Yoweli 2:1-32

  • Tsiku la Yehova komanso gulu lalikulu la asilikali ake (1-11)

  • Anawauza kuti abwerere kwa Yehova (12-17)

    • “Ngʼambani mitima yanu” (13)

  • Yehova anayankha anthu ake (18-32)

    • “Ndidzapereka mzimu wanga”  (28)

    • Zodabwitsa kumwamba ndi padziko lapansi (30)

    • Oitana pa dzina la Yehova adzapulumuka (32)

2  “Lizani lipenga mu Ziyoni.+ Lengezani mʼphiri langa loyera kuti kukubwera nkhondo. Anthu onse okhala mʼdzikoli anjenjemere,Chifukwa tsiku la Yehova likubwera+ ndipo lili pafupi.   Limeneli ndi tsiku lamdima ndi lachisoni,+Tsiku lamitambo ndi lamdima wandiweyani.+Tsikuli lili ngati mmene kuwala kwa mʼbandakucha kumaonekera pamwamba pa mapiri. Pali mtundu wa anthu ambiri ndiponso amphamvu.+Kuyambira kalekale, palibenso mtundu wina womwe ungafanane nawo,Ndipo sikudzakhalanso mtundu wina wofanana nawo,Kumibadwomibadwo.   Kutsogolo kwawo moto ukuwononga,Ndipo kumbuyo kwawo malawi amoto akusakaza.+ Dziko lomwe lili patsogolo pawo lili ngati munda wa Edeni,+Koma kumbuyo kwawo kuli chipululu,Ndipo palibe chilichonse chingapulumuke.   Mtundu wa anthuwo umaoneka ngati mahatchi,*Ndipo amathamanga ngati mahatchi ankhondo.+   Amadumphadumpha ndipo amachita mkokomo ngati magaleta oyenda pamwamba pa mapiri,+Ndiponso ngati moto walawilawi umene ukutentha mapesi. Ali ngati anthu amphamvu omwe ayalana pokonzekera kumenya nkhondo.+   Anthu adzakhala ndi nkhawa chifukwa cha mtunduwo. Nkhope zawo zonse zidzakhala zamantha.   Amathamanga ngati asilikali.Amakwera khoma ngati asilikali.Aliyense amayenda mʼnjira yake,Ndipo saphonya njira zawo.   Iwo sakankhanakankhana.Aliyense amayenda mʼnjira yake. Wina akalasidwa nʼkugwa,Enawo sabwerera mʼmbuyo.   Iwo amathamangira mʼmizinda ndipo amathamanga pakhoma la mpanda. Amakwera nyumba ndipo amalowera pawindo ngati mbala. 10  Dzombelo likamayenda, dziko limanjenjemera ndipo kumwamba kumagwedezeka. Dzuwa ndi mwezi zada,+Ndipo nyenyezi zasiya kuwala. 11  Yehova adzawalankhula asilikali ake mokweza+ chifukwa anthu amumsasa wake ndi ambiri.+ Amene akukwaniritsa mawu ake ndi wamphamvu.Tsiku la Yehova ndi lalikulu komanso lochititsa mantha.+ Ndani angalimbe pa tsiku limeneli?”+ 12  Yehova wanenanso kuti, “Tsopano bwererani kwa ine ndi mtima wonse.+Salani kudya,+ lirani momvetsa chisoni ndiponso mokweza. 13  Ngʼambani mitima yanu,+ osati zovala zanu,+Ndipo bwererani kwa Yehova Mulungu wanu,Chifukwa iye ndi wachifundo, wokoma mtima, wosakwiya msanga+ ndiponso wachikondi chokhulupirika chochuluka.+Iye adzasintha maganizo okubweretserani tsoka. 14  Ndani akudziwa kuti mwina adzasintha maganizo,+Ndipo adzakusiyirani madalitso,Nsembe yambewu ndi nsembe yachakumwa kuti mupereke kwa Yehova Mulungu wanu? 15  Lizani lipenga mu Ziyoni. Lengezani za nthawi yosala kudya. Itanitsani msonkhano wapadera.+ 16  Sonkhanitsani anthu ndipo muyeretse mpingo.+ Sonkhanitsani amuna achikulire,* ana komanso makanda.+ Mkwati atuluke mʼchipinda chake ndipo nayenso mkwatibwi atuluke mʼchipinda chake. 