Zekariya 8:1-23

  • Yehova anapatsa Ziyoni mtendere ndi choonadi (1-23)

    • Yerusalemu, “mzinda wa choonadi” (3)

    • “Muziuzana zoona” (16)

    • Kusiya kusala kudya nʼkuyamba kuchita chikondwerero (18, 19)

    • ‘Tifunefune Yehova’ (21)

    • Amuna 10 adzagwira mkanjo wa Myuda (23)

8  Yehova wa magulu ankhondo akumwamba analankhula nanenso kuti:  “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: ‘Ndatsimikiza mtima kuti ndidzateteza Ziyoni.+ Ndatsimikiza kuti ndidzamuteteza nditakwiya kwambiri.’”  “Yehova wanena kuti, ‘Ndidzabwerera ku Ziyoni+ ndipo ndizidzakhala ku Yerusalemu.+ Yerusalemu adzatchedwa mzinda wa choonadi*+ ndipo phiri la Yehova wa magulu ankhondo akumwamba lidzatchedwa phiri loyera.’”+  “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Amuna ndi akazi achikulire adzakhalanso mʼmabwalo a mzinda wa Yerusalemu, aliyense atanyamula ndodo mʼmanja mwake chifukwa cha ukalamba.*+  Mʼmabwalo a mzindawo mudzadzaza anyamata ndi atsikana ndipo azidzasewera mmenemo.’”+  “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Ngakhale kuti pa nthawiyo anthu omwe adzatsale adzaona kuti zimenezo nʼzosatheka, kodi zidzakhalanso zosatheka kwa ine?’ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.”  “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Ine ndipulumutsa anthu anga kuchokera kudziko lakumʼmawa ndiponso lakumadzulo.+  Ndidzawabweretsa, ndipo azidzakhala mu Yerusalemu.+ Iwo adzakhala anthu anga ndipo ine ndidzakhala Mulungu wawo+ woona* ndi wachilungamo.’”  “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Limbani mtima ndipo mukonzeke kugwira ntchito,+ inu amene mukumva mawu a aneneri+ masiku ano. Awa ndi mawu amene ananenedwanso tsiku limene maziko a nyumba ya Yehova wa magulu ankhondo akumwamba anayalidwa kuti kachisi amangidwe. 10  Nthawi imeneyi isanafike, palibe malipiro omwe ankaperekedwa polipira munthu kapena chiweto.+ Zinali zoopsa kuyenda ulendo chifukwa cha adani, popeza ine ndinkachititsa kuti anthu onse aziukirana.’ 11  ‘Koma tsopano anthu anga otsala sindidzawachitiranso zinthu ngati mmene ndinachitira masiku akale,’+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. 12  ‘Mʼdzikolo mudzadzalidwa mbewu ya mtendere. Mpesa udzabala zipatso ndipo dziko lapansi lidzatulutsa zokolola zake.+ Kumwamba kudzagwetsa mame ndipo ndidzachititsa kuti anthu otsala alandire zinthu zonsezi.+ 13  Popeza munali temberero pakati pa anthu a mitundu ina,+ inu a mʼnyumba ya Yuda ndi a mʼnyumba ya Isiraeli ndidzakupulumutsani ndipo mudzakhala dalitso.+ Limbani mtima,+ musachite mantha.’+ 14  Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘“Monga zinalili kuti ndinatsimikiza mtima kukugwetserani tsoka chifukwa choti makolo anu anandikwiyitsa ndipo sindinakumvereni chisoni,”+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, 15  “panopa ndatsimikizanso mtima kuchitira zabwino Yerusalemu ndi nyumba ya Yuda.+ Choncho musachite mantha.”’+ 16  ‘Muzichita zinthu izi: Muziuzana zoona.+ Poweruza milandu mʼmageti a mizinda yanu, muziweruza mogwirizana ndi choonadi komanso molimbikitsa mtendere.+ 17  Musamakonzerane chiwembu mumtima mwanu+ ndipo musamakonde kulumbira monama.+ Chifukwa zinthu zonsezi ndimadana nazo,’+ watero Yehova.” 18  Yehova wa magulu ankhondo akumwamba analankhula nanenso kuti: 19  “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Kusala kudya kwa mʼmwezi wa 4,+ kusala kudya kwa mʼmwezi wa 5,+ kusala kudya kwa mʼmwezi wa 7+ ndiponso kusala kudya kwa mʼmwezi wa 10,+ idzakhala nthawi yachikondwerero komanso yosangalala kwa anthu a mʼnyumba ya Yuda.+ Choncho muzikonda choonadi ndiponso mtendere.’ 20  Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Ndithu anthu a mitundu ina ndi anthu amʼmizinda yambiri adzabwera. 21  Ndipo anthu amumzinda wina adzapita kwa anthu amumzinda wina nʼkuwauza kuti: “Tiyeni tipite tikapemphe Yehova kuti atikomere mtima* komanso tikafunefune Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. Inenso ndipita nawo.”+ 22  Anthu ambiri a mitundu ina ndiponso mitundu yamphamvu idzabwera kudzafunafuna Yehova wa magulu ankhondo akumwamba mu Yerusalemu,+ ndiponso kudzapempha Yehova kuti awakomere mtima.’* 23  Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Mʼmasiku amenewo, amuna 10 ochokera mʼzilankhulo zonse za anthu a mitundu ina+ adzagwira mkanjo* wa Myuda nʼkunena kuti: “Anthu inu tikufuna tipite nanu limodzi,+ chifukwa tamva kuti Mulungu ali ndi inu.”’”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “wokhulupirika.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “chifukwa cha kuchuluka kwa masiku.”
Kapena kuti, “wokhulupirika.”
Kapena kuti, “timukhazike mtima pansi.”
Kapena kuti, “timukhazike mtima pansi.”
Kapena kuti, “mʼmunsi mwa chovala.”