Zekariya 3:1-10
3 Ndiyeno Mulungu anandionetsa Yoswa+ mkulu wa ansembe, ataimirira pamaso pa mngelo wa Yehova. Satana+ anali ataima kudzanja lamanja la Yoswa kuti azimutsutsa.
2 Kenako mngelo wa Yehovayo anauza Satana kuti: “Iwe Satana, Yehova akudzudzule!+ Yehova amene wasankha Yerusalemu+ akudzudzule. Kodi munthu uyu sali ngati chikuni chimene chapulumutsidwa pamoto kuti chisapse?”
3 Pa nthawiyi, Yoswa anali ataima pamaso pa mngelo, atavala zovala zonyansa.
4 Mngeloyo anauza anthu amene anaima patsogolo pake kuti: “Muvuleni zovala zonyansazo.” Kenako anauza Yoswa kuti: “Waona, ndakuchotsera zolakwa zako ndipo uvekedwa zovala zabwino kwambiri.”*+
5 Choncho ndinanena kuti: “Auzeni kuti amuveke nduwira yoyera kumutu kwake.”+ Ndipo anamuvekadi nduwira yoyera kumutu kwake komanso zovala zina. Apa nʼkuti mngelo wa Yehova ataima chapafupi.
6 Mngelo wa Yehova uja anauza Yoswa kuti:
7 “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Ukayenda mʼnjira zanga ndi kutsatira malamulo anga, udzakhala woweruza wa anthu a mʼnyumba yanga+ ndipo uzidzasamalira* mabwalo a nyumba yanga. Komanso ndidzakulola kumafika pamaso panga ngati mmene amachitira aima apawa.’
8 ‘Tamvetsera iwe Yoswa mkulu wa ansembe ndi anzako amene akhala pansi kutsogolo kwako, chifukwa amuna amenewa ali ngati chizindikiro. Ine ndibweretsa mtumiki wanga+ dzina lake Mphukira.+
9 Taonani mwala umene ndauika pamaso pa Yoswa. Mwala umenewu uli ndi maso 7 ndipo pamwalawu ndilembapo zinthu mochita kugoba. Ndidzachotsa zolakwa za dzikoli tsiku limodzi,’+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.
10 ‘Pa tsiku limenelo aliyense adzaitana mnzake kuti abwere pansi pa mtengo wake wa mpesa ndiponso wa mkuyu,’+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.”