Yoweli 1:1-20

  • Mliri woopsa wa ziwala ndi dzombe (1-14)

  • “Tsiku la Yehova lili pafupi” (15-20)

    • Mneneri anaitana Yehova (19, 20)

1  Yehova analankhula kudzera mwa Yoweli* mwana wa Petueli kuti:   “Tamverani inu akulu,Ndipo tcherani khutu inu nonse okhala mʼdzikoli. Kodi zinthu ngati izi zinachitikapo mʼmasiku anu,Kapena mʼmasiku a makolo anu?+   Fotokozerani ana anu zinthu zimenezi.Nawonso ana anu adzafotokozere ana awo,Ndipo ana awowo adzafotokozerenso mʼbadwo wotsatira.   Zinthu zimene ziwala zowononga zinasiya zinadyedwa ndi dzombe lambirimbiri.+Zimene dzombelo linasiya zinadyedwa ndi ana a dzombe opanda mapiko.Ndipo zimene ana a dzombe opanda mapiko anasiya zinadyedwa ndi dzombe losakaza.+   Dzukani zidakwa inu+ ndipo lirani. Fuulani inu nonse okonda vinyo,Chifukwa vinyo wotsekemera wachotsedwa pakamwa panu.+   Pali mtundu umene walowa mʼdziko langa, wamphamvu ndiponso wa anthu osawerengeka.+ Mano ndiponso nsagwadwa zawo zili ngati za mikango.+   Iwo awononga mtengo wanga wa mpesa ndipo asandutsa mtengo wanga wa mkuyu kukhala chitsa.Nthambi za mitengoyi azichotsa makungwa nʼkuzitaya.Mphukira zake azichotsanso makungwa.   Lirani ngati mmene amalirira namwali amene wavala chiguduli,Polirira mwamuna amene amafuna kumukwatira.   Nsembe zambewu+ ndi nsembe zachakumwa+ sizikupezekanso mʼnyumba ya Yehova.Ansembe omwe ndi atumiki a Yehova, akulira. 10  Munda wawonongedwa ndipo nthaka ikulira.+Mbewu zawonongedwa, vinyo watsopano watha ndipo mafuta sakupezekanso.+ 11  Alimi asokonezeka ndipo osamalira minda ya mpesa akulira mofuula,Chifukwa cha tirigu ndi barele.Popeza zokolola zamʼmunda zawonongeka. 12  Mtengo wa mpesa wauma,Mtengo wa mkuyu wafota. Mtengo wa makangaza,* wa kanjedza ndiponso wa maapozi, yonse yauma.Mitengo yonse yamʼmunda yauma.+Chifukwa chisangalalo cha anthu chasanduka manyazi. 13  Valani ziguduli ndipo lirani* inu ansembe.Lirani mofuula, inu atumiki apaguwa lansembe.+ Lowani, valani ziguduli usiku wonse inu atumiki a Mulungu wanga,Chifukwa nsembe yambewu+ ndi nsembe yachakumwa+ sizikubweranso mʼnyumba ya Mulungu wanu. 14  Lengezani nthawi yosala kudya. Itanitsani msonkhano wapadera.+ Sonkhanitsani akulu ndi anthu onse okhala mʼdzikoli,Kuti akumane kunyumba ya Yehova Mulungu wanu+ ndipo alirire Yehova kuti awathandize. 15  Tsikulo lidzakhala lochititsa mantha. Tsiku la Yehova lili pafupi.+Lidzafika ngati chiwonongeko chochokera kwa Wamphamvuyonse. 16  Kodi chakudya sichinachotsedwe ife tikuona?Kodi kusangalala sikunachotsedwe mʼnyumba ya Mulungu wathu? 17  Mbewu* zawonongeka mafosholo ali pamwamba pake. Nyumba zosungiramo zinthu zawonongedwa. Nkhokwe zapasulidwa chifukwa mbewu zauma. 18  Ngakhale ziweto zikubuula. Magulu a ngʼombe akuyendayenda mosokonezeka chifukwa palibe msipu. Ndiponso magulu a nkhosa alangidwa. 19  Ine ndidzaitana inu Yehova,+Chifukwa moto wawononga malo onse komwe kuli tchire lodyetserako ziweto,Ndipo malawi amoto atentha mitengo yonse yakutchire. 20  Ngakhale zilombo zakutchire zikufuna kuti muzithandize,Chifukwa mitsinje ya madzi yauma,Ndipo moto wawononga malo onse komwe kuli tchire lodyetserako ziweto.”

Mawu a M'munsi

Kutanthauza “Yehova ndi Mulungu.”
“Makangaza” ndi mtundu wa chipatso. Ena amati chimanga chachizungu.
Kapena kuti, “dzimenyeni pachifuwa.”
Mabaibulo ena amati, “Nkhuyu zouma.”