Zekariya 4:1-14

  • Masomphenya a 5: Choikapo nyale ndi mitengo iwiri ya maolivi (1-14)

    • ‘Sipakufunika mphamvu, koma mzimu wanga’ (6)

    • Asakunyozeni chifukwa munayamba ndi zinthu zochepa (10)

4  Mngelo amene ankalankhula ndi ine uja anabwerera nʼkundidzutsa ngati akudzutsa munthu amene akugona.  Kenako anandifunsa kuti: “Ukuona chiyani?” Ndinayankha kuti: “Ndikuona choikapo nyale chagolide yekhayekha.+ Pamwamba pake pali mbale yolowa. Choikapo nyalecho chili ndi nyale 7,+ inde nyale 7, ndipo nyale zimene zili pachoikapo nyalecho, zilinso ndi mapaipi 7.  Pafupi ndi choikapo nyalecho pali mitengo iwiri ya maolivi.+ Umodzi uli kumanja kwa mbale yolowa ija ndipo wina uli kumanzere kwa mbaleyo.”  Kenako ndinafunsa mngelo amene ankalankhula nane uja kuti: “Kodi zimenezi zikuimira chiyani mbuyanga?”  Mngeloyo anafunsa kuti: “Kodi sukudziwa tanthauzo la zinthu zimenezi?” Ndinayankha kuti: “Sindikudziwa mbuyanga.”  Choncho iye anandiuza kuti: “Yehova wauza Zerubabele kuti, ‘“Kuti zinthu zonsezi zichitike, sipakufunika gulu lankhondo kapena mphamvu,+ koma mzimu wanga,”+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.  Ngakhale Zerubabele+ atakumana ndi chopinga chachikulu ngati phiri, chidzasalazidwa nʼkukhala malo afulati.+ Iye adzabweretsa mwala wotsiriza ndipo anthu adzafuula kuti: “Koma mwalawu ndiye ndi wokongola bwanji! Koma ndiye ndi wokongola!”’”  Ndinamvanso mawu a Yehova akuti:  “Manja a Zerubabele anayala maziko a nyumbayi+ ndipo manja ake omwewo adzaimalizitsa.+ Ndipo mudzadziwa kuti Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wandituma kwa inu. 10  Munthu asakunyozeni chifukwa chakuti munayamba kumanga ndi zinthu zochepa.+ Popeza anthu adzasangalala ndipo adzaona chingwe choyezera cha mmisiri womanga, mʼdzanja la Zerubabele. Nyale 7 zimenezi* ndi maso a Yehova amene akuyangʼana uku ndi uku padziko lonse lapansi.”+ 11  Ndiyeno ndinafunsa mngelo uja kuti: “Kodi mitengo iwiri ya maolivi, imene wina uli kumanja ndipo wina kumanzere kwa choikapo nyalechi, ikuimira chiyani?”+ 12  Ndinamufunsanso kuti: “Kodi nthambi* ziwiri za mitengo ya maolivi, zimene zikuthira mafuta agolide mʼmbale yolowa kudzera mʼmapaipi awiri agolide, zikuimira chiyani?” 13  Iye anandifunsa kuti: “Kodi sukudziwa tanthauzo la zinthu zimenezi?” Ndinayankha kuti: “Ayi mbuyanga.” 14  Ndiyeno iye anandiuza kuti: “Amenewa ndi odzozedwa awiri amene amaima kumbali iyi ndi mbali inayi ya Ambuye wa dziko lonse lapansi.”+

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “Maso 7 amenewa.”
Kapena kuti, “nthambi zolemedwa ndi zipatso.”