Zefaniya 2:1-15

  • Funafunani Yehova tsiku la mkwiyo wake lisanafike (1-3)

    • Yesetsani kukhala olungama ndi ofatsa (3)

    • “Mwina mungadzabisike” (3)

  • Kuweruza mitundu yozungulira (4-15)

2  Sonkhanani pamodzi, ndithu sonkhanani pamodzi,+Inu anthu a mtundu wopanda manyazi.+   Lamulo lisanayambe kugwira ntchito,Tsiku lisanadutse ngati mankhusu,*Yehova asanakusonyezeni mkwiyo wake woyaka moto,+Tsiku la mkwiyo wa Yehova lisanakufikireni,   Funafunani Yehova,+ inu nonse ofatsa* apadziko lapansi,Amene mumatsatira malamulo ake olungama.* Yesetsani kukhala olungama, yesetsani kukhala ofatsa.* Mwina mungadzabisike pa tsiku la mkwiyo wa Yehova.+   Gaza adzakhala mzinda wosiyidwa,Ndipo Asikeloni adzakhala bwinja.+ Anthu a ku Asidodi adzathamangitsidwa dzuwa likuswa mtengo,*Ndipo Ekironi adzazulidwa.+   “Tsoka kwa anthu okhala mʼmbali mwa nyanja, mtundu wa Akereti.+ Yehova wakudzudzulani. Iwe Kanani, dziko la Afilisiti, ndidzakuwononga,Moti mʼdziko lako simudzatsala munthu aliyense.   Malo amʼmbali mwa nyanja adzakhala odyetserako ziweto,Mudzakhala zitsime za abusa ndiponso makola a nkhosa amiyala.   Chigawo chimenecho chidzakhala cha anthu otsala a mʼnyumba ya Yuda.+Ndipo iwo adzadya kumeneko. Madzulo iwo adzagona mʼnyumba za ku Asikeloni. Chifukwa Yehova Mulungu wawo adzawakumbukira.*Ndipo adzasonkhanitsa ndi kubwezeretsa anthu omwe anapita ku ukapolo.”+   “Ndamva kunyoza kwa Mowabu+ ndi mawu achipongwe a Aamoni,+Amene ankanenera anthu anga nʼkumadzitama kuti alanda dziko lawo.”+   Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Pali ine Mulungu wamoyo,Mowabu adzakhala ngati Sodomu,+Ndipo Amoni adzakhala ngati Gomora,+Malo okhala ndi zomera zoyabwa, dothi lamchere ndiponso malo abwinja mpaka kalekale.+ Anthu anga amene adzatsale adzatenga zinthu za anthu amenewa,Ndipo anthu amtundu wanga amene adzatsale, adzawalanda anthuwa zinthu zawo. 10  Anthu amenewo adzaona zimenezi chifukwa cha kunyada kwawo,+Chifukwa ankanyoza anthu a Yehova wa magulu ankhondo akumwamba ndipo ankadzikweza pamaso pawo. 11  Yehova adzawachititsa mantha,Chifukwa adzawononga milungu yonse yapadziko lapansi.Ndipo zilumba zonse za anthu a mitundu ina zidzamugwadira,*+Chilichonse pamalo ake. 12  Inunso Aitiyopiya mudzaphedwa ndi lupanga langa.+ 13  Iye adzaloza dzanja lake kumpoto ndipo adzawononga Asuri.Adzachititsa Nineve kukhala bwinja,+ kukhala dziko louma ngati chipululu. 14  Magulu a nyama kapena kuti nyama zakutchire za mitundu yonse zidzagona mumzindawo. Nungu ndiponso mbalame ya vuwo zidzagona usiku wonse pamitu ya zipilala zamzindawo. Pawindo padzamveka nyimbo. Pamakomo a nyumba padzakhala zibulumwa za nyumba zakugwa,Chifukwa iye adzachititsa kuti matabwa oyalidwa kukhoma akhale pamtunda. 15  Mzinda uwu unali wodzikuza ndipo unkakhala mosatekeseka.Mumtima mwake unkanena kuti, ‘Ndine ndekha ndipo palibe wondiposa.’ Koma tsopano wakhala chinthu chodabwitsa,Malo amene nyama zakutchire zimagonamo. Aliyense wodutsa pafupi ndi mzindawu adzaimba mluzu ndipo adzapukusa mutu.”+

Mawu a M'munsi

“Mankhusu” ndi makoko amene amachotsa ku mbewu ngati mpunga popuntha, ndipo amatha kuwauluza ndi mphepo.
Kapena kuti, “odzichepetsa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “chiweruzo chake.”
Kapena kuti, “odzichepetsa.”
Kapena kuti, “lili paliwombo.”
Kapena kuti, “adzawasamalira.”
Kapena kuti, “zidzamulambira.”