Zekariya 2:1-13

  • Masomphenya Achitatu: Munthu atanyamula chingwe choyezera (1-13)

    • Kuyeza Yerusalemu (2)

    • Yehova, “mpanda wamoto” (5)

    • Kukhudza mwana wa diso la Mulungu (8)

    • Mitundu yambiri ya anthu idzakhala kumbali ya Yehova (11)

2  Kenako ndinakweza maso ndipo ndinaona munthu atanyamula chingwe choyezera.+ 2  Ndiyeno ndinamʼfunsa kuti: “Ukupita kuti?” Iye anandiyankha kuti: “Ndikupita kukayeza Yerusalemu kuti ndidziwe kutalika kwa mulitali ndi mulifupi mwake.”+ 3  Kenako mngelo amene ankalankhula ndi ine uja ananyamuka nʼkumapita ndipo kunabwera mngelo wina kudzakumana naye. 4  Mngeloyo anauza mnzakeyo kuti: “Thamanga ukauze mnyamata uyo kuti, ‘“Mu Yerusalemu anthu azidzakhalamo+ ngati mzinda wopanda mpanda chifukwa cha anthu onse ndiponso ziweto zimene zili mmenemo.+ 5  Ine ndidzakhala ngati mpanda wake wamoto+ ndipo ulemerero wanga udzadzaza mumzindawu,”’+ watero Yehova.” 6  “Bwerani! Bwerani! Thawani mʼdziko lakumpoto,”+ watero Yehova. “Chifukwa ndinakubalalitsirani kumbali zonse za dziko lapansi,”+ watero Yehova. 7  “Bwera Ziyoni! Thawa iwe amene ukukhala ndi mwana wamkazi wa Babulo.*+ 8  Atapatsidwa ulemerero, Mulungu wandituma kwa anthu a mitundu ina amene ankakulandani zinthu zanu,+ chifukwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Amene akukukhudzani, akukhudza mwana wa diso langa.+ 9  Ine ndidzawaloza mowaopseza, ndipo adzatengedwa ndi akapolo awo kuti akhale chuma cha akapolowo.’+ Mudzadziwa ndithu kuti Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wandituma. 10  Fuula chifukwa cha chisangalalo, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni,*+ popeza ine ndikubwera+ ndipo ndidzakhala pakati pako,”+ watero Yehova. 11  “Pa tsiku limenelo mitundu yambiri ya anthu idzakhala kumbali ya Yehova+ ndipo adzakhala anthu anga. Ine ndidzakhala pakati pako.” Ndipo udzadziwa kuti Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wandituma kwa iwe. 12  Yehova adzatenga Yuda kukhala gawo lake mʼdziko loyera, ndipo adzasankhanso Yerusalemu.+ 13  Anthu nonsenu, khalani chete pamaso pa Yehova, chifukwa iye wanyamuka pamalo ake oyera okhala ndipo akufuna kuchitapo kanthu.

Mawu a M'munsi

Mawu akuti “mwana wamkazi wa Babulo” ndi mawu andakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Babulo kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.
Mawu akuti “mwana wamkazi wa Ziyoni” ndi mawu andakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.