Zekariya 11:1-17
11 “Iwe Lebanoni, tsegula zitseko zako,Kuti moto uwotcheretu mitengo yako ya mkungudza.
2 Lira mofuula, iwe mtengo wa junipa,* chifukwa mtengo wa mkungudza wagwa.Mitengo ikuluikulu yawonongedwa.
Lirani mofuula, inu mitengo ya thundu* ya ku Basana,Chifukwa nkhalango yowirira kwambiri ija yawonongedwa.
3 Tamverani! Abusa akulira mofuula,Chifukwa ulemerero wawo watha.
Tamverani! Mikango yamphamvu ikubangula,Chifukwa nkhalango zowirira za mʼmbali mwa mtsinje wa Yorodano zawonongedwa.
4 Yehova Mulungu wanga wanena kuti, ‘Weta nkhosa zimene zinayenera kuphedwa.+
5 Amene anazigula amazipha,+ koma saimbidwa mlandu. Amene akuzigulitsa+ akunena kuti: “Yehova atamandike chifukwa ndilemera.” Ndipo abusa ake sazichitira chifundo.’+
6 ‘Sindidzachitiranso chifundo anthu okhala mʼdzikoli,’ watero Yehova. ‘Choncho ine ndidzachititsa kuti aliyense aziponderezedwa ndi mnzake ndiponso mfumu yake. Iwo adzawononga dzikoli, ndipo ine sindidzawapulumutsa mʼmanja mwawo.’”
7 Ine ndinayamba kuweta nkhosa zimene zinayenera kuphedwa+ ndipo ndinachita zimenezi chifukwa cha inu, anthu ovutika a mʼgulu la nkhosali. Choncho ndinatenga ndodo ziwiri. Ina ndinaipatsa dzina lakuti Wosangalatsa ndipo inayo ndinaipatsa dzina lakuti Mgwirizano.+ Ndiyeno ndinayamba kuweta gulu la nkhosalo.
8 Ndinachotsa abusa atatu mʼmwezi umodzi chifukwa sindinathenso kuwalezera mtima ndipo iwonso ananyansidwa nane.
9 Ndipo ndinanena kuti: “Sindikuwetaninso. Amene akufa afe ndipo amene akuwonongeka, awonongeke. Otsalawo adyane.”
10 Choncho ndinatenga ndodo yanga yotchedwa Wosangalatsa+ ija nʼkuiduladula. Ndinachita izi kuti ndithetse pangano limene ndinachita ndi anthu a mtundu wanga.
11 Panganolo linaswedwa tsiku limenelo ndipo nkhosa zovutika zimene zinaona ndikuchita zimenezi, zinadziwa kuti zimene ndachitazo nʼzimene Yehova ananena.
12 Kenako ndinawauza kuti: “Ngati mukuona kuti nʼzoyenera, ndipatseni malipiro anga. Koma ngati mukuona kuti nʼzosayenera musandipatse.” Iwo anandilipira* ndalama 30 zasiliva.+
13 Kenako Yehova anandiuza kuti: “Kaziponye mosungiramo chuma. Zimenezi ndi ndalama zochepa zimene aona kuti angandilipire.”+ Choncho ndinatenga ndalama 30 zasilivazo nʼkukaziponya mosungiramo chuma panyumba ya Yehova.+
14 Kenako ndinathyola ndodo yanga yachiwiri ija yotchedwa Mgwirizano,+ pothetsa ubale wa Yuda ndi Isiraeli.+
15 Ndiyeno Yehova anandiuza kuti: “Tenga zida za mʼbusa wopanda pake.+
16 Chifukwa ndilola kuti mʼdzikoli mukhale mʼbusa wina. Mʼbusa ameneyu sadzasamalira nkhosa zimene zikuwonongeka.+ Iye sadzafunafuna nkhosa yaingʼono, sadzachiritsa yovulala+ komanso sadzapatsa chakudya nkhosa zimene zikadali zamphamvu. Mʼmalomwake adzadya nyama ya nkhosa yonenepa+ ndipo adzakupula* ziboda za nkhosazo.+
17 Tsoka kwa mʼbusa wanga wopanda pake+ amene akusiya nkhosa.+
Lupanga lidzamutema padzanja ndi diso lake lakumanja.
Dzanja lake lidzalumala kwambiri,Ndipo diso lake lamanja lidzachita khungu.”*