Zefaniya 3:1-20
3 Tsoka kwa mzinda wogalukira, woipitsidwa komanso wopondereza anthu ake.+
2 Mzindawo sunamvere+ ndipo sunalole kulangizidwa,+
Sunakhulupirire Yehova+ komanso sunayandikire Mulungu wake.+
3 Akalonga ake ali ngati mikango yobangula.+
Oweruza ake ali ngati mimbulu imene ikuyenda usiku.Imene pofika mʼmawa imadya chilichonse osasiya ngakhale fupa.
4 Aneneri ake ndi amwano ndiponso achinyengo.+
Ansembe ake amaipitsa zinthu zopatulika,+Ndipo amaphwanya malamulo.+
5 Yehova ndi wolungama mumzindawo+ ndipo salakwitsa.
Mʼmawa uliwonse iye amadziwitsa anthu chilungamo chake,+Moti mofanana ndi kuwala, chilungamocho sichisowa.
Koma wosalungama sachita manyazi.+
6 “Ine ndinawononga mitundu ya anthu ndi kusakaza nsanja zawo zamʼmakona.
Ndinawononga misewu yawo moti simunkayendanso anthu.
Mizinda yawo inakhala mabwinja ndipo simunatsale munthu aliyense.+
7 Ndiyeno ndinati, ‘Mosakayikira udzandiopa ndipo udzalola kulangizidwa,’+
Kuti iye* asawonongedwe.+Ndidzamuimba mlandu wa zonsezi.*
Koma mʼpamene ankafunitsitsa kwambiri kuchita zoipa.+
8 Yehova wanena kuti: ‘Choncho pitirizani kundiyembekezera,*+Mpaka tsiku limene ndidzanyamuke kuti ndikatenge zinthu za anthu omwe ndawagonjetsa.*Chiweruzo changa ndi choti ndisonkhanitse mitundu ya anthu, ndisonkhanitse maufumu,Kuti ndiwasonyeze mkwiyo wanga, ndithu mkwiyo wanga wonse woyaka moto,+Chifukwa moto wa mkwiyo wanga udzawotcheratu dziko lonse lapansi.+
9 Pa nthawiyo ndidzasintha chilankhulo cha anthu kuti chikhale chilankhulo choyera,Kuti onse aziitanira pa dzina la Yehova,Nʼkumamutumikira mogwirizana.’*+
10 Kuchokera kuchigawo cha mitsinje ya ku Itiyopiya,Anthu amene akundichonderera, anthu anga obalalitsidwa, adzandibweretsera mphatso.+
11 Pa tsiku limenelo, sudzachita manyaziChifukwa cha zinthu zonse zimene unachita pondigalukira,+Popeza ndidzachotsa anthu odzikweza pakati panu.Ndipo sudzakhalanso wodzikweza mʼphiri langa lopatulika.+
12 Ndidzasiya anthu odzichepetsa ndi ofatsa kuti akhalebe pakati panu,+Ndipo iwo adzapeza chitetezo mʼdzina la Yehova.
13 Aisiraeli otsala+ sadzachita zinthu zosalungama.+Sadzalankhula bodza kapena kukhala ndi lilime lachinyengo.Iwo adzadya ndi kugona ndipo sipadzakhala wowaopseza.”+
14 Fuula mosangalala, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni!*
Fuula chifukwa chopambana, iwe Isiraeli!+
Sangalala ndiponso kondwera ndi mtima wonse, iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu!*+
15 Yehova wakuchotsera ziweruzo zake.+
Wabweza mdani wako.+
Yehova, Mfumu ya Isiraeli, ali pakati panu.+
Ndipo sudzaopanso kuti tsoka likugwera.+
16 Tsiku limenelo Yerusalemu adzauzidwa kuti:
“Usaope iwe Ziyoni,+
Ndipo manja ako asafooke.
17 Yehova Mulungu wako ali pakati panu+
Ndipo adzakupulumutsa chifukwa ndi wamphamvu.
Iye adzakondwera nawe.+
Adzakhala phee chifukwa chokhutira ndi chikondi chimene akukusonyeza,
Ndipo adzafuula mosangalala chifukwa chokondwera nawe.
18 Ndidzasonkhanitsa anthu amene akumva chisoni chifukwa chosapezeka pazikondwerero zako.+Iwo sanali ndi iwe chifukwa anali ku ukapolo kumene ankanyozedwa.+
19 Pa nthawiyo ndidzalanga onse amene akukupondereza,+Ndipo ndidzapulumutsa wotsimphina.+Ndidzasonkhanitsa anthu amene anabalalitsidwa.+
Ndidzachititsa kuti akhale otchuka* komanso azitamandidwa,Mʼdziko lonse limene anachititsidwa manyazi.
20 Pa nthawiyo ndidzakubweretsani,Ndidzachita zimenezi pa nthawi imene ndidzakusonkhanitseni.
Ndikadzabwezeretsa iwe ukuona, anthu a mtundu wako amene anatengedwa kupita ku ukapolo,+Ndidzachititsa kuti ukhale wotchuka* komanso uzitamandidwa,+ pakati pa anthu a mitundu yonse yapadziko lapansi,” watero Yehova.
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “Ndidzamulanga chifukwa cha zonsezi.”
^ Kutanthauza Yerusalemu.
^ Kapena kuti, “kundidikirira moleza mtima.”
^ Mabaibulo ena amati, “ndidzanyamuke ngati mboni.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “phewa ndi phewa.”
^ Mawu akuti “mwana wamkazi wa Ziyoni” ndi mawu andakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.
^ Mawu akuti “mwana wamkazi wa Yerusalemu” ndi mawu andakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi dzina.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi dzina.”