Zekariya 6:1-15

  • Masomphenya a 8: Magaleta 4 (1-8)

  • Mphukira idzakhala mfumu ndi wansembe (9-15)

6  Kenako nditayangʼananso kumwamba ndinaona magaleta 4 akubwera kuchokera pakati pa mapiri awiri. Mapiriwo anali akopa.* 2  Galeta loyamba linkakokedwa ndi mahatchi ofiira ndipo galeta lachiwiri linkakokedwa ndi mahatchi akuda.+ 3  Galeta lachitatu linkakokedwa ndi mahatchi oyera ndipo galeta la 4 linkakokedwa ndi mahatchi amawangamawanga ndiponso amadonthomadontho.+ 4  Ndiyeno ndinafunsa mngelo amene ankalankhula nane uja kuti: “Kodi magaleta amenewa akuimira chiyani mbuyanga?” 5  Mngeloyo anandiyankha kuti: “Magaletawa akuimira zolengedwa zauzimu 4+ zakumwamba zomwe zinakaima pamaso pa Ambuye wa dziko lonse lapansi+ ndipo zikubwera. 6  Galeta limene likukokedwa ndi mahatchi akuda likupita kudziko lakumpoto.+ Mahatchi oyera akupita kutsidya la nyanja. Mahatchi amawangamawanga akupita kudziko lakumʼmwera. 7  Mahatchi amadonthomadontho anali okonzeka kupita nʼkumakayendayenda padziko lapansi.” Kenako iye anauza mahatchiwo kuti: “Pitani mukayendeyende padziko lapansi.” Ndipo mahatchiwo anapita nʼkumakayendayenda padziko lapansi. 8  Mngelo uja anandiitana nʼkundiuza kuti: “Taona, mkwiyo umene Yehova anali nawo padziko lakumpoto watha chifukwa cha mahatchi amene apita kumeneko.” 9  Yehova analankhula nanenso kuti: 10  “Ukatenge kwa Heledai, Tobiya ndi Yedaya zinthu zimene abweretsa kuchokera kwa anthu amene anatengedwa kupita ku ukapolo. Pa tsiku limenelo udzapite kunyumba ya Yosiya mwana wa Zefaniya pamodzi ndi anthu amene achokera ku Babulowo. 11  Ukatenge siliva ndi golide nʼkupangira chisoti chachifumu.* Chisoticho udzaveke Yoswa+ mkulu wa ansembe, mwana wa Yehozadaki. 12  Ndiyeno udzamuuze kuti,‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: “Munthu uyu dzina lake ndi Mphukira.+ Adzaphuka pamalo ake ndipo adzamanga kachisi wa Yehova.+ 13  Munthu ameneyu ndi amene adzamange kachisi wa Yehova ndipo adzalandira ulemerero. Iye adzakhala pampando wake wachifumu nʼkumalamulira. Adzakhalanso wansembe ali pampando womwewo+ ndipo maudindo awiri onsewo adzakhala ogwirizana. 14  Chisoti chachifumucho* chizidzakhala mʼkachisi wa Yehova kuti anthu azidzakumbukira Helemu, Tobiya, Yedaya+ ndi Heni mwana wa Zefaniya. 15  Anthu amene ali kutali adzabwera kudzamanga nawo kachisi wa Yehova.” Anthu inu mukadzamvera mawu a Yehova Mulungu wanu, mudzadziwa kuti Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wandituma kwa inu.’”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “amkuwa.”
Kapena kuti, “chisoti chachifumu cholemekezeka.”
Kapena kuti, “chisoti chachifumu cholemekezekacho.”