Zefaniya 1:1-18

  • Tsiku la chiweruzo la Yehova lili pafupi (1-18)

    • Tsiku la Yehova likubwera mofulumira (14)

    • Siliva ndi golide sizingapulumutse munthu (18)

1  Mʼmasiku a Yosiya+ mwana wa Amoni+ mfumu ya Yuda, Yehova analankhula kudzera mwa Zefaniya* mwana wa Kusa, mwana wa Gedaliya, mwana wa Amariya, mwana wa Hezekiya. Iye anati:   “Ine ndidzasesa chilichonse chimene chili panthaka,” watero Yehova.+   “Ndidzasesa anthu ndi nyama. Ndidzasesa mbalame zamumlengalenga ndiponso nsomba zamʼnyanja.+Ndidzasesanso zopunthwitsa*+ pamodzi ndi anthu oipa,Ndipo ndidzawononga anthu onse padziko,” watero Yehova.   “Ndidzatambasula dzanja langa nʼkuwononga Yuda,Ndiponso anthu onse okhala mu Yerusalemu.Ndidzawononga chilichonse chokhudza Baala+ pamalowa.Ndidzawononganso ansembe komanso dzina la ansembe a mulungu wachilendo.+   Ndidzawononga anthu amene amakwera padenga nʼkumagwadira magulu a zinthu zakumwamba.*+Komanso amene amagwada ndiponso kulumbira kuti adzakhala okhulupirika kwa Yehova+Koma nʼkumalumbiranso kuti adzakhala okhulupirika kwa Malikamu.+   Ndidzawononga amene asiya kutsatira Yehova,+Komanso amene sanafunefune Yehova kapena kufunsa malangizo kwa iye.”+   Khalani chete pamaso pa Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, chifukwa tsiku la Yehova lili pafupi,+ Yehova wakonza nsembe ndipo wayeretsa anthu amene wawaitana.   “Pa tsiku limene Yehova adzapereke nsembe, ine ndidzaweruza akalonga,Ana a mfumu+ ndi onse ovala zovala zachilendo.   Pa tsiku limenelo ndidzaweruza aliyense amene amakwera pamalo omwe pamakhala mpando wachifumu,Anthu amene adzaza nyumba ya ambuye awo ndi chiwawa ndiponso chinyengo.” 10  Yehova wanena kuti: “Patsiku limenelo,Ku Geti la Nsomba+ kudzamveka phokoso la anthu,Ndipo Kumbali Yatsopano ya mzinda kudzamveka kulira mokweza.+Kumapiri kudzamveka phokoso la chiwonongeko. 11  Lirani mofuula inu anthu okhala ku Makitesi,*Chifukwa amalonda onse awonongedwa.Ndipo onse amene amayeza siliva pasikelo aphedwa.* 12  Pa nthawi imeneyo ndidzafufuza ndi nyale mosamala kwambiri mu Yerusalemu,Ndipo ndidzaweruza anthu amene akukhala mosatekeseka* nʼkumaganiza kuti,‘Yehova sadzachita zabwino kapena zoipa.’+ 13  Chuma chawo chidzatengedwa ndipo nyumba zawo zidzawonongedwa.+ Iwo adzamanga nyumba, koma sadzakhalamo.Iwo adzalima minda ya mpesa koma sadzamwa vinyo wake.+ 14  Tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi.+ Lili pafupi ndipo likubwera mofulumira kwambiri.+ Mkokomo wa tsiku la Yehova ukubwera ndi zowawa.+ Pa tsiku limenelo msilikali adzalira.+ 15  Tsiku limenelo ndi tsiku la mkwiyo,+Tsiku la masautso ndi zowawa,+Tsiku lowononga ndi la mphepo yamkuntho,Tsiku la mdima wochititsa mantha,+Tsiku la mitambo ndi la mdima wandiweyani,+ 16  Tsiku loliza lipenga ndiponso la mfuu yankhondo,+Pochenjeza mizinda ya mipanda yolimba komanso nsanja zazitali zamʼmakona.+ 17  Ndidzasautsa anthu,Ndipo adzayenda ngati anthu osaona,+Chifukwa iwo achimwira Yehova.+ Magazi awo adzakhuthulidwa pansi ngati fumbi,Ndipo matumbo awo adzakhuthulidwa pansi ngati ndowe.+ 18  Siliva kapena golide wawo sadzawapulumutsa pa tsiku la mkwiyo wa Yehova.+Popeza moto wa mkwiyo wake udzawotcheratu dziko lonse lapansi,+Chifukwa iye adzawononga anthu onse apadziko lapansi.”+

Mawu a M'munsi

Kutanthauza “Yehova Wasunga (Kusungidwa).”
Ayenera kuti akunena zinthu zokhudza kulambira mafano.
Nʼkutheka kuti akunena za dzuwa, mwezi ndi nyenyezi.
Mʼchilankhulo choyambirira, “awakhalitsa chete.”
Zikuoneka kuti imeneyi inali mbali ina ya Yerusalemu pafupi ndi Geti la Nsomba.
Mʼchilankhulo choyambirira, “amene adikha pansi ngati nsenga,” mkapu ya vinyo.