Yoweli 3:1-21

  • Yehova adzaweruza mitundu yonse ya anthu (1-17)

    • Chigwa cha Yehosafati (2, 12)

    • Chigwa choweruzira (14)

    • Yehova, malo othawirako a Isiraeli (16)

  • Yehova adzadalitsa anthu ake (18-21)

3  “Mʼmasiku amenewo ndiponso pa nthawiyo,Ndikadzabwezeretsa anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu amene anagwidwa ukapolo,+   Ndidzasonkhanitsanso anthu a mitundu yonse,Nʼkuwabweretsa mʼchigwa cha Yehosafati.* Ndipo ndidzawaweruza kumeneko,+Mʼmalo mwa anthu anga ndiponso cholowa changa, Isiraeli.Chifukwa anamwaza Aisiraeli pakati pa anthu a mitundu ina,Ndiponso anagawana dziko langa.+   Ankachitira maere anthu anga.+Ankagulitsa mnyamata kuti alipire hule,Ndipo ankagulitsa mtsikana kuti agule vinyo woti amwe.   Komanso kodi ndakulakwira chiyaniIwe Turo ndi Sidoni ndiponso nonse amʼchigawo cha Filisitiya? Kodi mukundichitira zimenezi pondibwezera zimene ndinachita? Ngati mukundibwezera,Ine ndidzakubwezerani mwamsanga ndiponso mofulumira zimene mwandichitirazo.+   Chifukwa chakuti mwatenga siliva ndi golide wanga,+Ndipo mwabweretsa zinthu zanga zabwino kwambiri mu akachisi anu,   Komanso mwagulitsa anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu kwa Agiriki,+Kuti muwapititse kutali ndi dziko lawo,   Choncho ndiwatenga kuti achoke kumalo amene munawagulitsa,+Ndipo ndikubwezerani zimene munachita.   Ndidzagulitsa ana anu aamuna ndi aakazi kwa anthu a ku Yuda.+Iwo adzawagulitsa kwa anthu a ku Sheba, mtundu wa anthu akutali.Ine Yehova ndanena zimenezi.   Lengezani kwa anthu a mitundu ina+ kuti: ‘Konzekerani nkhondo! Konzekeretsani amuna amphamvu! Asilikali onse abwere nʼkuukira!+ 10  Sulani makasu anu a pulawo kuti akhale malupanga, ndiponso zida zanu zosadzira mitengo kuti zikhale mikondo. Munthu wofooka anene kuti: “Ndine wamphamvu.” 11  Inu anthu a mitundu yotizungulira, bwerani mudzathandize ndipo nonse musonkhane.’”+ Inu Yehova, bweretsani asilikali anu kumalo amenewo. 12  “Mitundu ya anthu inyamuke nʼkubwera kuchigwa cha Yehosafati,Chifukwa ndidzakhala kumeneko kuti ndiweruze anthu a mitundu yozungulira.+ 13  Yambani kumweta ndi chikwakwa, chifukwa zokolola zacha. Bwerani nʼkuyamba kuponda chifukwa moponderamo mphesa mwadzaza.+ Malo ogweramo vinyo asefukira, chifukwa zoipa zawo zachuluka kwambiri. 14  Anthu ambirimbiri ali mʼchigwa choweruzira mlandu,Chifukwa tsiku la Yehova layandikira mʼchigwa choweruzira mlandu.+ 15  Dzuwa ndi mwezi zidzachita mdima,Ndipo nyenyezi zidzasiya kuwala. 16  Yehova adzabangula kuchokera ku Ziyoni,Ndipo adzalankhula mokweza ali ku Yerusalemu. Kumwamba ndi dziko lapansi zidzagwedezeka.Koma Yehova adzakhala malo othawirako a anthu ake,+Malo achitetezo champhamvu kwa Aisiraeli. 17  Ndipo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndimakhala mu Ziyoni, phiri langa lopatulika.+ Yerusalemu adzakhala malo opatulika,+Ndipo anthu achilendo* sadzadutsanso mmenemo.+ 18  Nthawi imeneyo mʼmapiri akuluakulu mudzatuluka vinyo wotsekemera.+Mʼmapiri angʼonoangʼono mudzayenda mkaka.Ndipo mʼmitsinje yonse ya Yuda mudzayenda madzi. Kasupe adzatuluka mʼnyumba ya Yehova,+Ndipo adzathirira chigwa cha Mitengo ya Mthethe. 19  Koma Iguputo adzasanduka bwinja,+Ndipo Edomu adzakhala chipululu chopanda kanthu.+Chifukwa cha nkhanza zimene anachitira anthu a ku Yuda,+Ndiponso chifukwa chokhetsa magazi a anthu osalakwa mʼdziko la Yudalo.+ 20  Koma ku Yuda kuzidzakhala anthu nthawi zonse,Ndipo ku Yerusalemu kudzakhala anthu mibadwomibadwo.+ 21  Magazi awo amene anali ndi mlandu adzakhala opanda mlandu,+Ndipo ine Yehova ndizidzakhala ku Ziyoni.”+

Mawu a M'munsi

Kutanthauza “Yehova ndi Woweruza.”
Kapena kuti, “ochokera kwina.”