Zekariya 10:1-12

  • Pemphani mvula kwa Yehova osati kwa milungu yabodza (1, 2)

  • Yehova akugwirizanitsa anthu ake (3-12)

    • Mtsogoleri wochokera mʼbanja la Yuda (3, 4)

10  “Pemphani Yehova kuti akugwetsereni mvula pa nthawi ya mvula yomalizira. Yehova ndi amene amapanga mitambo yamvula,Ndiponso amene amagwetsera anthu mvula.+Iye amakulitsa mbewu mʼmunda mwa munthu aliyense.  2  Aterafi* amalankhula zabodza,Ndipo olosera zamʼtsogolo amaona masomphenya onama. Amafotokoza maloto opanda pake,Ndipo saphula kanthu polimbikitsa anthu. Nʼchifukwa chake adzasochere ngati nkhosa. Iwo adzavutika chifukwa adzakhala opanda mʼbusa.  3  Ine ndakwiyira kwambiri abusa,Ndipo atsogoleri awo opondereza* ndiwaimba mlandu.Chifukwa ine Yehova wa magulu ankhondo akumwamba ndacheukira gulu langa la nkhosa+ lomwe ndi nyumba ya YudaNdipo ndalisandutsa hatchi yanga yaulemerero, yokwera popita kunkhondo.  4  Mʼnyumba ya Yuda mudzatuluka mtsogoleri.Mudzatulukanso wolamulira wothandiza,Komanso mudzatuluka uta womenyera nkhondo.Woyangʼanira* aliyense adzatuluka mwa iye. Onse adzatulukira limodzi.  5  Onsewa adzakhala ngati asilikali.Adzapondaponda matope a mʼmisewu ya kunkhondo. Iwo adzamenya nkhondo chifukwa Yehova ali nawo.+Adani awo oyenda pamahatchi adzachitsidwa manyazi.+  6  Ndidzachititsa nyumba ya Yuda kukhala yapamwamba,Ndipo nyumba ya Yosefe ndidzaipulumutsa.+ Ndidzawabwezera pamalo awo amene ankakhala,Chifukwa ndidzawachitira chifundo.+Iwo adzakhala ngati sanakanidwepo chiyambire.+Popeza ine ndine Yehova Mulungu wawo, ndidzawayankha.  7  A nyumba ya Efuraimu adzakhala ngati msilikali wamphamvu,Ndipo mumtima mwawo adzasangalala ngati amwa vinyo.+ Ana awo aamuna adzaona zimenezi ndipo adzakondwera.Mitima yawo idzakondwera chifukwa cha Yehova.+  8  ‘Ndidzawaitana ndi likhweru nʼkuwasonkhanitsa pamodzi.Popeza ndidzawawombola,+ iwo adzachuluka.Ndipo adzapitiriza kuchuluka.  9  Ngakhale kuti ndidzawamwaza ngati mbewu pakati pa anthu a mitundu ina,Iwo adzandikumbukira ali kumadera akutali.Iwowo ndi ana awo adzapezanso mphamvu ndipo adzabwerera. 10  Ndidzawabweretsa kuchokera kudziko la Iguputo.Ndidzawasonkhanitsa pamodzi kuchokera kudziko la Asuri.+Ndidzawabweretsa kudera la Giliyadi+ ndi la LebanoniNdipo malo okwanira anthu onsewo sadzapezeka.+ 11  Ndidzadutsa panyanja, nyanjayo nditaigwetsera tsoka.Ndidzamenya mafunde a nyanjayo,+Ndipo madzi onse a mtsinje wa Nailo adzauma. Kunyada kwa Asuri kudzathetsedwa,Ndipo ndodo yachifumu ya Iguputo idzachoka.+ 12  Ine Yehova ndidzawachititsa kukhala amphamvu,+Ndipo zochita zawo zidzalemekeza dzina langa,’+ watero Yehova.”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Milungu ya banja; Mafano.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “okhala ngati atonde a mbuzi.”
Kapena kuti, “Kapitawo.”