17  Pakati pa khonde ndi guwa la nsembe,+Ansembe omwe ndi atumiki a Yehova alire nʼkumanena kuti: ‘Inu Yehova, mverani chisoni anthu anu,Ndipo musachititse manyazi cholowa chanu,Kuti anthu a mitundu ina awalamulire. Anthu a mitundu ina asanene kuti: “Kodi Mulungu wawo ali kuti?”’+ 18  Ndiyeno Yehova adzachitira nsanje dziko lake,Ndipo adzachitira chifundo anthu ake.+ 19  Yehova adzayankha anthu ake kuti: ‘Ndikukutumizirani mbewu, vinyo watsopano ndi mafuta.Anthu inu mudzakhuta.+Sindidzachititsanso kuti muzinyozedwa pakati pa anthu a mitundu ina.+ 20  Mdani wakumpoto ndidzamuthamangitsira kutali ndi inu.Ndidzamuthamangitsira kudziko louma komanso lopanda anthu,Nkhope yake itayangʼana kunyanja yakumʼmawa,*Nkhongo yake italoza kunyanja yakumadzulo.* Fungo lake lonunkha lidzamveka,Ndipo fungo lake loipalo lidzafalikira mʼdziko lonselo,+Chifukwa Mulungu adzachita zinthu zazikulu.’ 21  Usachite mantha iwe dziko. Sangalala chifukwa Yehova adzachita zinthu zazikulu. 22  Inu zilombo zakutchire musachite mantha,Chifukwa malo odyetserako ziweto kutchire adzamera msipu wobiriwira.+Mitengo nayonso idzabereka zipatso.+Mtengo wa mkuyu ndi mtengo wa mpesa udzabereka zipatso zambiri.+ 23  Inu ana aamuna a Ziyoni sangalalani chifukwa cha Yehova Mulungu wanu.+Iye adzakupatsani mvula yoyambirira pa mlingo woyenera,Ndipo adzakugwetserani mvula yamvumbi,Mvula yoyambirira ndi mvula yomaliza, ngati mmene zinalili poyamba.+ 24  Malo opunthira mbewu adzadzaza ndi mbewu,Ndipo malo opangira vinyo komanso mafuta adzasefukira.+ 25  Ndidzakubwezerani mbewu za zaka zonseZimene dzombe, ana a dzombe opanda mapiko komanso dzombe losakaza zinadya.Limeneli ndi gulu langa lankhondo limene ndinakutumizirani.+ 26  Mudzadya nʼkukhuta,+Ndipo mudzatamanda dzina la Yehova Mulungu wanu,+Amene wakuchitirani zodabwitsa.Anthu anga sadzachitanso manyazi mpaka kalekale.+ 27  Mudzadziwa kuti ine ndili pakati pa Isiraeli,+Komanso kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu+ ndipo palibenso wina. Anthu anga sadzachitanso manyazi mpaka kalekale. 28  Zimenezi zikadzachitika ndidzapereka* mzimu wanga+ kwa chamoyo chilichonse,Ndipo ana anu aamuna ndi ana anu aakazi adzalosera.Amuna achikulire adzalota maloto,Ndipo anyamata adzaona masomphenya.+ 29  Ngakhale akapolo anga aamuna ndi aakazi,Ndidzawapatsa mzimu wanga mʼmasiku amenewo. 30  Ndidzachita zodabwitsa kumwamba ndi padziko lapansi.Padzakhala magazi, moto ndi utsi wambiri wokwera mʼmwamba.+ 31  Dzuwa lidzasanduka mdima ndipo mwezi udzasanduka magazi,+Tsiku lalikulu ndi lochititsa mantha la Yehova lisanafike.+ 32  Ndipo aliyense woitana pa dzina la Yehova adzapulumuka,+Chifukwa mʼphiri la Ziyoni ndiponso mu Yerusalemu mudzakhala anthu opulumuka+ ngati mmene Yehova ananenera.Anthu opulumuka amene Yehova akuwaitana.”

Mawu a M'munsi

Ena amati “mahosi.”
Kapena kuti, “akulu.”
Kutanthauza “Nyanja Yakufa.”
Kutanthauza “Nyanja ya Mediterranean.”
Kapena kuti, “ndidzatsanulira.”