ndi ku Ai.+  Choncho anachita zinthu mwanzeru. Anaika chakudya mʼmatumba akutha nʼkukweza pa abulu. Ananyamulanso vinyo mʼmatumba achikopa akutha, atawasoka mongʼambika.  Anavalanso nsapato zakutha atazisokasoka ndiponso zovala zakutha. Mkate wonse umene anatenga unali wouma ndipo unkangoyoyoka.  Kenako anapita kwa Yoswa kumsasa ku Giligala,+ ndipo anamuuza iyeyo ndi amuna a Chiisiraeli kuti: “Tachokera kudziko lakutali kwambiri. Chonde muchite nafe pangano.”  Koma amuna a Chiisiraeli anayankha Ahiviwo+ kuti: “Mwina mumakhala chakonkuno. Ndiye tingachite nanu bwanji pangano?”+  Iwo anayankha Yoswa kuti: “Ndife akapolo* anu.” Ndiyeno Yoswa anawafunsa kuti: “Koma ndinu ndani, ndipo mwachokera kuti?”  Iwo anamuyankha kuti: “Akapolo anufe tachokera kudziko lakutali kwambiri.+ Tabwera chifukwa tamva za dzina la Mulungu wanu, Yehova. Tamva mbiri yake ndi zonse zimene anachita ku Iguputo.+ 10  Tamvanso zonse zimene anachita kwa mafumu awiri a Aamori kutsidya lina* la Yorodano, omwe ndi Mfumu Sihoni+ ya ku Hesiboni ndi Mfumu Ogi+ ya ku Basana, imene inali ku Asitaroti. 11  Choncho akulu akwathu ndi anthu onse amʼdziko lathu anatiuza kuti, ‘Tengani chakudya cha pa ulendo ndipo mupite kukakumana nawo. Mukawauze kuti: “Ife ndife akapolo anu.+ Chonde muchite nafe pangano.”’+ 12  Pamene tinkanyamuka kubwera kuno, mkate wathuwu unali wotentha. Koma mutha kuona kuti wauma ndipo ukungoyoyoka.+ 13  Ndipo matumba achikopa a vinyowa anali atsopano pamene timathiramo vinyo, koma tsopano angʼambika.+ Onaninso zovala ndi nsapato zathuzi, zangʼambika chifukwa cha kutalika kwa ulendo.” 14  Ndiyeno amuna a Chiisiraeli anatengako zakudyazo nʼkuziyangʼanitsitsa, koma sanafunsire kwa Yehova.+ 15  Choncho Yoswa anagwirizana nawo za mtendere,+ ndipo anachita nawo pangano kuti sawapha. Zitatero, atsogoleri a Isiraeli analumbira kwa anthuwo.+ 16  Koma patapita masiku atatu atachita nawo panganolo, anamva kuti anthuwo ankakhala pafupi, mʼdera lomwelo. 17  Aisiraeliwo ananyamuka nʼkukafika kumizinda ya anthuwo pa tsiku lachitatu. Mizindayo inali Gibiyoni,+ Kefira, Beeroti ndi Kiriyati-yearimu.+ 18  Koma Aisiraeli sanawaphe anthuwo chifukwa atsogoleri awo anali atalumbirira anthuwo mʼdzina la Yehova,+ Mulungu wa Isiraeli. Choncho gulu lonse linayamba kungʼungʼudza motsutsana ndi atsogoleriwo. 19  Ndiyeno atsogoleri onse anauza gululo kuti: “Ife tinawalumbirira mʼdzina la Yehova Mulungu wa Isiraeli, ndiye sitingawaphe. 20  Tipanga chonchi: Tiwasiya kuti akhale ndi moyo, kuti Mulungu asatikwiyire popeza tinawalumbirira.”+ 21  Atsogoleriwo ananenanso kuti: “Asaphedwe, koma azitola nkhuni ndiponso kutungira madzi gulu lonse la Aisiraeli.” Izi ndi zimene atsogoleriwo anawalonjeza. 22  Kenako Yoswa anaitana anthuwo nʼkuwafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani munatipusitsa nʼkumanena kuti ‘Timakhala kutali kwambiri ndi inu,’ chonsecho mumakhala pafupi?+ 23  Tsopano mukhala anthu otembereredwa.+ Mukhala akapolo ndipo muzitola nkhuni ndi kutungira madzi nyumba ya Mulungu wanga.” 24  Anthuwo anayankha Yoswa kuti: “Akapolo anufe tinauzidwa mosapita mʼmbali kuti Yehova Mulungu wanu analamula mtumiki wake Mose kuti akupatseni dziko lonseli ndiponso muphe anthu onse okhalamo.+ Choncho tinachita mantha kuti mutipha.+ Nʼchifukwa chake tinachita zimenezi.+ 25  Tsopano tili mʼmanja mwanu. Tichiteni chilichonse chimene mukuona kuti nʼchabwino ndi choyenera.” 26  Yoswa anavomereza zimenezo. Anawalanditsa kwa Aisiraeli ndipo sanawaphe. 27  Koma pa tsikuli, Yoswa anawalamula kuti azitunga madzi ndi kutola nkhuni za Aisiraeli onse+ ndiponso zapaguwa lansembe la Yehova, pamalo alionse amene Mulungu wasankha.+ Iwo akhala akuchita zimenezi mpaka lero.+

Mawu a M'munsi

Imeneyi ndi nyanja ya Mediterranean.
Kapena kuti, “Ndife antchito.”
Imeneyi ndi mbali yakumʼmawa.