Zekariya 12:1-14

  • Yehova anateteza Yuda ndi Yerusalemu (1-9)

    • Yerusalemu, “mwala wolemera” (3)

  • Kulirira munthu amene anabayidwa (10-14)

12  Uthenga wokhudza Isiraeli: “Awa ndi mawu a Yehova okhudza Isiraeli.”Yehova, amene anatambasula kumwamba,+Amene anayala maziko a dziko lapansi,+Komanso amene anapanga mzimu* umene uli mwa munthu, wanena kuti: 2  “Yerusalemu ndimusandutsa kapu imene imachititsa anthu a mitundu yonse yomuzungulira kuyenda dzandidzandi. Ndipo mdani adzazungulira Yuda komanso Yerusalemu.+ 3  Pa tsiku limenelo, Yerusalemu ndidzamusandutsa mwala wolemera* kwa anthu a mitundu yonse. Onse onyamula mwala umenewo, adzavulala koopsa.+ Anthu a mitundu yonse yapadziko lapansi adzasonkhana kuti amuukire.+ 4  Pa tsiku limenelo, ndidzachititsa kuti hatchi iliyonse ipanikizike ndipo wokwera pahatchiyo ndidzamuchititsa misala. Maso anga adzakhala panyumba ya Yuda, koma hatchi iliyonse ya anthu a mitundu ina ndidzaichititsa khungu,” watero Yehova. 5  “Mafumu a Yuda adzanena mumtima mwawo kuti, ‘Anthu a ku Yerusalemu akutipatsa mphamvu chifukwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba ndi Mulungu wawo.’+ 6  Pa tsiku limenelo, ndidzachititsa mafumu a Yuda kukhala ngati mbaula zamoto pakati pa mitengo komanso ngati miyuni yamoto pamilu ya tirigu.+ Iwo adzatentha anthu a mitundu yonse yowazungulira, kumanja ndi kumanzere.+ Ndipo anthu a ku Yerusalemu adzakhalanso pamalo awo mumzinda wa Yerusalemu.+ 7  Yehova adzayamba nʼkupulumutsa matenti a Yuda. Adzachita zimenezi kuti kukongola* kwa nyumba ya Davide ndi kukongola* kwa anthu a ku Yerusalemu, kusakhale kwakukulu kwambiri kuposa kwa Yuda. 8  Pa tsiku limenelo, Yehova adzateteza anthu a ku Yerusalemu.+ Munthu amene wapunthwa* pa tsikulo, adzakhala wamphamvu ngati Davide. Nyumba ya Davide idzawatsogolera ngati Mulungu ndiponso ngati mngelo wa Yehova.+ 9  Ndipo pa tsikulo, ndidzatsimikiza kuwononga mitundu yonse ya anthu yobwera kudzaukira Yerusalemu.+ 10  Anthu a mʼnyumba ya Davide ndiponso a ku Yerusalemu ndidzawapatsa mzimu wanga posonyeza kuti ndawakomera mtima ndipo udzawalimbikitsa kundipempha mochonderera. Iwo adzayangʼana kwa munthu amene anamubaya,+ ndipo adzamulirira ngati mmene angachitire polirira mwana yekhayo wamwamuna. Adzamulira kwambiri ngati akulira maliro a mwana wamwamuna woyamba kubadwa. 11  Pa tsiku limenelo, anthu adzalira kwambiri mu Yerusalemu ngati mmene analirira ku Hadadirimoni, mʼchigwa cha Megido.+ 12  Anthu amʼdziko lonselo adzalira mokuwa. Banja lililonse lizidzalira palokha. Banja la nyumba ya Davide lizidzalira palokha ndipo akazi a mʼbanjali azidzalira paokha. Banja la nyumba ya Natani+ lizidzalira palokha, ndipo akazi a mʼbanjali azidzalira paokha. 13  Banja la nyumba ya Levi+ lizidzalira palokha, ndipo akazi a mʼbanjali azidzalira paokha. Anthu a mʼbanja la Simeyi+ azidzalira paokha, ndipo akazi a mʼbanjali azidzalira paokha. 14  Mabanja onse otsala adzalira. Banja lililonse lizidzalira palokha, ndipo akazi a mʼmabanjawo azidzalira paokha.”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “mpweya.”
Kapena kuti, “wotopetsa.”
Kapena kuti, “ulemerero.”
Kapena kuti, “ulemerero.”
Kapena kuti, “wafooka kwambiri.”