Zekariya 7:1-14

  • Yehova anadzudzula anthu osala kudya mwachinyengo (1-14)

    • “Kodi munkasaladi kudya chifukwa cha ine?” (5)

    • ‘Muzisonyeza chilungamo, chikondi chokhulupirika ndi chifundo’ (9)

7  Mʼchaka cha 4 cha ulamuliro wa Mfumu Dariyo, Yehova analankhula ndi Zekariya+ pa tsiku la 4 la mwezi wa 9, womwe ndi mwezi wa Kisilevi.*  Anthu a ku Beteli anatumiza Sarezere komanso Regemu-meleki ndi anthu ake, kuti akapemphe Yehova kuti awakomere mtima.*  Anawatuma kuti akauze ansembe apanyumba* ya Yehova wa magulu ankhondo akumwamba ndi aneneri kuti: “Kodi tilire* mʼmwezi wa 5+ ndiponso kusala kudya ngati mmene tachitira zaka zonsezi?”  Yehova wa magulu ankhondo akumwamba analankhula nanenso kuti:  “Kauze anthu onse amʼdzikoli ndi ansembe kuti, ‘Pamene munkasala kudya ndi kulira mʼmwezi wa 5 komanso mʼmwezi wa 7+ kwa zaka 70,+ kodi munkasaladi kudya chifukwa cha ine?  Ndipo pamene munkadya komanso kumwa, kodi simunkachita zimenezi kuti mudzisangalatse nokha?  Kodi simunayenera kumvera mawu amene Yehova ananena kudzera mwa aneneri akale,+ pamene ku Yerusalemu ndi mizinda yozungulira kunkakhala anthu komanso kunali mtendere? Kodi simunayenera kumvera Mulungu pamene ku Negebu ndi ku Sefela kunkakhala anthu?’”  Yehova analankhulanso ndi Zekariya kuti:  “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Muziweruza mwachilungamo chenicheni+ komanso muzisonyezana chikondi chokhulupirika+ ndi chifundo. 10  Musamabere mwachinyengo mkazi wamasiye, mwana wamasiye,*+ mlendo+ kapena munthu wosauka.+ Musamakonzerane chiwembu mumtima mwanu.’+ 11  Koma iwo anakanabe kumvetsera.+ Anapitiriza kumulozetsa nkhongo+ ndipo anatseka makutu awo kuti asamve.+ 12  Iwo anaumitsa mtima wawo ngati mwala wa dayamondi*+ ndipo sanamvere malamulo* ndi mawu a Yehova wa magulu ankhondo akumwamba amene anawatumizira pogwiritsa ntchito mzimu wake kudzera mwa aneneri akale.+ Choncho Yehova wa magulu ankhondo akumwamba anakwiya kwambiri.”+ 13  “‘Ine ndikawaitana sankandimvera,+ choncho iwonso akandiitana sindinkawamvera,’+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. 14  ‘Ndipo ndinawabalalitsira ku mitundu yonse ya anthu imene sankaidziwa+ ngati atengedwa ndi mphepo yamkuntho. Dzikoli analisiya ndipo linakhala bwinja, popanda munthu wodutsamo kapena kubwereramo.+ Chifukwa anasandutsa dziko losiririka kukhala chinthu chochititsa mantha.’”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “akakhazike pansi mtima wa Yehova.”
Kapena kuti, “apakachisi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndilire.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”
Mabaibulo ena amati, “mwala wolimba kwambiri.”
Kapena kuti, “malangizo.”