Zekariya 14:1-21
14 “Tamverani! Tsiku la Yehova likubwera pamene adani anu adzakulandani zinthu zanu nʼkuzigawana ali mumzinda wanu womwewo.
2 Ndidzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse kuti amenyane ndi Yerusalemu. Mzindawu udzalandidwa, katundu wamʼnyumba adzatengedwa ndipo akazi adzagwiriridwa. Hafu ya anthu amumzindawu idzatengedwa kupita kudziko lina, koma anthu otsalawo sadzachotsedwa mumzindawu.
3 Yehova adzapita kukamenyana ndi anthu a mitundu inawo+ ngati mmene amachitira pa tsiku la nkhondo.+
4 Pa tsiku limenelo mapazi ake adzaponda paphiri la Maolivi+ lomwe lili moyangʼanizana ndi Yerusalemu mbali yakumʼmawa. Phirili lidzagawanika pakati kuyambira kumʼmawa mpaka kumadzulo* ndipo pakati pake padzakhala chigwa chachikulu kwambiri. Hafu ya phirilo idzasunthira kumpoto ndipo hafu inayo idzasunthira kumʼmwera.
5 Inu mudzathawira kuchigwa chimene chidzakhale pakati pa mapiri anga, chifukwa chigwacho chidzafika mpaka ku Azeli. Mudzathawa ngati mmene munathawira chivomerezi chimene chinachitika mʼmasiku a Uziya, mfumu ya Yuda.+ Ndipo Yehova Mulungu wanga adzabwera limodzi ndi oyera onse.+
6 Pa tsiku limenelo, sipadzakhala kuwala kwapadera.+ Zinthu zidzaundana chifukwa cha kuzizira.
7 Lidzakhala tsiku limodzi lotchedwa tsiku la Yehova.+ Sikudzakhala masana kapena usiku, chifukwa ngakhale usiku kudzakhala kukuwalabe.
8 Pa tsikulo madzi amoyo+ adzatuluka mu Yerusalemu.+ Hafu ya madziwo idzapita kunyanja yakumʼmawa*+ ndipo hafu inayo idzapita kunyanja ya kumadzulo.*+ Zimenezi zidzachitika mʼnyengo yotentha ndiponso mʼnyengo yozizira.
9 Yehova adzakhala Mfumu ya dziko lonse lapansi.+ Pa tsiku limenelo, Yehova adzakhala mmodzi+ ndipo dzina lake lidzakhala limodzi.+
10 Dziko lonse lidzakhala ngati chigwa cha Araba,+ kuyambira ku Geba+ kukafika ku Rimoni+ kumʼmwera kwa Yerusalemu. Mzindawu udzakwezedwa pamalo ake ndipo anthu adzakhalamo,+ kuyambira ku Geti la Benjamini+ mpaka ku Geti Loyamba nʼkukafika ku Geti la Pakona. Komanso adzakhala kuyambira ku Nsanja ya Hananeli+ mpaka kukafika kumalo a mfumu oponderamo mphesa.
11 Anthu adzakhala mumzindawo ndipo sudzatembereredwanso kuti uwonongedwe.+ Anthu azidzakhala mu Yerusalemu motetezeka.+
12 Mliri umene Yehova adzagwetsere anthu onse a mitundu ina amene amamenyana ndi Yerusalemu+ ndi uwu: Munthu aliyense mnofu wake udzawola ali chiimire, maso ake adzawola ali mʼmalo mwake ndiponso lilime lake lidzawola mʼkamwa mwake.
13 Pa tsiku limenelo Yehova adzawasokoneza kwambiri. Aliyense adzagwira dzanja la mnzake ndipo aliyense adzamenya mnzake.+
14 Nayenso Yuda adzamenya nawo nkhondo ya ku Yerusalemu ndipo chuma cha anthu a mitundu yonse yowazungulira chidzasonkhanitsidwa. Adzasonkhanitsa golide, siliva ndi zovala zambirimbiri.+
15 Mliri wofanana ndi umenewu udzagweranso mahatchi, nyulu,* ngamila, abulu komanso ziweto zonse zimene zidzapezeke mʼmisasa ya adaniwo.
16 Aliyense wotsala mwa anthu a mitundu yonse obwera kudzamenyana ndi Yerusalemu, chaka chilichonse+ azidzapita kukagwadira* Mfumu, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba,+ ndiponso kukachita nawo Zikondwerero za Misasa.+
17 Koma mvula sidzagwa mʼdziko la munthu aliyense wochokera mʼmabanja apadziko lapansi, amene sadzapita ku Yerusalemu kukagwadira Mfumu, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.+
18 Ngati anthu a ku Iguputo sadzabwera mumzindawu, mʼdziko lawonso simudzagwa mvula. Mʼmalomwake, Yehova adzawagwetsera mliri umene amagwetsera anthu a mitundu ina amene sabwera kudzachita Zikondwerero za Misasa.
19 Chimenechi chidzakhala chilango cha tchimo la Iguputo komanso mitundu yonse imene sibwera kudzachita nawo Zikondwerero za Misasa.
20 Pa tsiku limenelo, pamabelu a mahatchi padzalembedwa mawu akuti ‘Chiyero nʼcha Yehova!’+ Ndipo miphika yakukamwa kwakukulu+ yamʼnyumba ya Yehova idzakhala ngati mbale zolowa+ zapaguwa lansembe.
21 Mphika uliwonse wakukamwa kwakukulu mu Yerusalemu ndi mu Yuda udzakhala woyera ndipo udzakhala wa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. Anthu onse amene azidzapereka nsembe azidzatenga ina mwa miphikayo nʼkuphikiramo. Pa tsiku limenelo, mʼnyumba ya Yehova wa magulu ankhondo akumwamba simudzapezeka munthu wa ku Kanani.”*+