Zekariya 1:1-21

  • Kuuza anthu kuti abwerere kwa Yehova (1-6)

    • ‘Bwererani kwa ine ndipo ine ndidzabwerera kwa inu’ (3)

  • Masomphenya Oyamba: Okwera pamahatchi ataima pamitengo ya mchisu (7-17)

    • “Yehova adzalimbikitsanso Ziyoni” (17)

  • Masomphenya Achiwiri: Nyanga 4 ndi amisiri 4 (18-21)

1  Mʼmwezi wa 8, mʼchaka chachiwiri cha ulamuliro wa Dariyo,+ Yehova analankhula ndi mneneri Zekariya*+ mwana wa Berekiya, mwana wa Ido, kuti:  “Yehova anakwiyira kwambiri makolo anu.+  Uwauze kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: “Bwererani kwa ine,” watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, “ndipo ine ndidzabwerera kwa inu,”+ akutero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.’”  “‘Musakhale ngati makolo anu amene aneneri akale anawauza kuti: “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Chonde, siyani njira zanu zoipa ndiponso zochita zanu zoipa.’”’+ ‘Koma iwo sanamvere ndipo sanatsatire mawu anga,’+ watero Yehova.  ‘Kodi makolo anuwo ali kuti pano? Ndipo “kodi aneneriwo anakhalabe ndi moyo mpaka kalekale?”  Ndinauza makolo anu malamulo oti azitsatira ndipo ndinatumiza atumiki anga aneneri kuti akawachenjeze zimene zidzawachitikire ngati sangatsatire malamulowo. Kodi zonse zimene ndinanena kuti zidzawachitikirazo sizinawachitikire?’+ Choncho iwo anabwerera kwa ine nʼkunena kuti: ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba watichitira zimene anakonza mogwirizana ndi njira zathu ndi zochita zathu.’”+  Pa tsiku la 24 la mwezi wa 11 womwe ndi mwezi wa Sebati,* mʼchaka chachiwiri cha ulamuliro wa Dariyo,+ Yehova analankhula ndi mneneri Zekariya mwana wa Berekiya, mwana wa Ido. Anamuuza kuti anene kuti:  “Ndinaona masomphenya usiku. Ndinaona munthu atakwera pahatchi* yomwe inaima pakati pa mitengo ya mchisu imene inali mʼchigwa. Kumbuyo kwake kunali mahatchi ofiira kwambiri, ofiirira ndi oyera.”*  Choncho ndinafunsa kuti: “Kodi amenewa ndi ndani mbuyanga?” Mngelo amene ankalankhula nane anandiyankha kuti: “Ndikuuza kuti amenewa ndi ndani.” 10  Kenako munthu amene anaima pakati pa mitengo ya mchisu uja anati: “Amenewa atumizidwa ndi Yehova kuti ayendeyende padziko lapansi.” 11  Ndiyeno iwo anauza mngelo wa Yehova amene anaima pakati pa mitengo ya mchisu uja kuti: “Ife tayendayenda padziko lonse lapansi ndipo taona kuti pali bata komanso palibe chosokoneza.”+ 12  Choncho mngelo wa Yehova anati: “Inu Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, kodi Yerusalemu ndiponso mizinda ya Yuda+ imene munaikwiyira kwa zaka 70 zimenezi,+ simuichitira chifundo mpaka liti?” 13  Yehova anayankha mngelo amene ankalankhula nane uja mokoma mtima komanso ndi mawu olimbikitsa. 14  Ndiyeno mngelo amene ankalankhula nane uja anandiuza kuti: “Fuula kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: “Ndatsimikiza mtima kuti nditeteze Yerusalemu ndi Ziyoni.+ 15  Ndakwiyira kwambiri anthu a mitundu ina amene akukhala mosatekeseka.+ Ndawakwiyira chifukwa chakuti ine ndinangokwiyira anthu anga pangʼono,+ koma anthu amenewa anakulitsa kwambiri mavuto a anthu angawo.”’+ 16  Choncho Yehova wanena kuti, ‘“Ndidzabwerera ku Yerusalemu nʼkuchitira chifundo mzinda umenewu+ ndipo nyumba yanga idzamangidwa mumzindawu.+ Chingwe choyezera chidzatambasulidwa pa Yerusalemu,”+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.’ 17  Fuulanso kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: “Mizinda yanga idzasefukiranso ndi zinthu zabwino. Yehova adzalimbikitsanso Ziyoni+ ndipo adzasankhanso Yerusalemu.”’”+ 18  Kenako nditakweza maso, ndinaona nyanga 4.+ 19  Choncho ndinafunsa mngelo amene ankalankhula nane uja kuti: “Kodi nyangazi zikuimira chiyani?” Iye anandiyankha kuti: “Izi ndi nyanga zimene zinabalalitsa Yuda,+ Isiraeli+ ndi Yerusalemu.”+ 20  Kenako Yehova anandionetsa amisiri 4. 21  Ndiyeno ndinafunsa kuti: “Kodi awa abwera kudzatani?” Mngeloyo anayankha kuti: “Zimenezi ndi nyanga zimene zinabalalitsa Yuda moti panalibe amene anatha kudzutsa mutu wake. Amisiriwa adzabwera kudzaopseza nyangazi ndipo adzawononga nyanga za mitundu ina ya anthu amene anakweza nyanga* zawo poukira dziko la Yuda kuti abalalitse anthu ake.”

Mawu a M'munsi

Kutanthauza “Yehova Wakumbukira.”
Ena amati “hosi.”
Nʼkuthekanso kuti panali hatchi yofiira kwambiri, yofiirira ndi yoyera.
Kapena kuti, “mphamvu.”