Zekariya 5:1-11

  • Masomphenya a 6: Mpukutu ukuuluka (1-4)

  • Masomphenya a 7: Chiwiya chokwana muyezo wa efa (5-11)

    • Munali mzimayi dzina lake Kuipa (8)

    • Chiwiya anachitenga nʼkupita nacho ku Sinara (9-11)

5  Nditayangʼananso kumwamba, ndinaona mpukutu ukuuluka. 2  Mngeloyo anandifunsa kuti: “Ukuona chiyani?” Ndinayankha kuti: “Ndikuona mpukutu ukuuluka. Mpukutuwo ndi wautali mikono* 20 mulitali ndiponso mikono 10 mulifupi.” 3  Ndiyeno anandiuza kuti: “Ili ndi temberero limene likubwera padziko lonse lapansi, chifukwa aliyense amene akuba,+ mogwirizana ndi zimene zalembedwa kumbali imodzi ya mpukutuwo, sakulandira chilango. Komanso aliyense amene akulumbira mwachinyengo,+ mogwirizana ndi zimene zalembedwa kumbali ina ya mpukutuwo, sakulandira chilango. 4  Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Ine ndatumiza mpukutuwo kuti ukalowe mʼnyumba ya munthu wakuba ndi mʼnyumba ya munthu wolumbira mwachinyengo mʼdzina langa. Mpukutuwo udzakhalabe mʼnyumba mwake nʼkuwonongeratu nyumbayo, matabwa ake ndi miyala yake.’” 5  Kenako mngelo amene ankalankhula nane uja anandiyandikira nʼkundiuza kuti: “Taona chimene chikubwera uko.” 6  Choncho ndinafunsa kuti: “Nʼchiyani chimenechi?” Iye anandiyankha kuti: “Chimenechi ndi chiwiya chokwana muyezo wa efa.”* Ndiyeno anapitiriza kuti: “Anthu oipa amaoneka chonchi padziko lonse lapansi.” 7  Kenako ndinaona akuvundukula chivundikiro chamtovu cha chiwiyacho, ndipo mkati mwake munali mzimayi atakhala pansi. 8  Mngelo uja anandiuza kuti: “Mayi ameneyu dzina lake ndi Kuipa.” Kenako anamukankha nʼkumubwezera mʼchiwiya chokwana muyezo wa efacho ndipo anachivundikira ndi chivundikiro chamtovu chija. 9  Ndiyeno nditayangʼana kumwamba ndinaona azimayi awiri akubwera. Azimayiwo ankauluka mphepo ikuwomba ndipo mapiko awo anali ooneka ngati a dokowe. Iwo ananyamula chiwiya chija nʼkupita nacho mʼmwamba.* 10  Choncho ndinafunsa mngelo amene ankalankhula nane uja kuti: “Kodi chiwiyacho akupita nacho kuti?” 11  Iye anandiyankha kuti: “Akupita nacho kudziko la Sinara*+ kuti akamangire mzimayiyo nyumba kumeneko. Akakamumangira nyumbayo, akamukhazika kumeneko pamalo ake oyenera.”

Mawu a M'munsi

Mkono umodzi ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu. Onani Zakumapeto B14.
Chiwiya chimenechi chinali basiketi yomwe ankagwiritsa ntchito poyeza muyezo wa efa. Muyezo wa efa ndi ofanana ndi malita 22. Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “pakati pa dziko lapansi ndi kumwamba.”
Kumeneku ndi ku Babeloniya.